\id NUM - Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 \ide UTF-8 \h NUMERI \toc1 Numeri \toc2 Numeri \toc3 Num \mt1 Numeri \c 1 \s1 Kalembera \p \v 1 Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti, \v 2 “Werengani Aisraeli onse mʼmafuko awo ndi mʼmabanja awo, lemba dzina la munthu wamwamuna aliyense, mmodzimmodzi. \v 3 Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali. \v 4 Munthu mmodzi wochokera ku fuko lililonse yemwe ndi mtsogoleri wa banja lake, ndiye akuthandizeni pa ntchitoyi. \v 5 Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa: \b \li1 Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni, \li1 \v 6 Selumieli mwana wa Zurisadai, kuchokera ku fuko la Simeoni, \li1 \v 7 Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda, \li1 \v 8 Netanieli mwana wa Zuwara, kuchokera ku fuko la Isakara, \li1 \v 9 Eliabu mwana wa Heloni, kuchokera ku fuko la Zebuloni, \li1 \v 10 Mwa ana a Yosefe: \li2 kuchokera ku fuko la Efereimu, Elisama mwana wa Amihudi; \li2 kuchokera ku fuko la Manase, Gamalieli mwana wa Pedazuri; \li1 \v 11 Abidani mwana wa Gideoni, kuchokera ku fuko la Benjamini, \li1 \v 12 Ahiyezeri mwana wa Amisadai, kuchokera ku fuko la Dani, \li1 \v 13 Pagieli mwana wa Okirani, kuchokera ku fuko la Aseri, \li1 \v 14 Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi, \li1 \v 15 Ahira mwana wa Enani, kuchokera ku fuko la Nafutali.” \b \p \v 16 Amenewa ndi anthu amene anasankhidwa kuchokera mʼmagulu mwawo, eni mbumba a mafuko a makolo awo. Iwowa anali atsogoleri a mafuko a Israeli. \p \v 17 Mose ndi Aaroni anatenga anthu amene mayina awo anaperekedwa, \v 18 ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi \v 19 monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai: \b \li1 \v 20 Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 21 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500. \b \li1 \v 22 Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 23 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300. \b \li1 \v 24 Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 25 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650. \b \li1 \v 26 Kuchokera mwa zidzukulu za Yuda: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 27 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600. \b \li1 \v 28 Kuchokera mwa zidzukulu za Isakara: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 29 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400. \b \li1 \v 30 Kuchokera mwa zidzukulu za Zebuloni: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 31 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400. \b \li4 \v 32 Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe: \li1 Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 33 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500. \b \li1 \v 34 Kuchokera mwa zidzukulu za Manase: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 35 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Manase chinali 32,200. \b \li1 \v 36 Kuchokera mwa zidzukulu za Benjamini: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 37 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400. \b \li1 \v 38 Kuchokera mwa zidzukulu za Dani: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 39 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700. \b \li1 \v 40 Kuchokera mwa zidzukulu za Aseri: \li2 Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 41 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500. \b \li1 \v 42 Kuchokera mwa zidzukulu za Nafutali: \li2 Aamuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. \v 43 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400. \b \p \v 44 Amenewa ndiwo anthu amene Mose ndi Aaroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri khumi ndi awiri a Israeli, aliyense kuyimira fuko lake. \v 45 Aisraeli onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli anawawerenga monga mwa mabanja awo. \v 46 Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550. \p \v 47 Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena. \v 48 Pakuti Yehova anawuza Mose kuti, \v 49 “Usawerenge fuko la Levi kapena kuliphatikiza mʼkawundula wa Aisraeli. \v 50 Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo. \v 51 Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa. \v 52 Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake. \v 53 Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.” \p \v 54 Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose. \c 2 \s1 Malo a Misasa ya Mafuko Onse a Aisraeli \p \v 1 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: \v 2 “Aisraeli azimanga misasa yawo mozungulira tenti ya msonkhano motalikira pangʼono. Munthu aliyense amange pamene pali mbendera ya fuko lake.” \b \pi1 \v 3 Kummawa, kotulukira dzuwa, magulu a msasa wa Yuda amange pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Ayudawo ndi Naasoni mwana wa Aminadabu. \v 4 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600. \pi1 \v 5 Fuko la Isakara lidzamanga pafupi ndi Yuda. Mtsogoleri wa gulu la Isakara ndi Netanieli mwana wa Zuwara. \v 6 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 54,400. \pi1 \v 7 Lotsatira lidzakhala fuko la Zebuloni. Mtsogoleri wa gulu la Zebuloni ndi Eliabu mwana wa Heloni. \v 8 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 57,400. \pi1 \v 9 Anthu onse aamuna mʼmisasa ya Yuda, chiwerengero chawo ndi 186,400 monga mwa magulu awo. Iwowo ndiwo aziyamba kusamuka. \b \pi1 \v 10 Kummwera kudzakhala magulu a msasa wa Rubeni pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu la Rubeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri. \v 11 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 46,500. \pi1 \v 12 Fuko la Simeoni lidzamanga pafupi ndi Rubeni. Mtsogoleri wa gulu la Simeoni ndi Selumieli mwana wa Zurisadai. \v 13 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 59,300. \pi1 \v 14 Lotsatira lidzakhala fuko la Gadi. Mtsogoleri wa gulu la Gadi ndi Eliyasafu mwana wa Deuweli. \v 15 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 45,650. \pi1 \v 16 Anthu onse aamuna mu msasa wa Rubeni, chiwerengero chawo monga mwa magulu awo, ndi 151,450. Iwowo azikhala achiwiri posamuka. \b \pi1 \v 17 Tsono tenti ya msonkhano ndi msasa wa Alevi zidzakhala pakati pa misasayo. Iwo adzasamuka monga momwe anamangira misasa yawo, aliyense pa malo ake pamene pali mbendera yake. \b \pi1 \v 18 Kumadzulo kudzakhala magulu a msasa wa Efereimu pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Aefereimuwo ndi Elisama mwana wa Amihudi. \v 19 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 40,500. \pi1 \v 20 Fuko la Manase lidzakhala pafupi ndi Efereimu. Mtsogoleri wa Amanase ndi Gamalieli mwana wa Pedazuri. \v 21 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 32,200. \pi1 \v 22 Lotsatira lidzakhala fuko la Benjamini. Mtsogoleri wa Abenjamini ndi Abidani mwana wa Gideoni. \v 23 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 35,400. \pi1 \v 24 Anthu onse aamuna mu msasa wa Efereimu, chiwerengero chawo ndi 108,100 monga mwa magulu awo. Iwowo azikhala achitatu posamuka. \b \pi1 \v 25 Kumpoto kudzakhala msasa wa magulu a Dani pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Adani ndi Ahiyezeri mwana wa Amisadai. \v 26 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 62,700. \pi1 \v 27 Fuko la Aseri lidzamanga pafupi ndi iwowo. Mtsogoleri wa Aaseri ndi Pagieli mwana wa Okirani. \v 28 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 41,500. \pi1 \v 29 Lotsatira lidzakhala fuko la Nafutali. Mtsogoleri wa Anafutali ndi Ahira mwana wa Enani. \v 30 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 53,400. \pi1 \v 31 Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo. \b \pi1 \v 32 Amenewa ndi Aisraeli monga mwa mabanja a makolo awo. Chiwerengero cha Aisraeli onse mʼmisasa chinali 603,550, mwa magulu awo. \v 33 Koma Alevi sanawawerenge pamodzi ndi Aisraeli enawo monga momwe Yehova analamulira Mose. \b \p \v 34 Choncho Aisraeli anachita zonse zomwe Yehova analamulira Mose. Umo ndi momwe amamangira misasa yawo pamene panali mbendera zawo, ndipo ankasamuka monga mwa mafuko a makolo awo. \c 3 \s1 Alevi \p \v 1 Iyi ndi mbiri ya banja la Aaroni ndi Mose pa nthawi yomwe Yehova anayankhula ndi Mose pa phiri la Sinai. \b \p \v 2 Mayina a ana aamuna a Aaroni anali Nadabu, woyamba kubadwa, Abihu, Eliezara ndi Itamara. \v 3 Amenewa ndi mayina a ana aamuna a Aaroni, ansembe odzozedwa omwe anapatulidwa kuti azitumikira ngati ansembe. \v 4 Koma Nadabu ndi Abihu, anagwa nafa pamaso pa Yehova pamene ankapereka nsembe ndi moto wachilendo pamaso pa Yehova mʼchipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana aamuna. Choncho Eliezara ndi Itamara ndiwo amene ankatumikira ngati ansembe nthawi imene Aaroni abambo awo anali moyo. \p \v 5 Yehova anati kwa Mose, \v 6 “Bweretsa fuko la Levi ndipo ulipereke kwa Aaroni wansembe kuti lizimutumikira. \v 7 Azigwira ntchito yothandiza iyeyo ndi gulu lonse ku tenti ya msonkhano pogwira ntchito ya ku Chihema. \v 8 Azisamalira zipangizo zonse za mu tenti ya msonkhano, ndipo azigwirira ntchito Aisraeli potumikira mu tenti. \v 9 Pereka Alevi kwa Aaroni ndi kwa ana ake aamuna. Amenewa ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwa iye kwathunthu. \v 10 Usankhe Aaroni ndi ana ake aamuna kuti azitumikira pa ntchito ya unsembe. Koma wina aliyense woyandikira malo opatulika aphedwe.” \p \v 11 Yehova anawuzanso Mose kuti, \v 12 “Pakati pa Aisraeli onse ndatenga Alevi kulowa mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kwa amayi a Chiisraeli. Alevi ndi anga, \v 13 pakuti ana onse oyamba kubadwa ndi anga. Nditakantha ana onse oyamba kubadwa mu Igupto, ndinadzipatulira ndekha mwana aliyense woyamba kubadwa mu Israeli, wa munthu ndi nyama. Azikhala anga. Ine ndine Yehova.” \p \v 14 Yehova anawuza Mose mʼchipululu cha Sinai kuti, \v 15 “Werenga Alevi monga mwa mabanja awo ndi mafuko awo. Werenga mwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi kapena kupitirirapo.” \v 16 Choncho Mose anawawerenga potsatira zomwe Yehova anamulamulira. \li1 \v 17 Mayina a ana aamuna a Levi ndi awa: \li2 Geresoni, Kohati ndi Merari. \li1 \v 18 Mayina a ana a Geresoni potsata mabanja awo ndi awa: \li2 Libini ndi Simei. \li1 \v 19 Ana a Kohati potsata mabanja awo ndi awa: \li2 Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. \li1 \v 20 Ana a Merari potsata mabanja awo ndi awa: \li2 Mali ndi Musi. \p Amenewa ndiwo anali mabanja a Alevi monga mwa makolo awo. \b \p \v 21 Kwa Geresoni kunali banja la Alibini, banja la Asimei. Amenewa ndiwo anali mabanja a Ageresoni. \v 22 Chiwerengero cha amuna onse amene anawawerenga a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 7,500. \v 23 Mabanja a Ageresoni azimanga misasa yawo kumadzulo, kumbuyo kwa Chihema. \v 24 Mtsogoleri wa mabanja a Ageresoni anali Eliyasafu mwana wa Laeli. \v 25 Ntchito imene Ageresoni anapatsidwa ku tenti ya msonkhano inali yosamalira Chihema ndi tenti, pamodzi ndi zophimbira zake, katani ya pa khomo la ku tenti ya msonkhano, \v 26 ndi makatani wotchinga bwalo, katani ya pa chipata cholowera ku bwalo lozungulira Chihema ndi guwa lansembe, zingwe ndi zonse zokhudzana ndi ntchito yawo. \b \p \v 27 Kwa Kohati kunali mabanja a Amramu, Aizihara, Ahebroni ndi Auzieli. Awa ndiye anali mabanja a Akohati. \v 28 Chiwerengero cha amuna onse a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 8,600. Akohati ankagwira ntchito yosamalira malo wopatulika. \v 29 Mabanja a ana a Kohati ankamanga misasa yawo kummwera kwa Chihema. \v 30 Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Kohati anali Elizafani mwana wa Uzieli. \v 31 Iwo ankagwira ntchito yosamalira Bokosi la Chipangano, tebulo, choyikapo nyale, maguwa, zipangizo za kumalo wopatulika zimene ansembe ankagwiritsa ntchito, katani, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito. \v 32 Mtsogoleri wamkulu wa Alevi anali Eliezara mwana wa Aaroni wansembe. Iye anasankhidwa kukhala woyangʼanira omwe ankasamalira malo wopatulika. \b \p \v 33 Kwa Merari kunali banja la Mali ndi banja la Musi. Amenewa ndiye anali mabanja a Amerari. \v 34 Chiwerengero cha amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 6,200. \v 35 Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Amerari anali Zuriyeli mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga misasa yawo kumpoto kwa Chihema. \v 36 Amerari anapatsidwa ntchito yosamalira mitengo ya chihema, nsichi zake, mizati yake, matsinde ake, ndi zida zake zonse, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito, \v 37 pamodzi ndi mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema ndi zingwe zake. \b \p \v 38 Mose ndi Aaroni ndi ana ake aamuna ankamanga misasa yawo kummawa kwa chihema, kuyangʼana kotulukira dzuwa, kutsogolo kwa tenti ya msonkhano. Anali ndi ntchito yosamalira malo wopatulika mʼmalo mwa Aisraeli. Aliyense woyandikira malo wopatulika ankayenera kuphedwa. \b \p \v 39 Alevi onse amene Mose ndi Aaroni anawawerenga potsatira lamulo la Yehova monga mwa magulu a mabanja awo, amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo anali 22,000. \b \p \v 40 Yehova anawuza Mose kuti, “Werenga ana onse aamuna oyamba kubadwa mu Israeli, omwe ali ndi mwezi umodzi kapena kupitirirapo ndipo ulembe mndandanda wa mayina awo. \v 41 Unditengere Alevi onse mʼmalo mwa ana oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso ziweto zazimuna za Alevi mʼmalo mwa ziweto zonse zazimuna zoyamba kubadwa za Aisraeli. Ine ndine Yehova.” \p \v 42 Choncho Mose anawerenga ana aamuna onse oyamba kubadwa a Aisraeli monga momwe Yehova anamulamulira. \v 43 Chiwerengero chonse cha ana aamuna oyamba kubadwa kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 22, 273. \p \v 44 Ndipo Yehova anawuzanso Mose kuti, \v 45 “Tenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso zoweta zonse za Alevi mʼmalo mwa zoweta za Aisraeli. Alevi ndi anga. Ine ndine Yehova. \v 46 Pofuna kuwombola ana aamuna 273 oyamba kubadwa a Aisraeli amene anaposa chiwerengero cha aamuna a fuko la Levi, \v 47 utenge masekeli asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale ofanana ndi masekeli a ku malo wopatulika, kumene sekeli imodzi imakwanira magera makumi awiri. \v 48 Ndalama zimenezi uzipereke kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kuti ukhale mtengo woombolera Aisraeli woonjezerawo.” \p \v 49 Choncho Mose anatenga ndalama zowombolera zija kuchokera kwa Aisraeli amene chiwerengero chawo chinaposa chiwerengero cha omwe anawomboledwa ndi Alevi. \v 50 Anatenga masekeli a siliva okwana 1,365 molingana ndi masekeli a ku malo opatulika, kuchokera kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisraeli. \v 51 Mose anapereka ndalama zowombolera zija kwa Aaroni ndi ana ake aamuna monga mwa mawu amene Yehova analamulira. \c 4 \s1 Akohati \p \v 1 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: \v 2 “Werengani Akohati omwe ndi gawo limodzi la Alevi monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo. \v 3 Werengani amuna onse amene ali ndi zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu amene amabwera kudzagwira ntchito mu tenti ya msonkhano. \p \v 4 “Ntchito ya Akohati mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kusamalira zinthu zopatulika kwambiri. \v 5 Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni. \v 6 Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake. \p \v 7 “Pa tebulo pamene pamakhala buledi wa ansembe aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo, ndipo aziyikapo mbale, mabeseni, zipande ndi mitsuko yoperekera nsembe yachakumwa. Aziyikaponso buledi wokhala pamenepo nthawi zonse. \v 8 Tsono pamwamba pa izi aziyalapo nsalu yofiira, ndi kuzikuta mʼzikopa za akatumbu ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake. \p \v 9 “Azitenga nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira choyikapo nyale, pamodzi ndi nyale zake, zopanira zake, zotengera zake ndi mitsuko yonse yosungiramo mafuta. \v 10 Kenaka achikulunge pamodzi ndi zipangizo zake zonse mʼzikopa za akatumbu ndi kuchiyika pa chonyamulira chake. \p \v 11 “Pamwamba pa guwa la golide aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira ndi zikopa za akatumbu ndi kuyika mʼmalo mwake mitengo yonyamulira. \p \v 12 “Azitenga zipangizo zonse zogwiritsira ntchito ku malo wopatulika, azizikulunga mʼnsalu ya mtundu wa thambo, azizikuta ndi zikopa za akatumbu ndi kuziyika pa zonyamulira zake. \p \v 13 “Azichotsa phulusa la pa guwa lansembe lamkuwa ndi kuyalapo nsalu yapepo pamwamba pake. \v 14 Kenaka aziyikapo zipangizo zonse zogwiritsira ntchito potumikira pa guwa, kuphatikizapo miphika yowotchera nyama, mafoloko otengera nyama, zowolera phulusa ndi mbale zowazira magazi pa guwa lansembe ndipo pamwamba pake aziyalapo zikopa za akatumbu ndi kuziyika mʼzonyamulira zake. \p \v 15 “Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano. \p \v 16 “Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe, aziyangʼanira mafuta a nyale, ndi lubani wa nsembe zofukiza, nsembe yaufa yoperekedwa nthawi zonse ndi mafuta odzozera. Aziyangʼaniranso chihema ndi zonse zili mʼmenemo, kuphatikizapo zida ndi ziwiya zonse zopatulika.” \p \v 17 Yehova anawuzanso Mose ndi Aaroni kuti, \v 18 “Onetsetsani kuti mabanja a fuko la Kohati asachotsedwe kwa Alevi. \v 19 Koma muziwachitira izi kuti asafe, akhalebe ndi moyo pamene ayandikira zinthu za ku malo wopatulika kwambiri: Aaroni ndi ana ake aamuna azipita ku malo wopatulika ndi kumamupatsa munthu aliyense ntchito yake ndi zimene ayenera kunyamula. \v 20 Koma Akohati asalowe kukaona zinthu zopatulika, ngakhale kanthawi pangʼono, chifukwa akatero adzafa.” \s1 Ageresoni \p \v 21 Yehova anawuza Mose kuti, \v 22 “Werenganso Ageresoni monga mwa mabanja ndi mafuko awo. \v 23 Uwerenge amuna onse a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu zakubadwa amene amabwera kudzatumikira ku tenti ya msonkhano. \p \v 24 “Ntchito ya mafuko a Ageresoni pamene akugwira ntchito ndi kunyamula katundu ndi iyi: \v 25 Azinyamula makatani a ku chihema, tenti ya msonkhano, zokutira zake ndi zokutira kunja za zikopa za akatumbu, makatani a pa khomo la ku tenti ya msonkhano, \v 26 makatani wotchingira bwalo lozungulira chihema ndi guwa, katani ya pa khomo, zingwe ndi zida zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito mʼchihema. Ageresoni azichita zonse zofunika kuchitika ndi zinthu zimenezi. \v 27 Ntchito yawo yonse, kaya kunyamula kapena kugwira ntchito zina, achite Ageresoni motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Uwagawire ntchito zonse zimene akuyenera kugwira. \v 28 Iyi ndiye ntchito ya fuko la Ageresoni ku tenti ya msonkhano. Ntchito zawo zichitike motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni. \s1 Amerari \p \v 29 “Werenga Amerari monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo. \v 30 Werenga amuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu zakubadwa amene akatumikire mu tenti ya msonkhano. \v 31 Ntchito yawo pamene azikatumikira mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kunyamula matabwa a chihema, mitanda, mizati ndi matsinde, \v 32 ndiponso mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema, zingwe ndi zipangizo zake zonse ndiponso zonse zokhudzana ndi ntchito yake. Uwuze munthu aliyense chomwe ayenera kuchita. \v 33 Iyi ndiyo ntchito ya mafuko a Amerari pamene akugwira ntchito ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni.” \s1 Chiwerengero cha Fuko la Levi \p \v 34 Mose, Aaroni ndi atsogoleri a magulu a anthu anawerenga Akohati monga mwa mafuko ndi mabanja awo. \v 35 Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano, \v 36 atawawerenga mwa mafuko awo, anali 2,750. \v 37 Ichi chinali chiwerengero cha mafuko a Akohati onse omwe ankatumikira mu tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova. \p \v 38 Ageresoni anawerengedwanso monga mwa mafuko ndi mabanja awo. \v 39 Amuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano, \v 40 atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 2,630. \v 41 Ichi chinali chiwerengero cha Ageresoni mwa mabanja awo amene ankatumikira ku tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova. \p \v 42 Amerari anawawerenga monga mwa mafuko ndi mabanja awo. \v 43 Amuna onse kuyambira zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzatumikira ntchito mu tenti ya msonkhano, \v 44 atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 3,200. \v 45 Ichi ndicho chinali chiwerengero cha mabanja a Amerari. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga momwe Yehova anawalamulira kudzera mwa Mose. \p \v 46 Kotero Mose, Aaroni ndi atsogoleri a Israeli anawerenga Alevi onse monga mwa mafuko ndi mabanja awo. \v 47 Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu omwe anabwera kudzagwira ntchito yonyamula zinthu ku tenti ya msonkhano \v 48 analipo 8,580. \v 49 Aliyense anamupatsa ntchito ndi kumuwuza choti anyamule monga mwa lamulo la Yehova kudzera mwa Mose. \p Anawawerenga chomwechi potsata zimene Yehova analamula Mose. \c 5 \s1 Ukhondo wa pa Msasa \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Lamula Aisraeli kuti achotse mu msasa aliyense amene ali ndi matenda opatsirana a pa khungu kapena matenda otuluka madzi mʼthupi a mtundu uliwonse, kapena aliyense wodetsedwa chifukwa cha munthu wakufa. \v 3 Muchotse amuna komanso amayi ndipo muwatulutsire kunja kwa msasa kuti asadetse msasa wawo kumene Ine ndimakhala pakati pawo.” \v 4 Aisraeli anachitadi zimenezi. Anawatulutsira kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose. \s1 Kukonza Zolakwika \p \v 5 Yehova anati kwa Mose, \v 6 “Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene mwamuna kapena mayi walakwira mnzake mwa njira iliyonse, ndiye kuti ndi wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Munthuyo ndi wochimwa ndithu ndipo \v 7 ayenera kuwulula tchimo limene anachitalo. Ayenera kubweza zonse zimene anawononga, ndipo awonjezerepo chimodzi mwa magawo asanu ndi kuzipereka kwa munthu amene anamulakwirayo. \v 8 Ngati wolakwiridwayo alibe mʼbale komwe kungapite zinthu zobwezedwazo, zinthuzo zikhale za Yehova ndipo azipereke kwa wansembe, pamodzi ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopepesera tchimo lake. \v 9 Zopereka zonse zopatulika zomwe Aisraeli abwera nazo kwa wansembe zikhale za wansembeyo. \v 10 Mphatso zilizonse zopatulika ndi za munthuyo, koma zomwe wapereka kwa wansembe ndi za wansembeyo.’ ” \s1 Mkazi Wosakhulupirika \p \v 11 Kenaka Yehova anawuza Mose kuti, \v 12 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mkazi wa munthu wina ayenda njira yosayenera nakhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake, \v 13 nakagonana ndi mwamuna wina koma mwamuna wake wosadziwa, ndipo palibe wina aliyense wadziwa za kudzidetsa kwake (pakuti palibe mboni yomuneneza chifukwa sanagwidwe akuchita), \v 14 mwamuna wake ndi kuyamba kuchita nsanje ndi kukayikira mkazi wakeyo kuti ndi wodetsedwa, komanso ngati amuchitira nsanje ndi kumukayikira ngakhale asanadzidetse, \v 15 apite naye mkaziyo kwa wansembe. Ndipo popita atengenso gawo lakhumi la chopereka chaufa wa barele wokwana kilogalamu imodzi mʼmalo mwa mkaziyo. Asathire mafuta pa nsembeyo kapena lubani, chifukwa ndi nsembe ya chopereka ya chakudya yopereka chifukwa cha nsanje, nsembe yozindikiritsa tchimo.’ ” \p \v 16 “ ‘Wansembe abwere naye mkaziyo ndi kumuyimitsa pamaso pa Yehova. \v 17 Ndipo wansembeyo atenge madzi oyera mʼmbiya ya dothi ndi kuyika mʼmadzimo fumbi lapansi la mʼTenti ya Msonkhano. \v 18 Wansembe atayimika mkaziyo pamaso pa Yehova, amumasule tsitsi lake, ndipo ayike mʼmanja mwake nsembe yozindikiritsa tchimo, nsembe yachakudya ya nsanje, wansembeyo atanyamula madzi owawa omwe amabweretsa temberero.’ \v 19 Kenaka wansembeyo alumbiritse mkaziyo ndi kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sanagonane ndi iwe ndipo sunayende njira yoyipa ndi kukhala wodetsedwa pomwe uli pa ukwati ndi mwamuna wako, madzi owawa awa omwe amabweretsa temberero asakupweteke. \v 20 Koma ngati wayenda njira yoyipa uli pa ukwati ndi mwamuna wako ndi kudzidetsa pogonana ndi mwamuna amene si mwamuna wako,’ \v 21 pamenepo wansembe alumbiritse mkaziyo ndi mawu a matemberero ndi kumuwuza kuti, ‘Yehova achititse anthu ako kukutemberera ndi kukunyoza pamene awononga ntchafu yako ndi kutupitsa mimba yako. \v 22 Madzi awa obweretsa temberero alowe mʼthupi mwako ndi kutupitsa mimba yako ndi kuwononga ntchafu yako.’ ” \p “Pamenepo mkaziyo anene kuti, ‘Ameni, ameni.’ ” \p \v 23 “ ‘Wansembe alembe matemberero amenewa mʼbuku ndi kuwanyika mʼmadzi owawa aja. \v 24 Amwetse mkaziyo madzi owawawo omwe amabweretsa temberero, ndipo madzi amenewo adzalowa mʼmimba mwake ndi kuyambitsa ululu woopsa. \v 25 Wansembe achotse mʼmanja mwa mkaziyo nsembe yachakudya ya nsanje ija, nayiweyula pamaso pa Yehova ndi kuyipereka pa guwa lansembe. \v 26 Tsono wansembeyo atapeko ufa dzanja limodzi kuti ukhale wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa lansembe. Atatha izi, amwetse mkaziyo madzi aja. \v 27 Ndipo ngati mkaziyo anadzidetsadi ndi kukhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake, pamene amwa madzi obweretsa matemberero aja, nalowa mʼmimba mwake, adzamva ululu woopsa. Mimba yake idzatupa ndi ntchafu yake idzawonongeka ndipo adzakhala wotembereredwa pakati pa anthu ake. \v 28 Koma ngati mkaziyo sanadzidetse ndi kuti alibe tchimo, adzakhala wopanda mlandu ndipo adzabereka ana. \p \v 29 “ ‘Limeneli ndiye lamulo la nsanje pamene mkazi wayenda njira yoyipa ndi kudzidetsa ali pa ukwati ndi mwamuna wake, \v 30 kapena pamene maganizo a nsanje abwera kwa mwamuna wake chifukwa chokayikira mkazi wakeyo. Wansembe azitenga mkazi wotere ndi kumuyimiritsa pamaso pa Yehova ndipo agwiritse ntchito lamulo lonseli kwa mkaziyo. \v 31 Mwamunayo adzakhala wopanda tchimo lililonse, koma mkaziyo adzasenza zotsatira za tchimo lake.’ ” \c 6 \s1 Za Mnaziri \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi afuna kuchita lonjezo lapadera, lonjezo lodzipatula yekha kwa Yehova ngati Mnaziri, \v 3 sayenera kumwa vinyo kapena zakumwa zosasa ndipo asamamwe chakumwa chilichonse cha mphesa. Asamamwe madzi a mphesa kapena kudya mphesa zaziwisi kapena zowuma. \v 4 Pa nthawi yonse imene ali Mnaziri, asamadye chilichonse chopangidwa kuchokera ku mphesa ngakhale mbewu zake kapena makungu ake.’ \p \v 5 “ ‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’ \v 6 Pa nthawi yonse imene munthuyo wadzipatula yekha kwa Yehova asayandikire mtembo. \v 7 Ngakhale abambo ake kapena amayi ake kapena mchimwene wake kaya mchemwali wake atamwalira, asadzidetse pokhudza mitembo yawo chifukwa kulumbira kwake kwa kudzipatula yekha kwa Yehova kuli pamutu pake. \v 8 Munthuyo ndi wopatulika masiku onse odzipereka kwake kwa Yehova. \p \v 9 “Ngati munthu wina afa mwadzidzidzi pafupi naye ndi kudetsa tsitsi lake loperekedwalo, amete mutu wake pa tsiku lodziyeretsa, tsiku lachisanu ndi chiwiri. \v 10 Tsono pa tsiku lachisanu ndi chitatu abweretse nkhunda ziwiri kapena mawunda awiri anjiwa kwa wansembe pa khomo lolowera ku tenti ya msonkhano. \v 11 Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi ina nsembe yopsereza yotetezera tchimo chifukwa anachimwa popezeka pafupi ndi mtembo. Ndipo tsiku lomwelo apatulenso tsitsi la pamutu pake. \v 12 Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake. \p \v 13 “Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. \v 14 Pamenepo apereke chopereka chake kwa Yehova: Nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi yopanda chilema kuti ikhale nsembe yopsereza, mwana wankhosa wamkazi mmodzi wopanda chilema kuti ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa imodzi yayikulu yayimuna kuti ikhale nsembe yachiyanjano, \v 15 ndipo abwere pamodzi ndi nsembe yachakudya ndi nsembe yachakumwa ndi dengu la buledi wopanda yisiti, makeke opangidwa ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda ta buledi topakidwa mafuta. \p \v 16 “Wansembe apereke zimenezi pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe ya uchimo ndi nsembe yopsereza. \v 17 Apereke dengu la buledi wopanda yisiti ndiponso nsembe yachiyanjano kwa Yehova ya nkhosa yayimuna, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chopereka cha chakumwa. \p \v 18 “Mnaziriyo amete tsitsi limene analipereka lija pa khomo la tenti ya msonkhano. Atenge tsitsilo ndi kuliyika pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano. \p \v 19 “Mnaziriyo atatha kumeta tsitsi analiperekalo, wansembe ayike mʼmanja mwake mwendo wa mmwamba wankhosa yayimuna umene waphikidwa ndipo atengenso keke ndi kamtanda ka buledi, zonse zopanda yisiti zomwe zili mʼdengu lija. \v 20 Wansembe aziweyule pamaso pa Yehova ngati nsembe yoweyula. Zimenezi ndi zopatulika ndipo ndi za wansembe pamodzi ndi chidale chimene anachiweyula ndi ntchafu yomwe anayipereka ija. Zitatha izi, Mnaziri akhoza kumwa vinyo. \p \v 21 “Ili ndi lamulo la Mnaziri yemwe walonjeza kudzipereka kwa Yehova podzipatula yekha kuphatikiza pa zomwe angathe kukwaniritsa. Ayenera kukwaniritsa lonjezo lomwe wachitalo potsata lamulo la Mnaziri.” \s1 Kupereka Mdalitso \p \v 22 Yehova anawuza Mose kuti, \v 23 “Uza Aaroni ndi ana ake aamuna kuti, ‘Umu ndi mmene muzidalitsira Aisraeli. Muzinena kuti, \q1 \v 24 “ ‘Yehova akudalitse \q2 ndi kukusunga; \q1 \v 25 Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, \q2 nakuchitira chisomo; \q1 \v 26 Yehova akweze nkhope yake pa iwe, \q2 nakupatse mtendere.’ ” \p \v 27 Choncho akadzatchula dzina langa podalitsa Aisraeli, Ine ndidzawadalitsadi. \c 7 \s1 Zopereka Popatula Chihema \p \v 1 Mose atamaliza kuyimika chihema chija, anachidzoza mafuta ndi kuchipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. \v 2 Kenaka atsogoleri a Aisraeli, akuluakulu a mabanja omwe ankayangʼanira mafuko a anthu omwe anawawerenga aja, anachita chopereka. \v 3 Anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova: ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ngʼombe zothena khumi ndi ziwiri. Mtsogoleri mmodzi ngʼombe yothena imodzi ndipo atsogoleri awiri ngolo imodzi. Izi anazipereka ku chihema. \p \v 4 Yehova anawuza Mose kuti, \v 5 “Ulandire zimenezi kwa iwo kuti zigwire ntchito ku tenti ya msonkhano. Uzipereke kwa Alevi, aliyense monga mwa ntchito yake.” \p \v 6 Choncho Mose anatenga ngolo ndi ngʼombe zothenazo nazipereka kwa Alevi. \v 7 Anapereka ngolo ziwiri ndi ngʼombe zothena zinayi kwa Ageresoni monga mwantchito yawo \v 8 ndiponso anapereka ngolo zinayi ndi ngʼombe zothena zisanu ndi zitatu kwa Amerari molingananso ndi ntchito yawo. Onsewa ankawayangʼanira anali Itamara mwana wa Aaroni wansembe. \v 9 Koma Mose sanapereke zimenezi kwa Akohati chifukwa zinthu zawo zopatulika zomwe ankayangʼanira zinali zoti azinyamula pa mapewa awo. \mi \v 10 Guwa la nsembe litadzozedwa, atsogoleri anabweretsa zopereka zawo zopatulira guwa nazipereka paguwapo. \v 11 Pakuti Yehova anawuza Mose kuti, “Tsiku lililonse mtsogoleri mmodzi azibweretsa chopereka chake chopatulira guwa lansembe.” \b \m \v 12 Amene anabweretsa chopereka chake tsiku loyamba anali Naasoni mwana wa Aminadabu wa fuko la Yuda. \mi \v 13 Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, ndi beseni lasiliva limodzi lowazira, lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo wopatulika ndipo zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka chachakudya; \v 14 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; \v 15 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; \v 16 mbuzi yayimuna imodzi, nsembe ya machimo; \v 17 ndi ngʼombe zothena ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Naasoni mwana wa Aminadabu. \b \m \v 18 Pa tsiku lachiwiri, Natanieli mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa Isakara, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 19 Chopereka chomwe anabwera nacho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, molingana ndi muyeso wa ku malo opatulika. Mbale zonse zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka cha chakudya. \v 20 Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110 yodzaza ndi lubani; \v 21 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza: \v 22 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yotetezera machimo; \v 23 ndi ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi, nsembe ya chiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Netanieli mwana wa Zuwara. \b \m \v 24 Pa tsiku lachitatu, Eliabu mwana wa Heloni, mtsogoleri wa Azebuloni, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 25 Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, mbale zonse zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, chopereka cha chakudya; \v 26 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; \v 27 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; \v 28 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; \v 29 ndi ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliabu mwana wa Heloni. \b \m \v 30 Tsiku lachinayi linali la Elizuri mwana wa Sedeuri, mtsogoleri wa fuko la Rubeni, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 31 Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, chopereka chachakudya. \v 32 Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; \v 33 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; \v 34 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; \v 35 ndi ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Elizuri mwana wa Sedeuri. \b \m \v 36 Pa tsiku lachisanu Selumieli mwana wa Zurisadai, mtsogoleri wa fuko la Simeoni, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 37 Chopereka chake chinali mbale yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. Zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; \v 38 mbale yagolide imodzi yolemera 110, yodzaza ndi lubani; \v 39 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wamwamuna wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; \v 40 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; \v 41 ngʼombe ziwiri, nkhosa zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Selumieli mwana wa Zurisadai. \b \m \v 42 Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, Eliyasafu mwana wa Deuweli, mtsogoleri wa fuko la Gadi, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 43 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; \v 44 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; \v 45 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, chopereka cha nsembe yopsereza: \v 46 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; \v 47 ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuweli. \b \m \v 48 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Elisama mwana wa Amihudi, mtsogoleri wa fuko la Efereimu, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 49 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonsezi monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; \v 50 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; \v 51 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; \v 52 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; \v 53 ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Elisama mwana wa Amihudi. \b \m \v 54 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Gamalieli mwana wa Pedazuri, mtsogoleri wa fuko Manase, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 55 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; \v 56 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani, \v 57 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; \v 58 mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; \v 59 ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Gamalieli mwana wa Pedazuri. \b \m \v 60 Pa tsiku lachisanu ndi chinayi Abidani mwana wa Gideoni mtsogoleri wa fuko la Benjamini, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 61 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka ndi beseni limodzi lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka cha zakudya; \v 62 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; \v 63 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; \v 64 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; \v 65 ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Abidani mwana wa Gideoni. \b \m \v 66 Pa tsiku lakhumi Ahiyezeri mwana wa Amisadai, mtsogoleri wa fuko la Dani anabweretsa chopereka chake. \mi \v 67 Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; \v 68 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; \v 69 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; \v 70 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; \v 71 ndi ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Ahiyezeri mwana wa Amisadai. \b \m \v 72 Pa tsiku la khumi ndi chimodzi, Pagieli mwana wa Okirani, mtsogoleri wa fuko la Aseri, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 73 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; \v 74 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; \v 75 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; \v 76 mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo; \v 77 ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Pagieli mwana wa Okirani. \b \m \v 78 Pa tsiku la khumi ndi chimodzi Ahira mwana wa Enani, mtsogoleri wa fuko la Nafutali, anabweretsa chopereka chake. \mi \v 79 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; \v 80 mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; \v 81 mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; \v 82 mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; \v 83 ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Ahira mwana wa Enani. \b \p \v 84 Zopereka za atsogoleri a Israeli zopatulira guwa lansembe pamene linadzozedwa zinali izi: mbale khumi ndi ziwiri zasiliva, mabeseni owazira asiliva khumi ndi awiri ndi mbale zagolide khumi ndi ziwiri. \v 85 Mbale iliyonse yasiliva inkalemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndipo beseni lililonse lowazira linkalemera magalamu 800. Pamodzi, mbale zonse zasiliva zinkalemera makilogalamu 27 monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. \v 86 Mbale khumi ndi ziwiri zagolide zodzaza ndi lubanizo zinkalemera magalamu 110 iliyonse, monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. Pamodzi, mbale zagolide zinkalemera kilogalamu imodzi ndi theka. \v 87 Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yopsereza chinali motere: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, nkhosa zazimuna khumi ndi ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi awiri a chaka chimodzi pamodzi ndi chopereka chachakudya. Mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri zinali za nsembe yopepesera machimo. \v 88 Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yachiyanjano chinali motere: ngʼombe zothena 24, nkhosa zazimuna 60, mbuzi zazimuna 60 ndi ana ankhosa aamuna a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndi zimene zinali zopereka zopatulira guwa lansembe litadzozedwa. \p \v 89 Mose atalowa mu tenti ya msonkhano kukayankhula ndi Yehova, anamva mawu kuchokera pakati pa Akerubi awiri amene anali pamwamba pa chivundikiro cha bokosi la umboni. Ndipo anayankhula naye. \c 8 \s1 Za Nyale \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Yankhula ndi Aaroni kuti pamene uyimika nyale zisanu ndi ziwiri, nyalezo ziziyaka kutsogolo kwa choyikapo nyale.” \p \v 3 Aaroni anachitadi zomwezo. Anayimika nyale ndi kuziyangʼanitsa kumene kunali choyikapo nyale monga Yehova analamulira Mose. \v 4 Choyikapo nyalecho chinapangidwa motere: chinasulidwa kuchokera ku golide, kuyambira pa tsinde pake mpaka ku maluwa ake. Choyikapo nyalecho chinapangidwa monga momwe Yehova anaonetsera Mose. \s1 Za Kupatulidwa kwa Alevi \p \v 5 Yehova anawuza Mose kuti, \v 6 “Tenga Alevi pakati pa Aisraeli ndipo uwayeretse. \v 7 Powayeretsa uchite izi: uwawaze madzi oyeretsa ndipo amete thupi lawo lonse ndi kuchapa zovala zawo kuti adziyeretse. \v 8 Atenge ngʼombe yayimuna yayingʼono ndi chopereka cha chakudya cha ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Atengenso ngʼombe ina yayimuna, yayingʼono, ya chopereka chopepesera machimo. \v 9 Ubwere nawo Aleviwo kutsogolo kwa tenti ya msonkhano ndipo usonkhanitse gulu la Aisraeli. \v 10 Ubwere nawo pamaso pa Yehova, ndipo Aisraeli asanjike manja awo pa iwo. \v 11 Aaroni apereke Alevi aja pamaso pa Yehova ngati chopereka choweyula kuchokera kwa Aisraeli kuti akhale okonzeka kugwira ntchito ya Yehova. \p \v 12 “Alevi akatsiriza kusanjika manja awo pa mitu ya ngʼombe zazimuna, imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza ya kwa Yehova, kupepesera machimo a Alevi. \v 13 Uyimiritse Aleviwo pamaso pa Aaroni ndi ana ake aamuna ndipo uwapereke ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. \v 14 Pochita zimenezi mudzapatula Alevi pakati pa Aisraeli ndipo Aleviwo adzakhala anga. \p \v 15 “Utatha kuyeretsa ndi kupereka Aleviwo monga nsembe yoweyula, apite kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano. \v 16 Iwo ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwathunthu kwa Ine. Ndawatenga kuti akhale anga mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa wa Mwisraeli aliyense wamkazi. \v 17 Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa mu Israeli, kaya wa munthu kapena wa ziweto, ndi wanga. Pamene ndinakantha ana oyamba kubadwa ku Igupto, ndinawapatulira kwa Ine mwini. \v 18 Ndipo ndatenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna onse oyamba kubadwa mu Israeli. \v 19 Mwa Aisraeli onse, ndapereka Alevi kuti akhale mphatso kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kugwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti azikapereka nsembe yopepesera machimo, kuti mliri usadzaphe Aisraeli pamene ayandikira ku malo wopatulika.” \p \v 20 Mose, Aaroni pamodzi ndi gulu lonse la Israeli anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose. \v 21 Alevi anadziyeretsa ndi kuchapa zovala zawo. Kenaka Aaroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe yopepesera machimo yowayeretsa. \v 22 Zitatha zimenezi, Alevi anapita kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose. \p \v 23 Yehova anawuza Mose kuti, \v 24 “Ntchito za Alevi ndi izi: Amuna a zaka 24 kapena kuposera pamenepa ndiye azibwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano. \v 25 Koma akakwana zaka makumi asanu, apume pa ntchito yawo ya tsiku ndi tsiku ndi kulekeratu kugwira ntchitoyo. \v 26 Atha kuthandiza abale awo kugwira ntchito za ku tenti ya msonkhano, koma iwowo asamagwire ntchitoyo. Mmenemu ndimo ugawire ntchito yomwe azigwira Alevi.” \c 9 \s1 Paska \p \v 1 Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai pa mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, nati, \v 2 “Aisraeli azichita Paska pa nthawi yake yoyikika. \v 3 Muzichita Paska pa nthawi yake yoyikika, madzulo a tsiku la 14 la mwezi uno, potsata malamulo ndi malangizo ake.” \p \v 4 Choncho Mose anawuza Aisraeli kuti azichita Paska, \v 5 ndipo anachitadi Paskayo mʼchipululu cha Sinai madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose. \p \v 6 Koma ena a iwo sanathe kuchita nawo Paska pa tsiku limenelo chifukwa anali odetsedwa chifukwa chokhudza mtembo. Choncho anabwera kwa Mose ndi Aaroni tsiku lomwelo, \v 7 ndipo anawuza Moseyo kuti, “Ife tadetsedwa chifukwa cha mtembo wa munthu. Nʼchifukwa chiyani taletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena pa nthawi yake?” \p \v 8 Mose anawayankha kuti, “Dikirani mpaka nditamva zimene Yehova walamula zokhudza Inu.” \p \v 9 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, \v 10 “Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene wina mwa inu kapena zidzukulu zanu adetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala pa ulendo, akhoza kuchita nawo Paska ya Yehova. \v 11 Azichita chikondwererochi madzulo a pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Azidya mwana wankhosa wamwamuna pamodzi ndi buledi wopanda yisiti ndi ndiwo zowawa zamasamba. \v 12 Iwo asasiye nyama ina iliyonse mpaka mmawa. Asaswe mafupa aliwonse. Pamene akuchita chikondwerero cha Paska, atsate malangizo onse. \v 13 Koma ngati munthu wina ali woyeretsedwa ndipo sali pa ulendo koma alephera kuchita Paska, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake chifukwa sanabweretse chopereka cha Yehova pa nthawi yake. Munthu ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake. \p \v 14 “ ‘Mlendo amene akukhala pakati panu, nafuna kuchita nawo Paska ya Yehova, achite nawo motsata malamulo ndi malangizo ake. Muzikhala ndi malangizo ofanana a Paska; mbadwa kapena mlendo.’ ” \s1 Mtambo Pamwamba pa Chihema \p \v 15 Pa tsiku limene anayimika chihema, tenti ya umboni, mtambo unaphimba chihemacho. Kuyambira madzulo mpaka mmawa, mtambo umene unali pamwamba pa chihemacho unkaoneka ngati moto. \v 16 Zinkachitika motere mosalekeza: mtambo unkakhala pamwamba pa chihema, ndipo usiku unkaoneka ngati moto. \v 17 Nthawi ina iliyonse mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso, ndipo paliponse pamene mtambo wayima, Aisraeli ankamangapo misasa. \v 18 Aisraeli ankasamuka pamalopo Yehova akawalamula, ndipo ankamanganso misasa Iyeyo akawalamula. Nthawi yonse imene mtambowo wayima pa chihema, ankakhalabe mʼmisasa yawo. \v 19 Mtambowo ukakhala pa chihema nthawi yayitali, Aisraeli ankasungabe lamulo la Yehova ndipo iwo sankasamukanso. \v 20 Nthawi zina mtambowo unkakhala pa chihemapo masiku owerengeka. Aisraeli ankamanga misasa molamulidwa ndi Yehova ndipo ankasamukanso molamulidwa ndi Iyeyo. \v 21 Nthawi zina mtambo unkakhala kuyambira madzulo mpaka mmawa ndipo unkachoka mmawa mwake, ankasamuka. Kaya ndi masana kapena usiku, pamene mtambo wachoka, ankasamuka. \v 22 Ngakhale mtambo ukhale pa chihema masiku awiri kapena mwezi kapena chaka, Aisraeli ankakhalabe pa msasa osachoka. Koma ukachoka, ankasamuka. \v 23 Molamulidwa ndi Yehova ankamanga misasa yawo ndipo ankasamukanso Yehova akawalamula. Ankamvera lamulo la Yehova kudzera mwa Mose. \c 10 \s1 Malipenga Asiliva \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Sula malipenga awiri a siliva, ndipo uziwagwiritsa ntchito posonkhanitsa anthu pamodzi ndiponso powasamutsa mʼmisasa. \v 3 Pamene akuliza malipenga onse awiri, anthu onse asonkhane kwa iwe pa khomo la tenti ya msonkhano. \v 4 Akaliza limodzi lokha, atsogoleri, akulu a mafuko a Aisraeli, asonkhane kwa iwe. \v 5 Akaliza lipenga lochenjeza, misasa yomwe ili kummawa iyambe kusamuka. \v 6 Akaliza lipenga lochenjeza lachiwiri, misasa yakummwera iyambe kusamuka. Kuliza kwa lipenga lochenjeza kudzakhala chizindikiro choyamba ulendo. \v 7 Pofuna kusonkhanitsa anthu, muziliza malipenga, koma mosiyana ndi mmene malipenga ochenjeza amalizidwira. \p \v 8 “Ana a Aaroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipengawo. Zimenezi zikhale zokhazikika kwa inu ndi ku mibado yanu yonse. \v 9 Pamene mukupita ku nkhondo mʼdziko lanu lomwe, kulimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipenga ochenjeza ndipo Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndi kukulanditsani mʼmanja mwa adani anu. \v 10 Komanso pa nthawi yanu ya chisangalalo, pa maphwando anu oyikika ndi maphwando a mwezi watsopano, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu za chiyanjano, ndipo zidzakhala chikumbutso chanu pamaso pa Mulungu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.” \s1 Aisraeli Achoka ku Sinai \p \v 11 Pa chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la 20, mtambo unachoka pamwamba pa chihema cha umboni. \v 12 Ndipo Aisraeli ananyamuka kuchoka mʼchipululu cha Sinai ndipo anayenda malo osiyanasiyana mpaka pamene mtambo unayima mʼchipululu cha Parani. \v 13 Kameneka kanali koyamba kuti Aisraeli anyamuke monga momwe Yehova analamulira Mose. \p \v 14 Magulu a msasa wa Yuda ndiwo anayamba kunyamuka potsata mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu lawo anali Naasoni mwana wa Aminadabu. \v 15 Mtsogoleri wa gulu la fuko la Isakara anali Netanieli mwana wa Zuwara, \v 16 Eliabu mwana wa Heloni ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Zebuloni. \v 17 Kenaka anagwetsa chihema, ndipo Ageresoni ndi Amerari amene ananyamula chihemacho, ananyamuka. \p \v 18 Kenaka magulu a msasa wa fuko la Rubeni ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Elizuri mwana wa Sedeuri. \v 19 Mtsogoleri wa fuko la Simeoni anali Selumieli mwana wa Zurisadai, \v 20 ndipo Eliyasafu mwana wa Deuweli ndiye ankatsogolera fuko la Gadi. \v 21 Kenaka Akohati ananyamuka atanyamula zinthu zopatulika. Chihema chinkayenera kuyimikidwa iwo asanafike. \p \v 22 Magulu a msasa wa Aefereimu anatsatira potsatira mbendera yawo. Elisama mwana wa Amihudi ndiye anali mtsogoleri wawo. \v 23 Gamalieli mwana wa Pedazuri ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Manase. \v 24 Abidani mwana wa Gideoni ndiye anali mtsogoleri wa mtundu wa Benjamini. \p \v 25 Pambuyo pa magulu onse panali magulu a msasa wa Dani, omwe ankateteza magulu onsewa ndipo ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri mwana wa Amisadai. \v 26 Pagieli mwana wa Okirani ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Aseri, \v 27 ndipo mtsogoleri wa mtundu wa Nafutali anali Ahira mwana wa Enani. \v 28 Umenewu ndiwo unali mndandanda wa kayendedwe ka magulu a Aisraeli pamene ankanyamuka ulendo wawo mʼmagulumagulu. \p \v 29 Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.” \p \v 30 Hobabu anayankha kuti, “Ayi, sindipita nanu, ndibwerera ku dziko la kwathu ndi kwa abale anga.” \p \v 31 Ndipo Mose anati, “Pepa usatisiye popeza ukudziwa kumene tingamange misasa mʼchipululu muno ndipo udzakhala maso athu. \v 32 Iweyo ukapita nafe, tidzagawana nawe zinthu zabwino zomwe Yehova adzatipatsa.” \p \v 33 Motero ananyamuka ku Phiri la Yehova nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi la Chipangano cha Yehova linkayenda patsogolo pawo pa masiku atatuwo kuti apeze malo woti apumulepo. \v 34 Mtambo wa Yehova unkawaphimba masana pamene ankasamuka pa misasa yawo. \p \v 35 Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti, \q1 “Dzukani, Inu Yehova! \q2 Adani anu abalalike; \q2 Odana nanu athawe pamaso panu. \p \v 36 “Pamene likupumula, ankanena kuti, \q1 “Bwererani, Inu Yehova, \q2 ku chinamtindi cha Aisraeli.” \c 11 \s1 Moto Wochokera kwa Yehova \p \v 1 Anthu atadandaula kwa Yehova chifukwa cha mavuto awo, Yehovayo anamva ndipo anakwiya kwambiri. Kenaka moto wa Yehova unayaka pakati pawo ndi kutentha zigawo zina za kunja kwa msasa. \v 2 Anthuwo analira kwa Mose ndipo Moseyo atapemphera kwa Yehova, motowo unazima. \v 3 Motero malowo anawatcha Tabera, chifukwa moto wa Yehova unayaka pakati pawo. \s1 Zinziri Zochokera kwa Yehova \p \v 4 Anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraeli anayamba kukhumba chakudya cha ku Igupto ndipo Aisraeli nawonso anayamba kufuwula kwambiri nʼkumati, “Tikanangopeza nyama yoti nʼkudya! \v 5 Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Igupto komanso nkhaka, mavwende, anyezi wamitundumitundu ndi adyo. \v 6 Koma tsopano chilakolako chathu chatha. Sitikuona kanthu kena kakudya koma mana basi!” \p \v 7 Mana ankafanana ndi mbewu zamapira ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wowuma. \v 8 Anthu ankapita kukatola manawo, nʼkumasinja mu mtondo kapena kupera. Ankawaphika mu mʼphika kapena kupanga makeke. Ndipo ankakoma ngati makeke ophikira mafuta a olivi. \v 9 Mame akamagwa pa msasawo usiku ankagwera kumodzi ndi manawo. \p \v 10 Mose anamva anthu a banja lililonse akufuwula, banja lililonse pa khomo la tenti yake. Yehova anakwiya kwambiri ndipo Mose anavutikanso mu mtima. \v 11 Mose anafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani mwabweretsa mavuto otere pa mtumiki wanune? Nʼchiyani chimene ndachita choti sichinakusangalatseni mpaka kundisenzetsa katundu wa anthu onsewa? \v 12 Kodi Ndine amene ndinatenga pathupi pa anthu onsewa? Kodi ndinawabala ndine? Bwanji mukundiwuza kuti ndiwanyamule mʼmanja mwanga, monga momwe mlezi amanyamulira kamwana, kupita nawo ku malo omwe munalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo? \v 13 Ndingayipeze kuti nyama yoti anthu onsewa adye? Iwowa akulirira ine kuti, ‘Tipatse nyama tidye!’ \v 14 Sindingathe kusamala anthu onsewa ndekha. Katundu ameneyu ndi wolemera kwambiri kwa ine. \v 15 Ngati umu ndi mmene muzichitira nane, chonde ingondiphani pompano. Koma ngati mwandikomera mtima ndiye ndisaonenso mavutowa.” \p \v 16 Yehova anawuza Mose kuti, “Undibweretsere anthu 70 ochokera pakati pa akuluakulu a Aisraeli, amene umawadziwa kuti ndiwo atsogoleri komanso akuluakulu a mabanja. Abwere ku tenti ya msonkhano kuti ayime kumeneko pamodzi ndi iwe. \v 17 Ndidzatsika ndi kuyankhula nawe kumeneko, ndipo ndidzatenga mzimu umene uli pa iwe ndi kuyika pa iwowo. Adzakuthandiza kusenza nkhawa za anthuwa ndipo sudzasenzanso wekha.” \p \v 18 “Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi. \v 19 Simudzadya tsiku limodzi lokha, kapena masiku awiri, kapena asanu, khumi kapena masiku makumi awiri, \v 20 koma mwezi wonse, mpaka itakukolani ndi kutopa nayo chifukwa mwakana Yehova yemwe ali pakati panu ndipo mwalira pamaso pake kuti, ‘Bwanji tinachoka ku Igupto?’ ” \p \v 21 Koma Mose anati, “Taonani pano ndili pakati pa anthu 600,000 amene ndi kuyenda nawo ndipo Inuyo mukuti, ‘Ndidzawapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu!’ \v 22 Kodi ngakhale titapha nkhosa ndi ngʼombe, zingawakwanire? Ngakhale titagwira nsomba zonse za mʼnyanja, kodi zingawakwanire iwowa?” \p \v 23 Yehova anayankha Mose kuti, “Kodi dzanja langa ndi lalifupi? Uwona tsopano ngati zimene ndanenazo zichitike kapena ayi.” \p \v 24 Choncho Mose anatuluka nakawuza anthu zomwe Yehova ananena. Anasonkhanitsa pamodzi akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja ndi kuwayimiritsa mozungulira Chihema. \v 25 Ndipo Yehova anatsika mʼmitambo ndi kuyankhula naye ndipo anatengako mzimu womwe unali pa Mose ndi kuwuyika pa akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja. Pamene mzimuwo unakhazikika pa akuluakuluwo, anayamba kunenera koma sanapitirize. \p \v 26 Koma anthu ena awiri omwe mayina awo anali Elidadi ndi Medadi, anatsalira mu msasa. Anali nawo mʼgulu la olembedwa aja, koma sanapite nawo ku Chihema. Komabe mzimu unakhala pa iwo ndipo ananenera ali mu msasa. \v 27 Mnyamata wina anathamanga kudzawuza Mose kuti, “Elidadi ndi Medadi akunenera mu msasa.” \p \v 28 Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha kuti, “Mbuye wanga Mose, aletseni!” \p \v 29 Koma Mose anati, “Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikanakonda kuti anthu onse a Yehova akhale aneneri ndi kuti Yehova ayike mzimu wake pa iwo!” \v 30 Mose ndi akuluakulu a Israeli aja anabwerera ku msasa. \p \v 31 Pamenepo Yehova anawutsa mphepo yochokera ku nyanja imene inabweretsa zinziri. Zinzirizo zinagwera pansi kuzungulira msasa, mtunda wa kilomita imodzi mbali zonse ndipo msinkhu wake unali mita imodzi. \v 32 Tsiku limenelo masana onse mpaka usiku ndiponso tsiku lotsatiralo, anthu anatuluka kunja kukatola zinziri. Palibe amene anasonkhanitsa zochepera makilogalamu 1,000 ndipo anaziyanika kuzungulira msasa wonse. \v 33 Koma pamene anthuwo ankadya nyamayo, asanayimeze nʼkomwe, ukali wa Yehova unafika pa iwo ndipo Iye anawakantha ndi mliri woopsa. \v 34 Nʼchifukwa chake malowo anawatcha Kibiroti Hatava chifukwa pamenepo anakwirirapo anthu osusuka aja. \p \v 35 Kuchoka pa Kibiroti Hatava anthuwo anayenda kupita ku Heziroti ndipo anakhala kumeneko kwa kanthawi. \c 12 \s1 Miriamu ndi Aaroni Atsutsana ndi Mose \p \v 1 Miriamu ndi Aaroni anayamba kuyankhula motsutsana ndi Mose chifukwa cha mkazi wa ku Kusi, popeza Moseyo anakwatira Mkusi. \v 2 Iwowo anafunsa kuti, “Kodi Yehova anayankhula kudzera mwa Mose yekha? Kodi sanayankhule kudzeranso mwa ife?” Ndipo Yehova anamva zimenezi. \p \v 3 (Koma Mose anali munthu wodzichepetsa kwambiri kuposa munthu aliyense pa dziko lapansi). \p \v 4 Nthawi yomweyo Yehova anati kwa Mose, Aaroni ndi Miriamu, “Bwerani ku tenti ya msonkhano nonse atatu.” Ndipo atatuwo anapitadi kumeneko. \v 5 Tsono Yehova anatsika mu mtambo, nayima pa khomo la chihema. Kenaka anayitana Aaroni ndi Miriamu. Ndipo onse awiri atapita patsogolo, \v 6 Mulungu anati, “Mverani mawu anga: \q1 “Pakakhala mneneri wa Yehova pakati panu, \q2 ndimadzionetsera kwa iyeyo mʼmasomphenya, \q2 ndimayankhula naye mʼmaloto. \q1 \v 7 Koma sinditero ndi Mose mtumiki wanga; \q2 Iyeyu ndi wokhulupirika mʼnyumba yanga yonse. \q1 \v 8 Ndimayankhula naye maso ndi maso, \q2 momveka bwino osati mophiphiritsa; \q2 ndipo amaona maonekedwe a Yehova. \q1 Nʼchifukwa chiyani simunaope \q2 kuyankhula motsutsana ndi Mose mtumiki wanga?” \p \v 9 Ndipo Yehova anawakwiyira, nachoka. \p \v 10 Pamene mtambo unachoka pamwamba pa Chihema, taonani, Miriamu anagwidwa ndi khate. Aaroni atachewuka anaona Miriamu ali ndi khate; \v 11 ndipo Aaroni anawuza Mose kuti, “Pepani mbuye wanga, musatilange chifukwa cha tchimo limene tachita mopusa. \v 12 Musalole kuti Miriamu akhale ngati mwana wobadwa wakufa kuchoka mʼmimba mwa amayi ake, thupi lake litawonongeka.” \p \v 13 Tsono Mose anafuwulira Yehova kuti, “Chonde Inu Mulungu, muchiritseni!” \p \v 14 Yehova anayankha Mose kuti, “Abambo ake akanamulavulira malovu mʼmaso, kodi sakanakhala wonyozeka masiku asanu ndi awiri? Mutsekereni kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri, kenaka mumulowetsenso.” \v 15 Choncho anamutsekera Miriamu kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri ndipo anthu sanayende ulendo wawo mpaka Miriamu atamulowetsanso. \p \v 16 Pambuyo pake anthu ananyamuka ku Heziroti ndi kukamanga mʼchipululu cha Parani. \c 13 \s1 Kukazonda Kanaani \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.” \p \v 3 Monga mwa mawu a Yehova, Mose anawatuma kuchokera ku chipululu cha Parani. Onsewo anali atsogoleri a Aisraeli. \v 4 Mayina awo ndi awa: \b \li1 kuchokera ku fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri; \li1 \v 5 kuchokera ku fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori; \li1 \v 6 kuchokera ku fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune; \li1 \v 7 kuchokera ku fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe; \li1 \v 8 kuchokera ku fuko la Efereimu, Hoseya mwana wa Nuni; \li1 \v 9 kuchokera ku fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu; \li1 \v 10 kuchokera ku fuko la Zebuloni, Gadieli mwana wa Sodi; \li1 \v 11 kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi; \li1 \v 12 kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali; \li1 \v 13 kuchokera ku fuko la Aseri, Seturi mwana wa Mikayeli; \li1 \v 14 kuchokera ku fuko la Nafutali, Naabi mwana wa Vofisi; \li1 \v 15 kuchokera ku fuko la Gadi, Geuweli mwana wa Maki. \b \m \v 16 Amenewa ndiwo mayina a anthu amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo. (Hoseya mwana wa Nuni, Mose anamupatsa dzina loti Yoswa). \b \p \v 17 Mose atawatuma kuti akazonde Kanaani anati, “Mupite kudzera ku Negevi, mukapitirire mpaka ku dziko la mapiri. \v 18 Mukaone dzikolo kuti ndi lotani ndi anthu okhala mʼmenemo ngati ndi amphamvu kapena ofowoka, ochepa kapena ambiri. \v 19 Nanga dziko limene akukhalako ndi lotani? Ndi labwino kapena loyipa? Mizinda imene akukhalamo ndi yotani? Kodi ilibe malinga kapena ndi ya malinga? \v 20 Nthaka yake ndi yotani? Yachonde kapena yopanda chonde? Kodi dzikolo lili ndi mitengo kapena lilibe mitengo? Mukayesetse kubweretsako zipatso za mʼdzikomo.” (Inali nthawi yamphesa zoyamba kupsa). \p \v 21 Choncho anapita kukazonda dzikolo kuchokera ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu, mopenyana ndi Lebo Hamati. \v 22 Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto). \v 23 Atafika ku chigwa cha Esikolo, anadulako nthambi ya mpesa ya phava limodzi la mphesa ndipo anthu awiri ananyamulizana, natenganso makangadza ndi nkhuyu. \v 24 Malo amenewo anawatcha chigwa cha Esikolo chifukwa cha phava la mphesa limene Aisraeli anadula kumeneko. \v 25 Patapita masiku makumi anayi, anthu aja anabwerako kokazonda dziko lija. \s1 Kufotokoza Zomwe Anakaona \p \v 26 Ndipo atabwerako anapita kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa Aisraeli onse ku Kadesi mʼchipululu cha Parani. Kumeneko anafotokozera anthu onse nawaonetsanso zipatso za mʼdzikolo. \v 27 Anthuwo anafotokozera Mose kuti, “Tinapita ku dziko komwe munatituma. Dzikolo ndi loyenda mkaka ndi uchi ndipo zipatso zake ndi izi. \v 28 Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko. \v 29 Aamaleki amakhala ku Negevi, Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala mʼdziko la mapiri ndipo Akanaani amakhala pafupi ndi nyanja, mʼmbali mwa Yorodani.” \p \v 30 Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.” \p \v 31 Koma anthu aja amene anapita naye anati, “Sitingathe kulimbana ndi anthuwo popeza ndi amphamvu kuposa ifeyo.” \v 32 Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali. \v 33 Kumeneko tinaona Anefili (ana a Aanaki ochokera kwa Nefili). Ifeyo timangodziona ngati ziwala mʼmaso mwawo, ndipo kwa iwo timaonekadi motero ndithu.” \c 14 \s1 Anthu Awukira \p \v 1 Usiku umenewo gulu lonse la Aisraeli linalira mofuwula kwambiri. \v 2 Ndipo Aisraeli onse anayankhula motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Gulu lonse linanena kwa iwo kuti, “Kunali bwino tikanafera ku Igupto kapena mʼchipululu muno! \v 3 Nʼchifukwa chiyani Yehova akutilowetsa mʼdziko limenelo? Kodi kuti tikaphedwe ndi lupanga? Kuti akazi ndi ana athu akatengedwe ngati katundu wolanda ku nkhondo? Kodi sikungakhale bwino kuti tibwerere ku Igupto?” \v 4 Ndipo anawuzana wina ndi mnzake kuti, “Tiyeni tisankhe mtsogoleri ndipo tibwerere ku Igupto.” \p \v 5 Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa pansi chafufumimba pamaso pa Aisraeli onse omwe anasonkhana pamenepo. \v 6 Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, omwe anali amodzi mwa amene anakazonda nawo dziko, anangʼamba zovala zawo \v 7 ndipo anati kwa gulu lonse la Aisraeli, “Dziko limene tinakayendamo ndi kuliona ndi labwino kwambiri zedi. \v 8 Ngati Yehova akukondwera nafe, adzatitsogolera kulowa mʼdziko limenelo. Dziko loyenda mkaka ndi uchi adzalipereka kwa ife, \v 9 koma musawukire Yehova. Komanso musaope anthu a mʼdzikomo, pakuti tidzawagonjetsa. Chitetezo chawachokera, koma ife Yehova ali nafe. Musawaope.” \p \v 10 Koma gulu lonse linayankhula zofuna kuwagenda miyala. Pamenepo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisraeli onse ku tenti ya msonkhano. \v 11 Yehova anawuza Mose kuti, “Anthu awa adzandinyoza mpaka liti? Sadzandikhulupirira mpaka liti, ngakhale ndachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi pakati pawo? \v 12 Ndidzawakantha ndi mliri ndi kuwawononga. Koma ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwo.” \p \v 13 Mose anati kwa Yehova, “Aigupto adzamva zimenezi! Mwa mphamvu yanu munawatulutsa anthu amenewa pakati pawo. \v 14 Ndipo iwowo adzawuza anthu okhala mʼdziko lino zimenezi. Anthuwa amva kale kuti Inu Yehova mumakhala pakati pa anthu amenewa ndi kuti Inuyo Yehova mwawaonekera maso ndi maso. Mtambo wanu umakhala pamwamba pawo ndiponso mumayenda nawo mu mtambo woyima, masana ndi moto woyima, usiku. \v 15 Tsono mukawapha anthu onsewa nthawi imodzi, mayiko amene anamva za Inu adzati, \v 16 ‘Yehova walephera kuwalowetsa anthuwo mʼdziko lomwe anawalonjeza molumbira, ndipo wawapha mʼchipululu.’ \p \v 17 “Chonde Ambuye wonetsani mphamvu yanu monga munalonjezera kuti, \v 18 ‘Yehova sakwiya msanga, ndipo ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika, wokhululukira tchimo ndi kuwukira. Koma Iye sadzaleka kulanga ochimwa. Iyeyo amalanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo kufikira mʼbado wachitatu ndi wachinayi.’ \v 19 Chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, akhululukireni anthuwa tchimo lawo monga mwakhala mukuwakhululukira kuchokera pa nthawi imene anachoka ku Igupto mpaka tsopano.” \p \v 20 Yehova anayankha kuti, “Ndawakhululukira monga wapemphera. \v 21 Komabe, ndikunenetsa kuti pali Ine, ndiponso pamene dziko lapansi ladzaza ndi ulemerero wa Yehova, \v 22 palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinazichita ku Igupto ndi mʼchipululu muno, koma osandimvera ndi kundiyesa kokwanira kakhumi, \v 23 palibe ndi mmodzi yemwe wa anthu amenewa amene adzaone dziko limene ndinalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo. Aliyense amene anandinyoza sadzaliona dzikolo. \v 24 Koma mtumiki wanga Kalebe, pakuti ali ndi mtima wosiyana ndi ena ndiponso amanditsatira ndi mtima wonse, ndidzamulowetsa mʼdziko limene anapitamolo ndipo zidzukulu zake zidzalandira dzikolo ngati cholowa chawo. \v 25 Ndipo popeza kuti Aamaleki ndi Akanaani akukhala ku chigwa, mawa mubwerere ndipo mupite ku chipululu podzera ku Nyanja Yofiira.” \p \v 26 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, \v 27 “Kodi anthu oyipawa adzangʼungʼudza ndi kutsutsana nane mpaka liti? Ndamva madandawulo a Aisraeli ongʼungʼudzawa. \v 28 Tsono awuze kuti, ‘Ndikulumbira pali Ine,’ akutero Yehova, ‘Ndidzakuchitirani zinthu zonse zimene ndamva inu mukunena: \v 29 Mitembo yanu idzakhala ili ngundangunda mʼchipululu muno; mtembo wa munthu aliyense pakati panu amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, amene anawerengedwa pa chiwerengero chija ndipo anangʼungʼudza motsutsana nane. \v 30 Palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzalowe mʼdziko lomwe ndinalumbira mokweza manja kuti likhale lanu, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni. \v 31 Koma ana anu amene mukunena kuti adzatengedwa ngati katundu wolanda ku nkhondo, Ine ndidzawalowetsa kuti akasangalale mʼdziko limene munalikana. \v 32 Koma inu mitembo yanu idzakhala ngundangunda mʼchipululu muno. \v 33 Ana anu adzakhala abusa mʼchipululu muno zaka makumi anayi, kuvutika chifukwa cha kusakhulupirika kwanu, mpaka munthu womaliza mwa inu atafa mʼchipululu muno. \v 34 Mudzavutika chifukwa cha machimo anu kwa zaka makumi anayi Chaka chimodzi chikuyimira tsiku limodzi la masiku makumi anayi amene munakazonda dziko lija ndipo mudzadziwa kuyipa kwake kwa kukangana ndi Ine.’ \v 35 Ine Yehova, ndanena, ndidzachitadi zimenezi kwa anthu onse oyipawa, amene agwirizana kunditsutsa. Adzathera mʼchipululu momwe muno, adzafera muno basi.” \p \v 36 Ndipo anthu amene Mose anawatuma kukazonda dziko aja anachoka pamaso pake nachititsa gulu lonse la anthu kuwukira Moseyo chifukwa chofalitsa mbiri yoyipa ya dzikolo. \v 37 Anthu amene ankafalitsa mbiri yoyipa ya dzikolo anakanthidwa ndi mliri ndipo anafa pamaso pa Yehova. \v 38 Mwa anthu amene anakaona dzikolo, Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune ndi okhawo amene anapulumuka. \p \v 39 Mose atafotokoza izi kwa Aisraeli onse, anthuwo analira kwambiri. \v 40 Mmamawa tsiku linalo anapita mbali ya ku dziko la mapiri. Iwo anati, “Tachimwa, tipita ku dziko limene Yehova anatilonjeza.” \p \v 41 Koma Mose anati, “Chifukwa chiyani simukumvera lamulo la Yehova? Zimenezi sizitheka! \v 42 Musapite chifukwa Yehova sali pakati panu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu \v 43 chifukwa kumeneko mukakumana ndi Aamaleki ndi Akanaani. Popeza mwaleka kutsata Yehova, Iyeyo sadzakhala nanu ndipo mudzaphedwa ndi lupanga.” \p \v 44 Komabe mwa maganizo awo anapita molunjika dziko la mapiri ngakhale kuti Mose sanachoke ndi Bokosi la Chipangano la Yehova pa msasa. \v 45 Koma Aamaleki ndi Akanaani amene ankakhala ku dziko lamapirilo anatsika ndi kumenyana nawo ndipo anawakantha mʼnjira yonse mpaka ku Horima. \c 15 \s1 Zopereka Zapadera \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo, \v 3 ndipo mukamadzapereka kwa Yehova, nsembe yotentha pa moto ya ngʼombe kapena nkhosa monga fungo lokoma kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena nsembe zina, nsembe yapadera chifukwa cha lumbiro kapena nsembe yoperekedwa mwaufulu kapenanso yoperekedwa pa chikondwerero, \v 4 munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi. \v 5 Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’ ” \p \v 6 “Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, muzikakonzanso chopereka cha chakudya cholemera makilogalamu awiri a ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita imodzi ndi theka, \v 7 ndi vinyo wokwanira lita imodzi ndi theka ngati chopereka cha chakumwa. Muzikapereka monga nsembe yopereka fungo lokoma kwa Yehova. \p \v 8 “ ‘Pamene mukukonza mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse: ya lumbiro lapadera kapena nsembe yachiyanjano kwa Yehova, \v 9 pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri. \v 10 Komanso muzibweretsa vinyo wokwanira malita awiri monga chopereka chachakumwa. Imeneyi idzakhala chopereka chotentha pa moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. \v 11 Ngʼombe yayimuna iliyonse kapena nkhosa yayimuna iliyonse, mwana wankhosa aliyense kapena mbuzi yayingʼono, zizikonzedwa motere. \v 12 Ngakhale zingachuluke chotani, chitani izi kwa iliyonse ya nyamazo. \p \v 13 “ ‘Mbadwa iliyonse ya mu Israeli izichita zimenezi pamene ibweretsa nsembe yotentha pa moto kuti ikhale fungo lokoma kwa Yehova. \v 14 Ku mibado yanu yonse ya mʼtsogolo, pamene mlendo kapena wina aliyense wokhala pakati panu apereka chopereka chotentha pa moto kuti chikhale fungo lokoma kwa Yehova, azichita mofanana ndi momwe inu mumachitira. \v 15 Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova. \v 16 Mudzakhale ndi malamulo ndi miyambo yofanana, inuyo ndi mlendo wokhala pakati panu.’ ” \p \v 17 Yehova anawuza Mose kuti, \v 18 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo unene kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukutengeraniko \v 19 ndipo mukakadya chakudya cha mʼdzikolo, mukapereke gawo lina kwa Yehova monga chopereka. \v 20 Pa buledi wanu woyamba, mukapereke mmodzi monga nsembe, ngati chopereka chochokera ku malo wopunthira tirigu. \v 21 Pa mibado yanu yonse muzidzapereka chopereka ichi kwa Yehova kuchokera ku zakudya zanu zoyamba za mʼnthaka. \s1 Chopereka Chopepesera Machimo Ochita Mosadziwa \p \v 22 “ ‘Ndipo ngati muchimwa mosadziwa posasunga ena mwa malamulo awa amene Yehova wapereka kwa Mose, \v 23 lina lililonse mwa malamulo a Yehova amene wapereka kwa inu kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Yehova anawapereka mpaka mibado ya mʼtsogolo, \v 24 ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa. \v 25 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo. \v 26 Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa. \p \v 27 “ ‘Koma ngati munthu mmodzi achimwa mosadziwa, ayenera kubweretsa mbuzi yayikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. \v 28 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimowo pamaso pa Yehova chifukwa cha munthu yemwe anachimwa mosadziwayo. Nsembe yopepesera tchimo lakelo ikaperekedwa, munthuyo adzakhululukidwa. \v 29 Lamulo lomweli ligwiritsidwe ntchito kwa aliyense wochimwa mosadziwa, kaya ndi mbadwa ya mu Israeli kapena mlendo. \p \v 30 “ ‘Koma aliyense amene achimwa mwadala, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, nachitira chipongwe Yehova, ameneyo achotsedwe ndithu pakati pa anthu ake. \v 31 Popeza wanyoza mawu a Yehova ndi kuphwanya malamulo ake. Munthu ameneyo achotsedwe ndithu, kuchimwa kwake kudzakhala pa iyeyo.’ ” \s1 Wosasunga Sabata Aphedwa \p \v 32 Aisraeli ali mʼchipululu, munthu wina anapezeka akutola nkhuni tsiku la Sabata. \v 33 Amene anamupeza akutola nkhunizo anabwera naye kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa gulu lonse \v 34 ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa sankadziwa choti achite naye. \v 35 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Munthu ameneyu ayenera kuphedwa. Gulu lonse liyenera kumugenda ndi miyala kunja kwa msasa.” \v 36 Choncho gululo linamutengera kunja kwa msasa ndi kumupha pomugenda ndi miyala, monga momwe Yehova analamulira Mose. \s1 Mphonje pa Zovala \p \v 37 Yehova anawuza Mose kuti, \v 38 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pa mibado yanu yonse muzisokerera mphonje pa ngodya za zovala zanu ndipo pa ngodya ya mphonje iliyonse azisokererapo chingwe chobiriwira. \v 39 Mudzakhala ndi mphonje zimenezi kuti mukaziona muzikakumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwamvera kuti musamatsatenso zilakolako za mʼmitima mwanu ndi za maso anu. \v 40 Motero mudzakumbukira kumvera malamulo anga ndipo mudzakhala opatulikira a Mulungu wanu. \v 41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ” \c 16 \s1 Kora, Datani ndi Abiramu Awukira Mose \p \v 1 Kora mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Perezi, ana a Rubeni, anayamba kudzikuza, \v 2 ndipo anawukira Mose. Mʼgulu mwawo munali atsogoleri a Aisraeli 250, anthu otchuka amene anasankhidwa ndi anthu pa msonkhano. \v 3 Iwo anasonkhana kudzatsutsana ndi Mose ndi Aaroni nawawuza kuti, “Mwawonjeza! Anthu onsewa ndi oyera, aliyense wa iwo, ndipo Yehova ali pakati pawo. Chifukwa chiyani mukudzikuza pakati pa gulu lonse la Yehova?” \p \v 4 Mose atamva izi, anagwa chafufumimba. \v 5 Ndipo iye anawuza Kora ndi anthu onse amene ankamutsatira kuti, “Yehova mawa mmawa adzasonyeza yemwe ndi wake ndiponso amene ndi woyera mtima. Munthuyo adzabwera pafupi ndi Iye. Munthu amene adzamusankheyo adzamusendeza pafupi. \v 6 Iwe Kora pamodzi ndi onse amene akukutsatira chitani izi: Tengani zofukizira \v 7 ndipo mawa muyikemo moto ndi lubani pamaso pa Yehova. Munthu amene Yehova amusankhe ndiye amene ali woyera. Alevi inu mwawonjeza kwambiri!” \p \v 8 Mose anawuzanso Kora kuti, “Inu Alevi, tsopano tamverani! \v 9 Kodi sizinakukwanireni kuti Mulungu wa Israeli anakupatulani pakati pa gulu lonse la Aisraeli ndi kukubweretsani pafupi ndi Iye, kuti muzigwira ntchito ku nyumba ya Yehova ndi kumayima pamaso pa gulu, kumatumikira? \v 10 Wakubweretsa iwe pamodzi ndi Alevi anzako kufupi ndi Iye mwini. Koma tsopano ukufuna kutenganso unsembe. \v 11 Nʼkulakwira Yehova kuti iwe ndi gulu lako lonseli mwasonkhana kuti mutsutsane ndi Yehova. Kodi Aaroni ndani kuti muzikangana naye?” \p \v 12 Kenaka Mose anayitana Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu koma iwo anati, “Sitibwera! \v 13 Kodi sikukwanira kuti unatitulutsa, kutichotsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphe mʼchipululu muno? Kodi tsopano ukufunanso kutilemetsa? \v 14 Kuwonjezera apo, sunatilowetse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kapena kutipatsa malo wolima ndi minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuchotsa maso a anthuwa? Ayi, sitibwera!” \p \v 15 Pamenepo Mose anakwiya kwambiri ndipo anati kwa Yehova, “Musalandire chopereka chawo. Sindinatenge kalikonse kwa iwo ngakhale bulu, ndiponso sindinalakwire wina aliyense wa iwo.” \p \v 16 Mose anati kwa Kora, “Iwe ndi okutsatira onse mudzaonekere pamaso pa Yehova mawa, iweyo ndi iwowo pamodzi ndi Aaroni. \v 17 Munthu aliyense akatenge chofukizira ndi kuyikamo lubani, zofukizira 250 zonse pamodzi ndi kuzibweretsa pamaso pa Yehova. Iwe ndi Aaroni mudzabweretsenso zofukizira zanu.” \v 18 Choncho munthu aliyense anatenga chofukizira chake nayikamo moto ndi lubani, ndipo anayima pamodzi ndi Mose ndi Aaroni pa khomo la tenti ya msonkhano. \v 19 Kora atasonkhanitsa omutsatira ake onse amene amatsutsa nawo pa khomo la tenti ya msonkhano, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa gulu lonselo. \v 20 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, \v 21 “Chokani pakati pa gulu ili kuti ndithetse mkanganowu kamodzinʼkamodzi.” \p \v 22 Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa chafufumimba ndipo analira mokweza, “Chonde Mulungu, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, kodi mudzakwiyira gulu lonse pamene munthu mmodzi yekha ndiye amene wachimwa?” \p \v 23 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, \v 24 “Uza gulu lonse kuti, ‘Khalani kutali ndi matenti a Kora, Datani ndi Abiramu.’ ” \p \v 25 Mose anayimirira napita kwa Datani, Abiramu ndi kwa akuluakulu a Israeli amene ankamutsatira. \v 26 Anachenjeza gulu lonse kuti, “Khalani kutali ndi matenti a anthu oyipawa! Musakhudze kanthu kawo kalikonse, mukatero mudzawonongedwa limodzi nawo chifukwa cha machimo awo.” \v 27 Choncho anthuwo anachokadi ku matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali atatuluka nayima pamodzi ndi akazi awo, ana awo ndi makanda awo pa makomo a matenti awo. \p \v 28 Tsono Mose anati, “Umu ndi mmene mudzadziwire kuti Yehova ndiye amene anandituma kuti ndichite zinthu zonsezi ndipo kuti si maganizo anga. \v 29 Ngati anthu awa afa ndi imfa ya chilengedwe ndi kuwachitikira zomwe zimachitikira munthu aliyense, ndiye kuti Yehova sananditume. \v 30 Koma Yehova akachita china chake chachilendo, nthaka nitsekula pakamwa pake ndi kuwameza iwo pamodzi ndi zonse zimene ali nazo, iwowa nʼkulowa mʼmanda ali moyo, pamenepo mudzazindikira kuti anthu amenewa ananyoza Yehova.” \p \v 31 Atangotsiriza kuyankhula zimenezi, nthaka ya pamene anayimapo inagawikana \v 32 ndipo dziko linatsekula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi nyumba zawo ndi anthu onse a Kora ndi katundu wawo yense. \v 33 Analowa mʼmanda amoyo pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. Nthaka inawatsekera ndi kuwawononga ndipo sanaonekenso. \v 34 Atamva kulira kwawo, Aisraeli onse amene anali pafupi ndi anthuwo anathawa akufuwula kuti, “Nthaka imezanso ife!” \p \v 35 Ndipo moto wochokera kwa Yehova unabwera nʼkunyeketsa anthu 250 amene ankapereka nsembe yofukiza aja. \p \v 36 Yehova anawuza Mose kuti, \v 37 “Uza Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe kuti atenge zofukizirazo pakati pa mitembo yopsererayo ndipo amwazire makalawo kutali chifukwa zofukizirazo nʼzopatulika. \v 38 Izi ndi zofukizira za anthu omwe anafa chifukwa cha uchimo wawo. Musule zofukizirazo kuti zikhale zophimbira pa guwa lansembe, chifukwa zinaperekedwa kwa Yehova ndipo ndi zopatulika. Zimenezi zikhale chizindikiro kwa Aisraeli.” \p \v 39 Choncho Eliezara, wansembe, anasonkhanitsa zofukizira zamkuwa zija zomwe anthu opsererawo anabwera nazo ndipo anazisula kuti zikhale zophimbira pa guwa lansembe, \v 40 monga momwe Yehova anamulangizira kudzera mwa Mose. Chimenechi chinali chikumbutso kwa Aisraeli kuti munthu wina aliyense, kupatula zidzukulu za Aaroni, sayenera kupsereza lubani pamaso pa Yehova, kuopa kuti munthu woteroyo angakhale ngati Kora ndi omutsatira ake. \p \v 41 Tsiku lotsatira, gulu lonse la Aisraeli linatsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Iwo anati, “Inu mwapha anthu a Yehova.” \p \v 42 Koma pamene anthuwo anasonkhana kuti atsutsane ndi Mose ndi Aaroni, atatembenuka kuyangʼana ku tenti ya msonkhano, mwadzidzidzi mtambo unaphimba tentiyo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera. \v 43 Pamenepo Mose ndi Aaroni anapita patsogolo pa tenti ya msonkhano ija \v 44 ndipo Yehova anawuza Mose kuti, \v 45 “Chokani pakati pa gulu la anthuwa kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.” Ndipo iwo anagwa pansi chafufumimba. \p \v 46 Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Tenga chofukizira chako ndipo ikamo lubani pamodzi ndi moto wochokera pa guwa lansembe, fulumira, pita pa gulu la anthuwo ndipo ukachite nsembe yopepesera machimo awo popeza mkwiyo wa Yehova wafika, mliri wayamba.” \v 47 Ndipo Aaroni anachita monga ananenera Mose, nathamangira mʼkatikati mwa gulu la anthuwo. Pamenepo nʼkuti mliri utayamba kale pakati pa anthu aja ndipo Aaroni anafukiza lubani ndi kupereka nsembe yopepesera machimo awo. \v 48 Iye anayimirira pakati pa anthu amoyo ndi akufa ndipo mliri unaleka. \v 49 Komabe anthu 14, 700 anafa ndi mliriwo, kuwonjezera pa aja amene anafa chifukwa cha Kora. \v 50 Ndipo Aaroni anabwerera kwa Mose ku khomo la tenti ya msonkhano, chifukwa mliriwo unali utatha. \c 17 \s1 Kuphukira kwa Ndodo ya Aaroni \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo akupatse ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake. \v 3 Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse. \v 4 Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe. \v 5 Ndodo ya munthu amene ndamusankha idzachita maluwa potero ndidzaletsa madandawulo osatha a Aisraeli otsutsana nawe.” \p \v 6 Choncho Mose anayankhula ndi Aisraeli, ndipo atsogoleri awo anapereka ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ndodo ya Aaroni inali pakati pa ndodo zawozo. \v 7 Mose anayika ndodozo pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. \p \v 8 Pa tsiku lotsatira Mose analowa mu tenti ya msonkhanoyo ndipo anaona kuti ndodo ya Aaroni, yomwe inkayimira fuko la Levi, sinangophuka masamba chabe, komanso inachita maluwa nʼkubala zipatso za alimondi. \v 9 Choncho Mose anatulutsa ndodo zonse pamaso pa Yehova napita nazo kwa Aisraeli onse. Iwowo anaziona ndipo munthu aliyense anatenga ndodo yake. \p \v 10 Yehova anawuza Mose kuti, “Bwezera ndodo ya Aaroni patsogolo pa Bokosi la Umboni, kuti chikhale chizindikiro cha kuwukira kwawo. Zimenezi zidzathetsa kudandaula kwawo kotsutsana nane, kuopa kuti angafe.” \v 11 Mose anachita monga Yehova anamulamulira. \p \v 12 Aisraeli anati kwa Mose, “Tikufa! Tatayika, tonse tatayika! \v 13 Aliyense woyandikira chihema adzafa. Kodi ndiye kuti tonse tikufa?” \c 18 \s1 Ntchito za Ansembe ndi Alevi \p \v 1 Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu. \v 2 Ubweretse Alevi, abale ako, kuchokera ku fuko la abambo ako kuti azikhala ndi iwe ndi kumakuthandiza pamodzi ndi ana ako amuna pamene mukutumikira mu tenti ya umboni. \v 3 Iwowo azikutumikirani ndipo azichita ntchito zonse za ku tenti, koma asamafike pafupi ndi zipangizo za ku malo opatulika kapena guwa lansembe, kuopa kuti iwo ndi inu mungafe. \v 4 Azikhala ndi inu ndipo azisamalira ntchito yonse ya mu tenti ya msonkhano koma munthu wina aliyense wapadera sayenera kufika pafupi nanu. \p \v 5 “Inuyo muzisamalira malo wopatulika ndi guwa lansembe, kuti ukali wa Yehova usawagwerenso Aisraeli. \v 6 Ine mwini ndasankha Alevi, abale ako, pakati pa Aisraeli ngati mphatso yako ndipo aperekedwa kwa Yehova kuti azigwira ntchito ku tenti ya msonkhano. \v 7 Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa. \s1 Zopereka za Ansembe ndi Alevi \p \v 8 “Kenaka Yehova anati kwa Aaroni, ona, Ine mwini ndikukuyika kuti ukhale woyangʼanira zopereka zobwera kwa Ine; zopereka zonse zopatulika za Aisraeli zimene amapereka kwa ine ndi kuzipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ngati gawo lanu la nthawi zonse. \v 9 Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna. \v 10 Muzidya zimenezo ngati zinthu zopatulika kwambiri; mwamuna aliyense adyeko. Uzitenge kukhala zopatulika. \p \v 11 “Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako. \p \v 12 “Ndikukupatsani mafuta onse abwino kwambiri a olivi ndi vinyo yense watsopano wabwino kwambiri ndi tirigu yense zomwe Aisraeli amapereka kwa Yehova ngati zipatso zoyamba pa zokolola zawo. \v 13 Zipatso zonse zoyamba kucha za mʼdziko lawo zomwe amapereka kwa Yehova zidzakhala zako. Aliyense mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa angathe kudyako. \p \v 14 “Chilichonse mu Israeli chomwe chapatulidwira Yehova ndi chako. \v 15 Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa. \v 16 Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika. \p \v 17 “Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. \v 18 Nyama yake ikhale yanu monga momwe chimakhalira chidale cha nsembe yoweyula ndi ntchafu za miyendo ya kumanja, zonsezi ndi zako. \v 19 Zonse zimene mwazichotsa ku zopereka zoyera zomwe Aisraeli anapereka kwa Yehova ndazipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lanu nthawi zonse. Ili ndi pangano losatha la mchere pamaso pa Yehova kwa iwe ndi ana ako.” \p \v 20 Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli. \p \v 21 “Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano. \v 22 Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo Aisraeli asamapite pafupi ndi tenti ya msonkhano. Ngati atero adzasenza zotsatira za tchimo lawo ndipo adzafa. \v 23 Alevi ndi amene azidzagwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano ndipo adzalangidwa chilichonse chikalakwika. Ili ndi lamulo losatha kwa mibado yawo yonse. Iwowo sadzalandira cholowa pakati pa Aisraeli. \v 24 Mʼmalo mwake, ndikuwapatsa Aleviwo chakhumi ngati cholowa chawo chimene Aisraeli amapereka kwa Yehova. Nʼchifukwa chake zokhudza iwo ndinati: ‘Sadzakhala ndi cholowa pakati pa Aisraeli.’ ” \p \v 25 Yehova anati kwa Mose, \v 26 “Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova. \v 27 Chopereka chanucho chidzawerengedwa kwa inu ngati tirigu wochokera kopunthira kapena ngati mphesa zopsinya kuchokera kopsinyira mphesa. \v 28 Mwa njira imeneyi inunso muzipereka chopereka kwa Yehova kuchokera ku chakhumi chanu chilichonse chimene mumalandira kuchokera kwa Aisraeli. Kuchokera ku chakhumicho muziperekako gawo la Yehova kwa Aaroni, wansembe. \v 29 Muyenera kupereka monga gawo la Yehova magawo abwino kwambiri ndi opatulika a chilichonse chimene chapatsidwa kwa inu.’ \p \v 30 “Nena kwa Alevi: ‘Pamene mupereka gawo labwino lopambana zonse, gawo limenelo lidzawerengedwa kwa inu ngati lochokera popunthira tirigu kapenanso kopsinyira mphesa. \v 31 Inu ndi a pa banja panu mungathe kudyera zimenezi paliponse chifukwa ndi malipiro a ntchito yanu ya ku tenti ya msonkhano. \v 32 Popereka gawo labwino kwambirilo simudzapezeka olakwa. Mukatero simudzadetsa zopereka zoyera za Aisraeli, ndipo simudzafa.’ ” \c 19 \s1 Phulusa ndi Madzi Oyeretsera \p \v 1 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: \v 2 “Lamulo limene Yehova wapereka ndi ili: Uzani Aisraeli kuti abweretse ngʼombe yayikazi yofiira yopanda chilema chilichonse imenenso sinakhalepo pa goli. \v 3 Muyipereke kwa Eliezara, wansembe ndipo apite nayo kunja kwa msasa. Iphedwe iye ali pomwepo. \v 4 Ndipo Eliezara wansembe atengeko ena mwa magazi a ngʼombeyo ndi chala chake ndi kuwaza kasanu nʼkawiri ku tsogolo kwa tenti ya msonkhano. \v 5 Wansembeyo akuona, ngʼombeyo ayiwotche ­­chikopa chake, mnofu wake, magazi ake ndi zamʼkati zake. \v 6 Wansembe atenge mtengo wamkungudza, hisope ndi kansalu kofiira ndipo aponye zimenezo pakati pa moto umene akuwotchera ngʼombeyo. \v 7 Zitatha izi, wansembeyo ayenera kuchapa zovala zake ndiponso asambe ndi madzi. Iye angathe kupita ku msasa, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. \v 8 Munthu amene amawotcha ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. \p \v 9 “Munthu amene ndi woyeretsedwa achotse phulusa la ngʼombeyo ndi kuliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa msasa. Aisraeli adzasunge phulusalo kuti azikaligwiritsa ntchito polithira mʼmadzi woyeretsera ndi wochotsera tchimo. \v 10 Munthu wochotsa phulusa la ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo. \p \v 11 “Aliyense wokhudza mtembo wa munthu wina aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. \v 12 Adziyeretse yekha ndi madzi pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ndipo adzayeretsedwa. Koma ngati sadziyeretsa yekha pa tsiku la chitatu ndi lachisanu ndi chiwiri sadzakhala woyeretsedwa. \v 13 Aliyense amene akhudza mtembo wa munthu nʼkulephera kudziyeretsa yekha, ndiye kuti wadetsa Nyumba ya Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraeli. Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanamuwaze madzi oyeretsa; kudetsedwa kwake kukhalabe pa iyeyo. \p \v 14 “Pamene munthu wamwalira mu tenti, lamulo lomwe ligwire ntchito ndi ili: Aliyense wolowa mu tentimo ndi amene anali momwemo adzakhala odetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, \v 15 ndiponso chiwiya chilichonse chopanda chivundikiro chidzakhala chodetsedwa. \p \v 16 “Aliyense wokhudza munthu amene waphedwera kunja ndi lupanga kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe, kapena aliyense wokhudza fupa la munthu kapena manda, munthu ameneyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri. \p \v 17 “Za munthu wodetsedwayo: ikani phulusa lochokera ku nsembe ya chiyeretso mu mtsuko ndi kuthiramo madzi abwino. \v 18 Tsono munthu woyeretsedwa atenge hisope, amuviyike mʼmadzi ndi kuwaza tentiyo ndi zipangizo zonse, pamodzi ndi anthu anali mʼmenemo. Ayenera kuwazanso aliyense wakhudza fupa kapena, munthu wochita kuphedwa, kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe kapenanso amene wakhudza manda. \v 19 Munthu woyeretsedwa ndiye awaze munthu wodetsedwayo pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amuyeretse. Munthu amene akuyeretsedwayo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyeretsedwa. \v 20 Koma ngati munthu wodetsedwayo sadziyeretsa yekha, ndiye kuti ayenera kuchotsedwa pakati pa gulu chifukwa anadetsa malo wopatulika a Yehova, popeza sanawazidwe madzi oyeretsa ndiye kuti ndi wodetsedwa. \v 21 Ili ndi lamulo lokhazikika kwa iwo. \p “Munthu amene amawaza madzi oyeretsawo ayenera kuchapa zovala zake ndipo yense wokhudza madzi oyeretserawo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. \v 22 Chilichonse chimene munthu wodetsedwayo achikhudze chidzakhala chodetsedwa ndiponso aliyense wochikhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.” \c 20 \s1 Madzi Ochokera Mʼthanthwe \p \v 1 Pa mwezi woyamba gulu lonse la Aisraeli linafika ku chipululu cha Zini, ndipo anakhala ku Kadesi. Miriamu anafera kumeneko ndipo anayikidwa mʼmanda. \p \v 2 Kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa, choncho anthuwo anasonkhana motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. \v 3 Anakangana ndi Mose kuti, “Kunali bwino ifenso tikanangofa pamene abale athu anafa pamaso pa Yehova! \v 4 Chifukwa chiyani unabweretsa gulu la Yehova mʼchipululu muno, kuti ife ndi ziweto zathu tife kuno? \v 5 Nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto ndi kutibweretsa kumalo woyipa ano? Kuno kulibe tirigu kapena nkhuyu, mphesa kapena makangadza. Ndipo kuno kulibenso madzi akumwa!” \p \v 6 Mose ndi Aaroni anachoka mu msonkhano ndi kupita pa khomo la tenti ya msonkhano, nagwa pansi chafufumimba ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera. \v 7 Yehova anati kwa Mose, \v 8 “Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mʼbale wako Aaroni musonkhanitse anthu onse pamodzi. Uyankhule ndi thanthwe ilo iwo akuona ndipo lidzatulutsa madzi ake. Udzatulutsa madzi mʼthanthwe limeneli kuti anthu onse ndi ziweto zawo amwe.” \p \v 9 Choncho Mose anatenga ndodo pamaso pa Yehova monga momwe anamulamulira. \v 10 Mose ndi Aaroni anasonkhanitsa anthuwo pamodzi ku thanthwelo ndipo Mose anawawuza kuti, “Tamverani osamvera inu, kodi tikupatseni madzi kuchokera ku thanthwe ili?” \v 11 Choncho Mose anatukula dzanja lake ndi kumenya thanthwelo kawiri ndi ndodo yake ndipo madzi ambiri anatuluka mwamphamvu, ndipo anthu ndi ziweto zawo anamwa. \p \v 12 Koma Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Chifukwa chakuti simunandikhulupirire ndiponso simunandilemekeze monga Woyera pamaso pa Aisraeli, simudzalowetsa anthuwa mʼdziko limene ndikupereka kwa iwo.” \p \v 13 Awa anali madzi a ku Meriba, kumene Aisraeli anakangana ndi Yehova ndiponso kumene Yehovayo anadzionetsa yekha kuti ndi Woyera pakati pawo. \s1 Aedomu Akaniza Njira Aisraeli \p \v 14 Mose anatumiza amithenga kuchokera ku Kadesi kupita kwa mfumu ya ku Edomu, kukanena kuti, \pm “Mʼbale wako Israeli akunena izi: Inuyo mukudziwa za mavuto onse amene anatigwera. \v 15 Makolo athu anapita ku Igupto ndipo tinakhala kumeneko zaka zambiri. Aigupto anatizunza pamodzi ndi makolo athuwo, \v 16 koma titalirira Yehova, Iyeyo anamva kulira kwathuko ndipo anatitumizira mngelo amene anatitulutsa ku Igupto.” \pm “Taonani, tsopano tili pano pa Kadesi, mzinda wa mʼmalire a dziko lanu. \v 17 Chonde mutilole tidutse mʼdziko lanu. Sitidzera mʼminda yanu kapena mu mpesa wanu, kapenanso kumwa madzi mʼchitsime chilichonse. Tidzayenda kutsata msewu waukulu wa mfumu ndipo sitidzapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere mpaka titadutsa malire a dziko lanu.” \p \v 18 Koma Edomu anayankha kuti, \pm “Musadutse kuno: Mukangoyesera tidzabwera ndi kumenyana nanu ndi lupanga.” \p \v 19 Aisraeli anayankha kuti, \pm “Tidzayenda motsata msewu waukulu. Ndipo ngati ife kapena ziweto zathu tidzamwa madzi anu tidzalipira. Tikungofuna tidutse nawo, palibenso china.” \p \v 20 Koma Edomu anayankhanso kuti, \pm “Musadutse.” \p Kenaka Edomu anatuluka ndi gulu lankhondo lalikulu komanso lamphamvu. \v 21 Edomu anakaniza Israeli kuti adutse mʼdziko lake, choncho Israeli anabwerera. \s1 Aaroni Amwalira \p \v 22 Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Kadesi ndipo linafika ku phiri la Hori. \v 23 Ali pa phiri la Hori, pafupi ndi malire a Edomu, Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, \v 24 “Aaroni adzakakhala ndi anthu a mtundu wake, sadzalowa mʼdziko limene ndapereka kwa Aisraeli, chifukwa nonse munandiwukira motsutsana ndi malamulo anga ku madzi a ku Meriba. \v 25 Tenga Aaroni ndi mwana wake wamwamuna Eliezara ndipo ukwere nawo ku phiri la Hori. \v 26 Uvule Aaroni zovala zake ndipo umuveke mwana wake Eliezara, pakuti Aaroni adzafera komweko, ndipo adzakakhala ndi anthu a mtundu wake.” \p \v 27 Mose anachita monga Yehova anamulamulira: Anapita ku phiri la Hori gulu lonse likuona. \v 28 Pamenepo Mose anavula Aaroni zovala zake ndi kuveka mwana wake Eliezara. Aaroni anafa kumeneko pamwamba pa phirilo. Koma Mose ndi Eliezara anatsika ku phiriko, \v 29 ndipo pamene anthu onse anamva kuti Aaroni wafa, nyumba yonse ya Israeli inamulira Aaroniyo masiku makumi atatu. \c 21 \s1 Kuwonongedwa kwa Aradi \p \v 1 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi, imene inkakhala ku Negevi, itamva kuti Aisraeli akubwera kudzera msewu wopita ku Atarimu, inachita nkhondo ndi Aisraeli nigwira ena mwa iwo. \v 2 Ndipo Israeli anachita lonjezo ili kwa Yehova: “Mukapereka anthu awa mʼdzanja lathu ife tidzawonongeratu mizinda yawo.” \v 3 Yehova anamva pempho la Aisraeli ndipo anapereka Akanaaniwo kwa iwo. Anawawononga pamodzi ndi mizinda yawo. Kotero malowo anatchedwa Horima. \s1 Njoka Yamkuwa \p \v 4 Aisraeli anayenda kuchokera ku phiri la Hori kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira kuzungulira dziko la Edomu. Koma anthu anataya mtima mʼnjiramo \v 5 ndipo anayankhula motsutsana ndi Mulungu ndi Mose, nati, “Chifukwa chiyani munatitulutsa kuchoka mʼdziko la Igupto kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya, kulibe madzi ndipo chakudya cha chabechabechi tatopa nacho.” \p \v 6 Choncho Yehova anatumiza njoka zaululu pakati pawo. Zinaluma anthu ndipo Aisraeli ambiri anafa. \v 7 Anthuwo anabwera kwa Mose ndi kunena kuti, “Tachimwa chifukwa tayankhula motsutsana ndi Yehova komanso inu. Pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Tsono Mose anapempherera anthuwo. \p \v 8 Yehova anati kwa Mose, “Upange njoka yaululu ndipo uyipachike pa mtengo. Aliyense amene walumidwa akangoyangʼana njokayo adzakhala ndi moyo.” \v 9 Pamenepo Mose anapanga njoka yamkuwa ndi kuyipachika pa mtengo. Ndipo aliyense wolumidwa akayangʼana njoka yamkuwayo ankakhala ndi moyo. \s1 Ulendo wa ku Mowabu \p \v 10 Aisraeli anayendabe nakamanga misasa yawo ku Oboti. \v 11 Kenaka anasamuka ku Oboti nakamanga misasa yawo ku Iye-Abarimu, mʼchipululu chimene chili kummawa kwa Mowabu, kotulukira dzuwa. \v 12 Kuchoka kumeneko anayendabe nakamanga misasa yawo mʼchigwa cha Zeredi. \v 13 Anasamukanso kumeneko nakamanga moyandikana ndi Arinoni mʼdera limene lili mʼchipululu chimene chimafika mʼdziko la Aamori. Arinoni ndiwo malire a Mowabu ndi Aamori. \v 14 Nʼchifukwa chake Buku la Nkhondo za Yehova limati, \q1 “Mzinda wa Wahebu uli mu Sufa, \q2 mu zigwa za Arinoni, \v 15 ku matsitso a zigwa \q1 amene afika mpaka ku Ari \q2 nakhudza malire a dziko la Mowabu.” \m \v 16 Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Beeri, pa chitsime chomwe Yehova anawuza Mose kuti, “Sonkhanitsa anthu pamodzi ndipo ndidzawapatsa madzi.” \p \v 17 Pamenepo Aisraeli anayimba nyimbo iyi: \q1 “Tulutsa madzi, chitsime iwe! \q2 Chiyimbireni nyimbo, \q1 \v 18 chitsime chomwe anakumba mafumu, \q2 chomwe anakumba anthu omveka, \q2 ndi ndodo zawo zaufumu ndi ndodo zawo zoyendera.” \m Kenaka anachoka ku chipululu ndi kupita ku Matana. \v 19 Kuchoka ku Matana anapita ku Nahalieli, kuchoka ku Nahalieli anapita ku Bamoti, \v 20 ndipo atachoka ku Bamoti anapita ku chigwa cha dziko la Mowabu kudzera njira ya pamwamba pa phiri la Pisiga, moyangʼanana ndi Yesimoni. \s1 Kugonjetsedwa kwa Sihoni ndi Ogi \p \v 21 Aisraeli anatumiza amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, kuti, \pm \v 22 “Tiloleni kuti tidutse mʼdziko mwanu. Sitidzapatukira mʼminda mwanu kapena mu mpesa wanu kapena kumwa madzi mʼchitsime chili chonse. Tidzayenda mu msewu waukulu wa mfumu mpaka titadutsa malire a dziko lanu.” \p \v 23 Koma Sihoni sanalole kuti Aisraeli adutse mʼdziko mwake. Iye anasonkhanitsa pamodzi ankhondo ake onse kuti akamenyane ndi Aisraeli mʼchipululu. Atafika pa Yahazi anamenyana ndi Aisraeli. \v 24 Koma Aisraeli anamupha ndi kulanda dziko lake kuchokera ku Arinoni mpaka ku Yaboki, kulekezera mʼmalire a dziko la Aamoni, chifukwa malire a dziko la Aamoni anali otetezedwa. \v 25 Ndipo Aisraeli analanda mizinda yonse ya Aamori, nakhalamo kuphatikizapo Hesiboni ndi midzi yake yozungulira. \v 26 Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, yemwe anamenyana ndi mfumu yakale ya dziko la Mowabu. Lonselo linakhala dziko lake mpaka ku Arinoni. \p \v 27 Nʼchifukwa chake alakatuli amati: \q1 “Bwerani ku Hesiboni, mzindawo umangidwenso; \q2 mzinda wa Sihoni ukhazikike. \b \q1 \v 28 “Moto unabuka ku Hesiboni, \q2 malawi a moto kuchokera mu mzinda wa Sihoni. \q1 Unanyeketsa Ari mzinda wa ku Mowabu, \q2 nzika za ku malo okwera a Arinoni. \q1 \v 29 Tsoka kwa iwe Mowabu! \q2 Mwawonongedwa inu anthu a ku Kemosi! \q1 Ana ake aamuna wawasandutsa ngati anthu othawathawa \q2 ndipo ana ake aakazi ngati akapolo, \q2 akapolo a Sihoni, mfumu ya Aamori. \b \q1 \v 30 “Koma ife tawagonjetsa; \q2 Hesiboni wawonongedwa mʼnjira monse mpaka kufika ku Diboni. \q1 Tawaphwasula mpaka ku mzinda wa Nofa, \q2 mzinda womwe umafika ku Medeba. \p \v 31 “Choncho Aisraeli anakhala mʼdziko la Aamori.” \p \v 32 Mose atatumiza azondi ku Yazeri, Aisraeliwo analanda midzi yozungulira ndi kuthamangitsa Aamori omwe ankakhala kumeneko. \v 33 Kenaka anabwerera, nadzera njira ya ku Basani. Choncho Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anatuluka kukakumana nawo ndipo anamenyana nawo ku Ederi. \p \v 34 Yehova anati kwa Mose, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.” \p \v 35 Choncho Aisraeli anapha Ogi pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse la nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala wamoyo, ndipo analanda dziko lakelo. \c 22 \s1 Balaki Ayitana Balaamu \p \v 1 Aisraeli anayenda kupita ku zigwa za Mowabu nakamanga misasa yawo tsidya lina la Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko. \p \v 2 Tsono Balaki mwana wa Zipori anaona zonse zimene Aisraeli anachitira Aamori, \v 3 ndipo Amowabu anaopa anthuwo chifukwa analipo ambiri. Amowabuwo anachita mantha kwambiri mpaka ananjenjemera chifukwa cha Aisraeli. \p \v 4 Iwo anati kwa akuluakulu a ku Midiyani, “Gulu ili lidzabudula zonse zimene zatizungulira monga momwe ngʼombe yothena imathera udzu wa ku tchire.” \p Tsono Balaki mwana wa Zipori, yemwe anali mfumu ya Mowabu pa nthawi imeneyo, \v 5 anatumiza amithenga kwa Balaamu mwana wa Beori, yemwe anali ku Petori, pafupi ndi mtsinje, mʼdziko la kwawo kuti akamuyitane. Balaki anati: \pm “Taonani, anthu ochokera ku Igupto abwera, adzaza dziko lonse ndipo akufuna kuchita nane nkhondo. \v 6 Tsopano bwera, utemberere anthu amenewa chifukwa ndi amphamvu kwambiri kuposa ine. Mwina ndingadzawagonjetse ndi kuwatulutsira kunja kwa dzikoli chifukwa ndikudziwa kuti amene umawadalitsa amadalitsika, ndipo amene umawatemberera amatembereredwa.” \p \v 7 Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena. \p \v 8 Balaamu anawawuza kuti, “Mugone konkuno usiku uno, ndipo ndikuyankhani zomwe Yehova andiwuze.” Choncho akuluakulu a Amowabu anagona kwa Balaamu. \p \v 9 Mulungu anabwera kwa Balaamu namufunsa kuti, “Kodi anthu ali ndi iwewa ndani?” \p \v 10 Balaamu anayankha Mulungu kuti, “Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, ananditumizira uthenga uwu: \v 11 ‘Taonani, anthu amene achokera ku dziko la Igupto adzaza dziko lonse. Tsopano bwera udzawatemberere mʼmalo mwanga. Mwina ndidzatha kumenyana nawo ndi kuwatulutsa.’ ” \p \v 12 Koma Mulungu anawuza Balaamu kuti, “Usapite nawo. Usawatemberere anthu amenewo chifukwa ndi odalitsika.” \p \v 13 Mmawa mwake Balaamu anadzuka ndi kuwuza akuluakulu a Balaki aja kuti, “Bwererani ku dziko la kwanu chifukwa Yehova sanandilole kuti ndipite nanu.” \p \v 14 Kotero akuluakulu a Mowabu anabwerera kwa Balaki ndi kukanena kuti, “Balaamu wakana kubwera nafe.” \p \v 15 Kenaka Balaki anatumanso akuluakulu ena ambiri ndi olemekezeka kwambiri kuposa oyamba aja ndipo \v 16 anafika kwa Balaamu nati; \pm “Zomwe Balaki mwana wa Zipori akunena ndi izi: ‘Usalole kuti china chilichonse chikulepheretse kubwera kwa ine, \v 17 chifukwa ndidzakulipira bwino kwambiri ndipo ndidzakuchitira chilichonse chimene unganene. Bwera ndipo uwatemberere anthu amenewa mʼmalo mwanga.’ ” \p \v 18 Koma Balaamu anayankha atumiki a Balaki kuti, “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingachite chilichonse chachikulu kapena chachingʼono kuposa kuchita lamulo la Yehova Mulungu wanga. \v 19 Tsopano mukhale kuno usiku uno monga ena anachitira, ndidzaona chimene Yehova adzandiwuza.” \p \v 20 Usiku umenewo Mulungu anabwera kwa Balaamu ndipo anati, “Popeza anthu awa abwera kudzakuyitana, nyamuka, pita nawo koma ukachite zokhazo zimene ndikuwuze.” \s1 Bulu Ayankhula \p \v 21 Balaamu anadzuka mmawa, namanga bulu wake wamkazi ndipo anapita ndi akuluakulu a Mowabu. \v 22 Koma Mulungu anakwiya kwambiri pamene ankapita ndipo mngelo wa Yehova anayima pa njira kutsutsana naye. Balaamu anakwera bulu wake wamkazi ndipo antchito ake awiri anali naye. \v 23 Pamene buluyo anaona mngelo wa Yehova atayima pa njira ndi lupanga mʼmanja mwake, anapatukira kumbali kwa msewu napita kutchire. Balaamu anamumenya kuti abwerere mu msewu. \p \v 24 Kenaka mngelo wa Yehova anayima mʼkanjira kakangʼono pakati pa minda iwiri ya mpesa yokhala ndi makoma mbali zonse \v 25 Bulu uja ataona mngelo wa Yehova anadzipanikiza ku khoma, kukhukhuza phazi la Balaamu kukhomako. Ndipo pomwepo Balaamu anamenya buluyo kachiwiri. \p \v 26 Kenaka mngelo wa Yehova anapita patsogolo ndi kuyima pamalo opanikizika pomwe panalibe poti nʼkutembenukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere. \v 27 Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anagona pansi Balaamu ali pa msana, ndipo iye anakwiya ndi kumumenya ndi ndodo yake. \v 28 Pamenepo Yehova anayankhulitsa bulu uja, ndipo buluyo anati kwa Balaamu, “Ndakuchitirani chiyani kuti mundimenye katatuka?” \p \v 29 Balaamu anati kwa buluyo, “Wandipusitsa, ndikanakhala ndi lupanga mʼmanja mwanga, ndikanakupha pomwe pano.” \p \v 30 Buluyo anati kwa Balaamu, “Kodi sindine bulu wanu, amene mumakwera nthawi zonse kufikira lero? Kodi ndinakuchitiranipo zoterezi?” \p Iye anati “Ayi.” \p \v 31 Pomwepo Yehova anatsekula maso Balaamu ndipo anaona mngelo wa Yehovayo ali chiyimire pa njira ndi lupanga losolola. Tsono iye anawerama nalambira pamaso pake. \p \v 32 Mngelo wa Yehova anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako katatu? Taona, Ine ndabwera kudzakutsutsa chifukwa ulendo wakowu ndi woyipa pamaso panga. \v 33 Buluyu anandiona ndi kupatuka katatu aka. Akanakhala kuti sanapatuke, ndikanakupha tsopano, koma buluyu nʼkanamusiya ndi moyo.” \p \v 34 Balaamu anati kwa mngelo wa Yehova uja, “Ndachimwa. Sindinadziwe kuti munayima pa njira kunditsutsa. Tsopano ngati Inu simunakondwe, ineyo ndibwerera.” \p \v 35 Mngelo wa Yehova anati kwa Balaamu, “Pita ndi anthuwa koma ukayankhule zokhazo zimene ndikakuwuze.” Choncho Balaamu anapita ndi akuluakulu a Balaki. \p \v 36 Balaki atamva kuti Balaamu akubwera, anapita kukakumana naye ku mzinda wa Mowabu umene unali mʼmalire a Arinoni, mʼmphepete mwa dziko lake. \v 37 Balaki anati kwa Balaamu, “Kodi sindinakutumizire uthenga woti ubwere msanga? Chifukwa chiyani sunabwere kwa ine? Kodi sindingathe kukulipira mokwanira?” \p \v 38 Balaamu anayankha Balaki kuti, “Taonani, ndabwera kwa inu lero, kodi ine ndili ndi mphamvu zoti nʼkuyankhula chilichonse? Inetu ndiyenera kuyankhula zokhazo zimene Mulungu wandiwuza.” \p \v 39 Pamenepo Balaamu anapita pamodzi ndi Balaki ku Kiriati-Huzoti. \v 40 Balaki anapereka nsembe ngʼombe ndi nkhosa, ndipo anapereka zina kwa Balaamu ndi kwa akuluakulu omwe anali naye. \v 41 Mmawa mwake Balaki anatenga Balaamu napita limodzi ku Bamoti Baala, ndipo kumeneko anakaonako gulu lina la Aisraeliwo. \c 23 \s1 Uthenga Woyamba wa Balaamu \p \v 1 Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano, ndipo mukonzenso ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” \v 2 Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo awiriwo anapereka ngʼombe imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse. \p \v 3 Kenaka Balaamu anati kwa Balaki, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu ineyo ndipite pambali. Mwina Yehova adzabwera kuti akumane nane. Chilichonse chimene akandionetse ndidzakuwuzani” Choncho anapita ku malo okwera a chipululu. \p \v 4 Mulungu anakumana naye ndipo Balaamu anati, “Ndakonza maguwa asanu ndi awiri ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo nsembe ya ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzinso.” \p \v 5 Yehova anawuza Balaamu kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.” \p \v 6 Ndipo anabwerera kwa iye namupeza atayima pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu onse a Mowabu. \v 7 Ndipo Balaamu ananena uthenga wake: \q1 “Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu, \q2 mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa. \q1 Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga, \q2 pita nyoza Israeli.’ \q1 \v 8 Ndingatemberere bwanji \q2 amene Mulungu sanawatemberere? \q1 Ndinganyoze bwanji \q2 amene Yehova sanawanyoze? \q1 \v 9 Kuchokera pamwamba pa mapiri ndikuona anthu, \q2 ndikuwaona kuchokera pa zitunda. \q1 Ndikuona anthu okhala pawokha, \q2 osakhala mʼgulu limodzi ndi mitundu ina. \q1 \v 10 Ndani angawerenge zidzukulu za Yakobo zochuluka ngati fumbi, \q2 kapena chimodzi mwa zigawo zinayi za Israeli? \q1 Lekeni ndife imfa ya oyera mtima, \q2 ndi chimaliziro changa chikhale ngati chawo!” \p \v 11 Balaki anati kwa Balaamu, “Wandichitira chiyani? Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, ndipo taona, sunachite chilichonse koma kuwadalitsa!” \p \v 12 Iye anayankha kuti, “Kodi sindinayenera kuyankhula zimene Yehova anandiwuza?” \s1 Uthenga Wachiwiri wa Balaamu \p \v 13 Kenaka Balaki anawuza Balaamu kuti, “Tiye tipite limodzi ku malo ena komwe ungawaone. Udzangoona gulu limodzi osati onsewo. Ndipo pamenepo, ukawatemberere mʼmalo mwanga.” \v 14 Tsono anamutengera ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo kumeneko anamanga maguwa ansembe asanu ndi awiri ndipo anapereka nsembe ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse. \p \v 15 Balaamu anawuza Balaki kuti, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu pamene ine ndikukakumana ndi Mulungu cha uko.” \p \v 16 Yehova anakumana ndi Balaamu ndipo anamuyankhula kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.” \p \v 17 Ndipo anapita kwa iye ndipo anamupeza atayimirira pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu a ku Mowabu. Balaki anafunsa Balaamu kuti, “Yehova wayankhula chiyani?” \p \v 18 Pamenepo Balaamu ananena uthenga wake: \q1 “Nyamuka Balaki ndipo tamvera; \q2 Undimvere iwe mwana wa Zipori. \q1 \v 19 Mulungu si munthu kuti aname, \q2 kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake. \q1 Kodi amayankhula koma osachita? \q2 Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa? \q1 \v 20 Wandilamula kuti ndidalitse, \q2 Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe. \b \q1 \v 21 “Palibe kuwukira kulikonse kumene wakuona mwa Yakobo, \q2 sanaone chovuta mu Israeli. \q1 Yehova Mulungu wawo ali nawo: \q2 mfuwu wa mfumu uli pakati pawo. \q1 \v 22 Mulungu wowatulutsa mʼdziko la Igupto, \q2 ali ndi mphamvu ngati za njati. \q1 \v 23 Palibe matsenga amene angalimbane ndi Yakobo, \q2 palibe mawula amene angalimbane ndi Israeli. \q1 Tsopano za Yakobo ndi Israeli adzanena kuti, \q2 ‘Onani zimene Mulungu wachita!’ \q1 \v 24 Taonani, anthu anyamuka ngati mkango waukazi; \q2 adzuka okha ngati mkango waumuna \q1 umene supuma mpaka utadya nyama imene wagwira \q2 ndi kumwa magazi a nyama yogwidwayo.” \p \v 25 Ndipo Balaki anati kwa Balaamu, “Usawatemberere ndi pangʼono pomwe kapena kuwadalitsa! \p \v 26 “Balaamu anayankha Balaki kuti, ‘Kodi sindinakuwuzeni kuti ndiyenera kuchita zimene Yehova wanena?’ ” \s1 Uthenga Wachitatu wa Balaamu \p \v 27 Kenaka Balaki anati kwa Balaamu, “Bwera ndikutengere ku malo ena. Mwina chidzamukondweretsa Mulungu kuti uwatemberere kumeneko mʼmalo mwanga.” \v 28 Ndipo Balaki anamutengera Balaamu pamwamba pa Peori, poyangʼanana ndi chipululu. \p \v 29 Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano ndipo mundikonzere ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” \v 30 Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo anapereka nsembe ngʼombe imodzi yayimuna ndi nkhosa imodzi yayimuna pa guwa lililonse. \c 24 \p \v 1 Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu. \v 2 Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye \v 3 ndipo ananena uthenga wake: \q1 “Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori, \q2 uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka, \q1 \v 4 uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu, \q2 yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse, \q2 yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere: \b \q1 \v 5 “Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo, \q2 misasa yako, iwe Israeli! \b \q1 \v 6 “Monga zigwa zotambalala, \q2 monga minda mʼmbali mwa mtsinje, \q1 monga aloe wodzalidwa ndi Yehova, \q2 monga mikungudza mʼmbali mwa madzi. \q1 \v 7 Madzi adzayenderera mʼmitsuko yake; \q2 mbewu zake zidzakhala ndi madzi ambiri. \b \q1 “Mfumu yake idzakhala yamphamvu kuposa Agagi; \q2 ufumu wake udzakwezedwa. \b \q1 \v 8 “Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto \q2 ali ndi mphamvu ngati za njati. \q1 Amawononga mitundu yomuwukira \q2 ndi kuphwanya mafupa awo, \q2 amalasa ndi mivi yake. \q1 \v 9 Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi, \q2 monga mkango waukazi, adzamuputa ndani? \b \q1 “Amene adalitsa iwe, adalitsike \q2 ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!” \p \v 10 Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka. \v 11 Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.” \p \v 12 Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine, \v 13 kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena? \v 14 Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.” \s1 Uthenga Wachinayi wa Balaamu \p \v 15 Ndipo iye ananena uthenga wake nati, \q1 “Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori, \q2 uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka. \q1 \v 16 Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu, \q2 amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba, \q1 amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse, \q2 amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka: \b \q1 \v 17 “Ndikumuona iye koma osati tsopano; \q2 ndikumupenya iye koma osati pafupi. \q1 Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo; \q2 ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli. \q1 Iye adzagonjetsa Mowabu \q2 ndi kugonjetsa ana onse a Seti. \q1 \v 18 Edomu adzagonjetsedwa; \q2 Seiri, mdani wake, adzawonongedwa \q2 koma mphamvu za Israeli zidzachuluka. \q1 \v 19 Wolamulira adzachokera mwa Yakobo \q2 ndipo adzawononga otsala a mu mzindamo.” \s1 Uthenga Wachisanu wa Balaamu \p \v 20 Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu: \q1 “Aamaleki anali oyamba mwa mitundu ya anthu \q2 koma potsiriza pake adzawonongeka.” \s1 Uthenga Wachisanu ndi Chimodzi wa Balaamu \p \v 21 Kenaka anaonanso Akeni ndipo ananena uthenga wake, \q1 “Malo amene mukukhalamo ndi otetezedwa, \q2 chisa chanu chinayikidwa pa thanthwe; \q1 \v 22 komabe inu Akeni mudzawonongedwa, \q2 pamene Asuri adzakutengeni ukapolo.” \s1 Uthenga Wachisanu ndi Chiwiri wa Balaamu \p \v 23 Ndipo ananenanso uthenga wina kuti, \q1 “Aa, ndani adzakhala ndi moyo Mulungu akachita zimenezi? \q2 \v 24 Sitima zapamadzi zidzabwera kuchokera ku madooko a Kitimu; \q1 kupondereza Asuri ndi Eberi, \q2 koma iwonso adzawonongeka.” \p \v 25 Pamenepo Balaamu ananyamuka ndi kubwerera kwawo ndipo Balaki anapitanso njira yake. \c 25 \s1 Aisraeli Achita Chigololo \p \v 1 Aisraeli akukhala ku Sitimu, anayamba kuchita chigololo ndi akazi a ku Mowabu, \v 2 amene ankawayitana ku nsembe za milungu yawo. Anthuwo anadya chakudya chopereka kwa milungu ndi kupembedza milunguyo. \v 3 Motero Aisraeli anapembedza nawo Baala-Peori ndipo Yehova anawapsera mtima kwambiri. \p \v 4 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga atsogoleri onse a anthu awa, uwaphe poyera, pamaso pa Yehova kuti mkwiyo waukulu wa Yehova uchoke pa Israeli.” \p \v 5 Choncho Mose anawuza oweruza a Israeli kuti, “Aliyense wa inu ayenera kupha anthu ake amene anapembedza nawo Baala-Peori.” \p \v 6 Kenaka mwamuna wina wa ku Israeli anabweretsa ku banja lake mkazi wa Chimidiyani pamaso pa Mose ndi anthu onse a Israeli pamene ankalira pa khomo la tenti ya msonkhano. \v 7 Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni ataona izi, anachoka pa msonkhanowo, natenga mkondo mʼdzanja lake. \v 8 Ndipo anatsatira Mwisraeliyu mpaka mʼtenti yake. Anasolola mkondowo ndi kubaya awiriwo kupyola Mwisraeliyo mpaka mʼthupi la mkaziyo. Pamenepo mliri unaleka pakati pa Aisraeli. \v 9 Pa mliriwo, anthu okwana 24,000 anafa. \p \v 10 Yehova anawuza Mose kuti, \v 11 “Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni wabweza mkwiyo wanga pa Aisraeli chifukwa sanalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine ndekha. Nʼchifukwa chake sindinawawononge mu mkwiyo wanga. \v 12 Tsono muwuze kuti ndikhazikitsa pangano langa la mtendere ndi iye. \v 13 Ndikupangana naye pangano la unsembe wosatha, iyeyo pamodzi ndi zidzukulu zake zonse, chifukwa sanalole kuti anthu awukire Ine Mulungu, ndipo anachita ntchito yopepesera machimo Aisraeli.” \p \v 14 Dzina la Mwisraeli yemwe anaphedwa ndi mkazi wa Chimidiyani anali Zimuri mwana wa Salu, mtsogoleri wa banja la Simeoni. \v 15 Ndipo dzina la mkazi wa Chimidiyani, yemwe anaphedwayo, linali Kozibi mwana wa Zuri, mtsogoleri wa fuko la ku Midiyaniko. \p \v 16 Yehova anawuza Mose kuti, \v 17 “Amidiyani ndi adani anu ndipo uwaphe, \v 18 chifukwa ankakuonani inu ngati adani awo pamene anakupusitsani pa nkhani ya ku Peori, ndiponso za mlongo wawo Kozibi, mwana wamkazi wa mtsogoleri wa Amidiyani, mkazi yemwe anaphedwa pamene mliri unabwera chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.” \c 26 \s1 Kalembera Wachiwiri \p \v 1 Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni, \v 2 “Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.” \v 3 Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti, \v 4 “Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” \b \p Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa: \b \m \v 5 Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi: \li1 kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki; \li1 kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu; \li1 \v 6 kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; \li1 kuchokera mwa Karimi, fuko la Akarimi. \m \v 7 Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730. \p \v 8 Mwana wa Palu anali Eliabu, \v 9 ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova. \v 10 Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo. \v 11 Koma ana a Kora sanafe nawo. \b \m \v 12 Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi: \li1 kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele; \li1 kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini; \li1 kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini; \li1 \v 13 kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera; \li1 kuchokera mwa Sauli, fuko la Asauli. \m \v 14 Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200. \b \m \v 15 Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi: \li1 kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni; \li1 kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi; \li1 kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni; \li1 \v 16 kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini; \li1 kuchokera mwa Eri, fuko la Aeri; \li1 \v 17 kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi; \li1 kuchokera mwa Arieli, fuko la a Areli. \m \v 18 Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500. \b \m \v 19 Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani. \m \v 20 Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi: \li1 kuchokera mwa Sela, fuko la Asera; \li1 kuchokera mwa Perezi, fuko la Aperezi; \li1 kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera. \li1 \v 21 Zidzukulu za Perezi zinali izi: \li2 kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; \li2 kuchokera mwa Hamuli, fuko la Ahamuli. \m \v 22 Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500. \b \m \v 23 Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi: \li1 kuchokera mwa Tola, fuko la Atola; \li1 kuchokera mwa Puwa, fuko la Apuwa; \li1 \v 24 kuchokera mwa Yasubu, fuko la Ayasubu. \li1 Kuchokera mwa Simironi, fuko la Asimironi. \m \v 25 Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300. \b \m \v 26 Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi: \li1 kuchokera mwa Seredi, fuko la Aseredi; \li1 kuchokera mwa Eloni, fuko la Aeloni; \li1 kuchokera mwa Yahaleeli, fuko la Ayahaleeli. \m \v 27 Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500. \b \m \v 28 Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi: \m \v 29 Zidzukulu za Manase: \li1 kuchokera mwa Makiri, fuko la Amakiri (Makiri anali abambo ake a Giliyadi); \li1 kuchokera mwa Giliyadi, fuko la Agiliyadi. \li1 \v 30 Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi; \li2 kuchokera mwa Iyezeri, fuko la Aiyezeri; \li2 kuchokera mwa Heleki, fuko la Aheleki; \li2 \v 31 kuchokera mwa Asirieli, fuko la Aasirieli; \li2 kuchokera mwa Sekemu, fuko la Asekemu; \li2 \v 32 kuchokera mwa Semida, fuko la Asemida; \li2 kuchokera mwa Heferi, fuko la Aheferi. \li2 \v 33 (Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.) \m \v 34 Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700. \m \v 35 Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi; \li1 kuchokera mwa Sutela, fuko la Asutela; \li1 kuchokera mwa Bekeri, fuko la Abekeri; \li1 kuchokera mwa Tahani, fuko la Atahani. \li1 \v 36 Zidzukulu za Sutela zinali izi: \li2 kuchokera mwa Erani, fuko la Aerani. \m \v 37 Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500. \m Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo. \b \m \v 38 Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi: \li1 kuchokera mwa Bela, fuko la Abela; \li1 kuchokera mwa Asibeli, fuko la Aasibeli; \li1 kuchokera mwa Ahiramu, fuko la Ahiramu; \li1 \v 39 kuchokera mwa Sufamu, fuko la Asufamu; \li1 kuchokera mwa Hufamu, fuko la Ahufamu; \li1 \v 40 Zidzukulu za Bela kupyolera mwa Aridi ndi Naamani zinali izi: \li2 kuchokera mwa Aridi, fuko la Aaridi; \li2 kuchokera mwa Naamani, fuko la Anaamani; \m \v 41 Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600. \b \m \v 42 Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi: \li1 kuchokera mwa Suhamu fuko la Asuhamu. \m Izi zinali zidzukulu za Dani. \v 43 Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400. \b \m \v 44 Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi: \li1 kuchokera mwa Imina, fuko la Aimuna; \li1 kuchokera mwa Isivi, fuko la Ayisivi; \li1 kuchokera mwa Beriya, fuko la Aberiya; \li1 \v 45 ndipo kupyolera mwa zidzukulu za Beriya: \li2 kuchokera mwa Heberi, fuko la Aheberi; \li2 kuchokera mwa Malikieli, fuko la Amalikieli; \li1 \v 46 (Aseri anali ndi mwana wamkazi dzina lake Sera) \m \v 47 Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400. \b \m \v 48 Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi: \li1 kuchokera mwa Yahazeeli, fuko la Ayahazeeli; \li1 kuchokera mwa Guni, fuko la Aguni; \li1 \v 49 kuchokera mwa Yezeri, fuko la Ayezeri; \li1 kuchokera mwa Silemu, fuko la Asilemu. \m \v 50 Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400. \b \m \v 51 Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730. \b \p \v 52 Yehova anawuza Mose kuti, \v 53 “Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo. \v 54 Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa. \v 55 Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo. \v 56 Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.” \b \m \v 57 Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa: \li1 kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni; \li1 kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati; \li1 kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari. \m \v 58 Awanso anali mabanja a Alevi: \li1 banja la Alibini, \li1 banja la Ahebroni, \li1 banja la Amali, \li1 banja la Amusi, fuko la Kora \li1 banja la Akohati, \li4 (Kohati anali abambo a Amramu. \v 59 Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo. \v 60 Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. \v 61 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo). \b \m \v 62 Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo. \b \p \v 63 Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko. \v 64 Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai; \v 65 Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni. \c 27 \s1 Ana Aakazi a Zelofehadi \p \v 1 Kenaka ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wamwamuna wa Manase, a mʼmabanja a Manase, mwana wa Yosefe anabwera. Mayina a ana aakaziwo anali awa: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Iwo anakayima \v 2 pa chipata cha tenti ya msonkhano pamaso pa Mose, wansembe Eliezara, atsogoleri ndi anthu onse, ndipo anati, \v 3 “Abambo athu anafera mʼchipululu koma sanali nawo mʼgulu la anthu otsatira Kora, omwe anasonkhana pamodzi kutsutsana ndi Yehova. Abambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo ndipo sanasiye ana aamuna. \v 4 Nʼchifukwa chiyani dzina la abambo athu lasowa pakati pa fuko lawo, kodi popeza analibe mwana wamwamuna? Tipatseni cholowa chathu pakati pa abale a abambo athu.” \p \v 5 Tsono Mose anabweretsa nkhani yawo pamaso pa Yehova \v 6 ndipo Yehova anati kwa iye, \v 7 “Zimene ana aakazi a Zelofehadi akunena ndi zoona. Uyenera kuwapatsadi cholowa chawo pakati pa abale a abambo awo ndipo uwapatse cholowa cha abambo awowo. \p \v 8 “Uza Aisraeli kuti, ‘Ngati munthu afa wosasiya mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi. \v 9 Ngati alibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chakecho kwa abale ake. \v 10 Ngati alibe abale muzipereka cholowa chake kwa abale a abambo ake. \v 11 Ngati abambo ake analibe mʼbale, muzipereka cholowa chakecho kwa mnansi wake wa mʼbanja lake kuti chikhale chake. Ili likhale lamulo kwa Aisraeli, monga momwe Yehova analamulira Mose.’ ” \s1 Yoswa Alowa Mʼmalo mwa Mose \p \v 12 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kwera phiri la Abarimu kuti ukaone dziko limene ndalipereka kwa Aisraeli. \v 13 Ukakaliona udzamwalira ngati Aaroni mʼbale wako, \v 14 chifukwa pamene anthu anawukira ku madzi a Meriba mʼchipululu cha Zini, inu nonse simunamvere lamulo londilemekeza Ine ngati Woyera pamaso pawo.” (Awa anali madzi a ku Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini). \p \v 15 Mose anati kwa Yehova, \v 16 “Ngati nʼkotheka Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, sankhani munthu woti ayangʼanire gulu ili kuti \v 17 alitsogolere potuluka ndi polowa, kuti anthu a Yehova asakhale ngati nkhosa zopanda mʼbusa.” \p \v 18 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene ali ndi mzimu wa utsogoleri, ndipo umusanjike dzanja lako. \v 19 Umuyimiritse pamaso pa wansembe Eliezara ndi pamaso pa gulu lonse ndipo umupatse mphamvu zolamulira, anthuwo akuona. \v 20 Umupatse gawo lina la ulemerero wako kuti Aisraeli onse azimumvera. \v 21 Ayime pamaso pa wansembe Eliezara, amene adzamudziwitse zimene Yehova akufuna pogwiritsa ntchito Urimu. Iye akalamula, Aisraeli onse azituluka ndipo akalamulanso, Aisraeliwo azibwereranso.” \p \v 22 Mose anachita monga Yehova anamulamulira. Anatenga Yoswa ndi kumuyimiritsa pamaso pa Eliezara wansembe ndi pamaso pa gulu lonse. \v 23 Ndipo anamusanjika manja ndi kumupatsa mphamvu, monga Yehova ananenera kudzera mwa Mose. \c 28 \s1 Zopereka za Tsiku ndi Tsiku \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Lamula Aisraeli kuti, ‘Onetsetsani kuti mukupereka kwa Ine pa nthawi yoyikika, chopereka cha chakudya chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Ine.’ \v 3 Awuze kuti, ‘Nsembe ya chakudya imene muzipereka pa moto kwa Yehova tsiku ndi tsiku ndi iyi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri, wopanda chilema. \v 4 Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo. \v 5 Muziperekanso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi. \v 6 Iyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku imene analamula pa phiri la Sinai kuti ikhale fungo lokoma, nsembe yopsereza pa moto yopereka kwa Yehova. \v 7 Chopereka chachakumwa chikhale lita imodzi yachakumwa chaukali pa nkhosa iliyonse. Muzithira pamalo opatulika, kupereka kwa Yehova. \v 8 Muzipereka mwana wankhosa winayo madzulo, pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa. Ichi ndi chopereka chachakudya, fungo lokoma kwa Yehova.’ ” \s1 Zopereka za pa Sabata \p \v 9 “ ‘Pa tsiku la Sabata, muzipereka nsembe ana ankhosa awiri a chaka chimodzi wopanda chilema, pamodzi ndi chopereka chachakumwa ndi chopereka chachakudya chokwana makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. \v 10 Iyi ndi nsembe yopsereza ya pa Sabata iliyonse, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake chachakumwa.’ ” \s1 Zopereka za pa Mwezi \p \v 11 “Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, onse wopanda chilema. \v 12 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; ndi nkhosa yayimuna, chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; \v 13 ndipo pa mwana wankhosa aliyense, chopereka cha ufa wa kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, izi ndi za nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto ya kwa Yehova. \v 14 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakumwa cha malita awiri a vinyo; ndipo pa nkhosa yayimuna, lita limodzi ndi theka, ndipo pa mwana wankhosa, lita limodzi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi yoperekedwa pa mwezi watsopano mʼkati mwa chaka. \v 15 Powonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake cha chakumwa, mbuzi yayimuna imodzi iperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopepesera machimo. \s1 Paska \p \v 16 “ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova. \v 17 Pa tsiku la 15 la mwezi womwewo pazikhala chikondwerero. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. \v 18 Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. \v 19 Koma muzipereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri aamuna a chaka chimodzi, onsewo wopanda chilema. \v 20 Pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; makilogalamu awiri pa nkhosa yayimuna iliyonse. \v 21 Kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa asanu ndi awiri aja. \v 22 Muziphatikizapo mbuzi yayimuna monga nsembe yopepesera machimo anu. \v 23 Muzikonza zimenezi nthawi zonse, powonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa. \v 24 Motere muzikonza chakudya cha nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pa masiku asanu ndi awiri ngati fungo lokomera Yehova. Zimenezi ziziperekedwa kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse pamodzi ndi nsembe yachakumwa. \v 25 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. \s1 Madyerero a Masabata \p \v 26 “ ‘Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Yehova, pa nthawi ya chikondwerero cha Masabata, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. \v 27 Muzipereka nsembe zopsereza za ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa imodzi yayimuna ndi ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi monga fungo lokomera Yehova. \v 28 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pazikhala chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri. \v 29 Ndipo pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja, kilogalamu imodzi. \v 30 Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu. \v 31 Muzipereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za zakumwa ndi nsembe yake ya chakudya. Onetsetsani kuti nyamazo zilibe chilema. \c 29 \s1 Chikondwerero cha Malipenga \p \v 1 “ ‘Pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Ili ndi tsiku limene muziliza malipenga. \v 2 Muzipereka mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi wopanda chilema monga nsembe zopsereza, fungo lokoma kwa Yehova. \v 3 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzipereka chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa yayimuna iliyonse muzipereka makilogalamu awiri. \v 4 Pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja muzipereka kilogalamu imodzi. \v 5 Muziperekanso mbuzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu. \v 6 Izi ndi zowonjezera pa nsembe zopsereza za mwezi ndi mwezi komanso za tsiku ndi tsiku pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi zopereka za chakumwa potsata malamulo ake. Izi ndi zopereka zotentha pa moto, zoperekedwa kwa Yehova, fungo lokoma. \s1 Tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo \p \v 7 “ ‘Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiriwu, muzichita msonkhano wopatulika. Muzisala zakudya ndipo musamagwire ntchito. \v 8 Muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokoma lokondweretsa Yehovayo; ngʼombe yayimuna imodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi. Zimenezi zizikhala zopanda chilema. \v 9 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri; \v 10 kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiriwo. \v 11 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe yopepesera machimo ya pa tsiku la mwambo ija, kuwonjezanso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi cha chakumwa. \s1 Chikondwerero cha Misasa \p \v 12 “ ‘Pa tsiku la mwezi wachisanu ndi chiwiri, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Muzichita madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri. \v 13 Muzipereka nsembe yotentha pa moto, kuti izikhala fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu, nkhosa zazimuna ziwiri, ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. \v 14 Pa mwana wangʼombe aliyense mwa ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu aja, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa iliyonse mwa nkhosa ziwiri zija, mukonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri. \v 15 Pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa aamuna khumi ndi anayiwo, muzipereka chakudya cha kilogalamu imodzi. \v 16 Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. \p \v 17 “ ‘Pa tsiku lachiwiri muzipereka ana angʼombe aamuna khumi ndi awiri aja, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi aja, zonse zopanda chilema. \v 18 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. \v 19 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. \p \v 20 “ ‘Pa tsiku lachitatu muzipereka ngʼombe zazimuna khumi ndi imodzi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. \v 21 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. \v 22 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. \p \v 23 “ ‘Pa tsiku lachinayi muzipereka ngʼombe zazimuna khumi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. \v 24 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. \v 25 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. \p \v 26 “ ‘Pa tsiku lachisanu muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zinayi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. \v 27 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. \v 28 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. \p \v 29 “ ‘Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zitatu, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. \v 30 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. \v 31 Muziperekenso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. \p \v 32 “ ‘Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa amuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. \v 33 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. \v 34 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. \p \v 35 “ ‘Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzichita msonkhano ndipo musamagwire ntchito iliyonse. \v 36 Muzipereka chopereka chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ngʼombe imodzi yayimuna, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa amuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. \v 37 Pamodzi ndi ngʼombe yayimunayo, nkhosa yayimunayo ndi ana ankhosawo, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. \v 38 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. \p \v 39 “ ‘Kuwonjezera pa zopereka zimene munalumbirira ndi pa zopereka zanu zaufulu, muzipereka zimenezi kwa Yehova pa masiku osankhika a chikondwerero chanu. Nsembe zanu zachakumwa ndi nsembe zanu zachiyanjano.’ ” \p \v 40 Mose anawuza Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamulira. \c 30 \s1 Za Kulumbira \p \v 1 Mose anawuza Aisraeli onse zonse zimene Yehova anamulamula. Iye anati, “Zimene Yehova walamula ndi izi: \v 2 Munthu wamwamuna ngati walonjeza kwa Yehova kapena kulumbira kuti adzachita zimene walumbirazo, asaphwanye mawuwo koma ayenera kuchita chilichonse chimene wanena. \p \v 3 “Pamene munthu wamkazi amene akukhalabe mʼnyumba ya abambo ake alumbira kwa Yehova kuti adzachita zimene walonjeza pa ubwana wake, \v 4 abambo ake namva kulumbira kwakeko kapena kulonjeza kwake kuti adzachitadi, ndipo abambo akewo wosayankhula kanthu, mkaziyo achitedi zomwe analumbirazo. Ayenera kudzachita zonse zimene walonjeza zija. \v 5 Koma ngati abambo akewo amva kulumbira kwake ndi kumukaniza, palibe lamulo lomukakamiza mkaziyo kuchita zimene walonjeza. Yehova adzamukhululukira chifukwa abambo ake anamukaniza. \p \v 6 “Ngati akwatiwa atalumbira kale kapena ngati alonjeza mofulumira ndi pakamwa pake, \v 7 mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma wosanenapo kanthu, mkaziyo achitedi zomwe walumbirazo. Achite ndithu zomwe walonjeza zija. \v 8 Koma ngati mwamuna wake amuletsa atamva kulumbira kwakeko, pamenepo amumasula mayiyo ku zimene analumbira komanso ku zimene analonjeza mosaganiza bwinozo ndipo Yehova adzamukhululukira. \p \v 9 “Mayi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi. \p \v 10 “Koma ngati mayi wokwatiwa alumbira nalonjeza kuti adzachitadi zimene walonjeza, \v 11 mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma osayankhulapo kanthu, osamuletsa, ayenera kuchitadi zonse zimene walumbira ndi zonse zimene walonjeza. \v 12 Koma ngati mwamuna wake amva ndi kumuletsa kuti asachite zomwe walumbirazo, palibe lamulo lomukakamiza mayiyo kuchita zomwe walumbirazo kapenanso zimene walonjeza. Popeza mwamuna wake wamuletsa, Yehova adzamukhululukira mayiyo. \v 13 Mwamuna wake ali ndi mphamvu zovomereza kapena kukana zimene mayiyo walumbira kapena zimene walonjeza zokhudza kudzilanga yekha. \v 14 Ndipo ngati mmawa mwake ndi masiku otsatira mwamuna wake sanenapo kanthu atamva zimenezi, mayiyo achitedi zimene walumbira kapena zimene walonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa sanamuwuze kanthu mayiyo pa tsiku limene anamva akulonjeza kapena kulumbira. \v 15 Koma ngati mwamunayo amukaniza patapita kanthawi atazimva kale, iyeyo ndiye wochimwa mʼmalo mwa mayiyo.” \p \v 16 Awa ndiwo malamulo amene Yehova analamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso abambo ndi mwana wawo wamkazi amene akanali mtsikana wokhalabe mʼnyumba ya abambo akewo. \c 31 \s1 Aisraeli Agonjetsa Amidiyani \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Uwabwezere zoyipa Amidiyani chifukwa cha zimene anachitira Aisraeli. Ukatha kuchita zimenezi, iwe udzamwalira.” \p \v 3 Ndipo Mose anati kwa Aisraeli, “Perekani zida kwa ena mwa anthu anu kuti akamenyane ndi Amidiyani ndi kuwabwezera choyipa mʼmalo mwa Yehova. \v 4 Mutumize ku nkhondoko amuna 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli.” \v 5 Choncho amuna okwana 12,000 anatenga zida kukonzekera nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli. \v 6 Mose anawatumiza ku nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse pamodzi ndi Finehasi mwana wa Eliezara wansembe amene ananyamula zipangizo zochokera ku malo wopatulika ndi malipenga okaliza. \p \v 7 Iwo anamenyana ndi Amidiyani monga momwe Yehova analamulira Mose ndipo anapha mwamuna aliyense. \v 8 Mwa anthu ophedwawo munali Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani. Ndipo anaphanso ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori. \v 9 Aisraeli anagwira ukapolo amayi a Chimidiyani ndi ana awo ndipo analandanso ngʼombe, ziweto zawo zina zonse ndi katundu wawo yense. \v 10 Anawotcha mizinda yonse imene Amidiyani ankakhalamo pamodzi ndi misasa yawo yonse. \v 11 Anatenga zonse zimene analanda ku nkhondoko, anthu ndi zoweta zomwe. \v 12 Ndipo anabwera nawo akapolowo ndi zolanda ku nkhondozo kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa gulu lonse la Aisraeli ku misasa yawo ku chigwa cha Mowabu, mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko. \p \v 13 Mose, wansembe Eliezara ndi atsogoleri onse a gululo anapita kukakumana nawo kunja kwa misasa. \v 14 Mose anakwiya nawo akuluakulu a magulu a ankhondowo: olamulira 1,000 ndi olamulira 100, amene ankachokera ku nkhondo. \p \v 15 Iye anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mwawaleka amoyo amayi onsewa?” \v 16 Paja iwo ndi amene ankatsatira uphungu wa Balaamu ndiponso ndi amene anachititsa Aisraeli kuti asiye Yehova pa zimene zinachitika ku Peori, kotero mliri unagwera anthu a Yehova. \v 17 Tsopano iphani munthu wamwamuna aliyense. Ndiponso iphani mayi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna, \v 18 koma sungani mtsikana aliyense amene sanagonepo ndi mwamuna. \p \v 19 “Inu nonse amene mwaphapo wina wake, kapena kukhudza aliyense amene anaphedwa mukhale kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachitatu mudziyeretse nokha pamodzi ndi akapolo anu. \v 20 Muyeretsenso zovala zanu ndi china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ubweya wa mbuzi kapenanso ndi mtengo.” \p \v 21 Tsono wansembe Eliezara anati kwa asilikali amene anapita ku nkhondo aja, “Lamulo limene Yehova anapereka kwa Mose ndi ili: \v 22 Golide, siliva, mkuwa, chitsulo, chiwaya, mtovu \v 23 ndi china chilichonse chimene sichingapse ndi moto muchidutsitse pa moto, ndipo chidzayeretsedwa. Komanso chiyeretsedwe ndi madzi oyeretsa. Ndipo chilichonse chimene chingapse ndi moto muchidutsitse mʼmadzimo. \v 24 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muchape zovala zanu ndipo mudzayera. Mukatero mutha kulowa mu msasa.” \s1 Kugawana Zolanda ku Nkhondo \p \v 25 Yehova anawuza Mose kuti, \v 26 “Iwe ndi wansembe Eliezara ndiponso akuluakulu a mabanja a anthuwa, muwerenge anthu onse ndi ziweto zomwe zinagwidwa ku nkhondo. \v 27 Mugawe zolanda ku nkhondozo magawo awiri, lina la ankhondo amene anapita ku nkhondo, lina la anthu onse. \v 28 Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Yehova, pa zofunkha 500 zilizonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, ngʼombe, bulu ndi nkhosa. \v 29 Utenge zimenezo pa theka la gawo la ankhondowo ndipo upereke kwa wansembe Eliezara kuti zikhale zopereka zanu kwa Yehova. \v 30 Kuchokera pa theka la gawo la Aisraeli, utengeko cholanda chimodzi pa makumi asanu aliwonse, pa anthu, ngʼombe, abulu, nkhosa, mbuzi kapena zoweta zina. Uzipereke kwa Alevi amene ntchito yawo ndi yosamalira tenti ya Yehova.” \v 31 Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara anachita monga Yehova analamulira Mose. \p \v 32 Zotsala pa zolanda ku nkhondo zimene ankhondowo anatenga zinali nkhosa 675,000, \v 33 Ngʼombe 72,000, \v 34 abulu 61,000, \v 35 ndi atsikana omwe sanagonepo ndi mwamuna 32,000. \p \v 36 Gawo la ankhondo amene anapita ku nkhondo linali: \b \li1 nkhosa 337,500, \v 37 mwa zimenezi gawo la Yehova linali 675; \li1 \v 38 ngʼombe zinalipo 36,000 ndipo gawo la Yehova linali 72; \li1 \v 39 abulu analipo 30,500 ndipo gawo la Yehova linali 61; \li1 \v 40 anthu analipo 16,000 ndipo gawo la Yehova linali 32. \b \p \v 41 Mose anapereka kwa wansembe Eliezara gawo limene linali loyenera kupereka kwa Yehova monga momwe Yehova analamulira Mose. \p \v 42 Pa gawo la Aisraeli, Mose anapatula theka limodzi kuchotsa pa zolanda ku nkhondo zonse zimene zinabwera ndi ankhondo aja. \v 43 Tsono gawo la Aisraeli linali ili: nkhosa 337,500, \v 44 ngʼombe 36,000, \v 45 abulu 30,500, \v 46 anthu 16,000. \v 47 Kuchoka pa gawo la Aisraelilo, Mose anatengapo chimodzi pa zolanda ku nkhondo makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo anazipereka kwa Alevi amene ankayangʼanira tenti ya Yehova monga Yehova analamulira Mose. \p \v 48 Pamenepo omwe ankayangʼanira magulu a ankhondo olamulira 1,000 ndi olamulira 100 anabwera kwa Mose, \v 49 iwo anati kwa iye, “Ife anthu anu tawerenga ankhondo amene timawalamulira. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene wasowa. \v 50 Ndipo tabweretsa zopereka kwa Yehova zimene munthu aliyense anapeza: ziwiya zagolide, zibangiri, zigwinjiri, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda kuti tichitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova.” \p \v 51 Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara analandira kuchokera kwa atsogoleriwo golide pamodzi ndi zipangizo zonse zosula. \v 52 Golide yense wochokera kwa atsogoleri a 1,000 ndi atsogoleri a 100 zomwe Mose ndi Eliezara anapereka ngati mphatso kwa Yehova zinali zolemera makilogalamu 200. \v 53 Wankhondo aliyense anatenga zomwe analanda yekha ku nkhondo. \v 54 Mose ndi Eliezara wansembe analandira golide kuchokera kwa atsogoleri a 1,000 ndi atsogoleri a 100 ndi kukamuyika mu tenti ya msonkhano ngati chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova. \c 32 \s1 Mafuko a ku Tsidya la Yorodani \p \v 1 Arubeni ndi Agadi amene anali ndi ngʼombe zambiri ndi ziweto zina anaona dziko la Yazeri ndi la Giliyadi kuti linali labwino kwa ziwetozo. \v 2 Choncho Arubeni ndi Agadi anapita kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa atsogoleri a anthu ndi kunena kuti, \v 3 “Ataroti, Diboni, Yazeri, Nimira, Hesiboni, Eleali, Sebamu, Nebo ndi Beoni, \v 4 dziko lomwe Yehova anagonjetsa pamaso pa Aisraeli, ndiwo malo woyenera ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto. \v 5 Iwo anati, ‘Ngati tapeza ufulu pamaso panu atumiki anufe, mutipatse dziko limeneli kuti likhale lathu. Tisawoloke nanu Yorodani.’ ” \p \v 6 Ndipo Mose anati kwa Agadi ndi Arubeni, “Kodi anthu a mtundu wanu apite ku nkhondo inu mutangokhala kuno? \v 7 Chifukwa chiyani mukufowoketsa Aisraeli kupita mʼdziko limene Yehova wawapatsa? \v 8 Izi ndi zimene makolo anu anachita pamene ndinawatuma kuchokera ku Kadesi kukaona dzikolo. \v 9 Atapita ku chigwa cha Esikolo, ndi kuliona dzikolo, anafowoketsa Aisraeli kuti asalowe mʼdziko limene Yehova anawapatsa. \v 10 Yehova anakwiya tsiku limenelo ndipo analumbira kuti, \v 11 ‘Chifukwa sananditsatire ndi mtima wonse, palibe ndi mmodzi yemwe mwa amuna a zaka makumi awiri kapena kuposa pamenepo, amene anachokera ku Igupto, amene adzaone dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo. \v 12 Palibe ndi mmodzi yemwe kupatula Kalebe mwana wa Yefune, Mkeni, ndi Yoswa mwana wa Nuni chifukwa anatsatira Yehova ndi mtima wonse.’ \v 13 Yehova anakwiyira Aisraeli kwambiri ndipo anawachititsa kuyenda mʼchipululu zaka makumi anayi, mpaka mʼbado wonse wa anthu amene anachita choyipa pamaso pake unatha. \p \v 14 “Ndipo onani tsopano, inu mʼbado wochimwa, mwalowa mʼmalo mwa makolo anu ndipo mwachititsa kuti Yehova akwiyire Israeli kwambiri. \v 15 Ngati muleka kumutsata, Iye adzawasiyiranso anthu onsewa mʼchipululu ndipo mudzawonongetsa anthu onsewa.” \p \v 16 Ndipo iwo anabwera kwa Mose namuwuza kuti, “Ife tikufuna kumanga makola a ziweto zathu kuno ndi mizinda yokhalamo akazi athu ndi ana athu. \v 17 Koma ndife okonzeka kutenga zida za nkhondo ndi kupita pamodzi ndi Aisraeli mpaka titakawafikitsa ku malo awo. Panopa, akazi ndi ana athu akhala mʼmizinda yotetezedwa, kuwateteza kwa anthu okhala mʼdzikoli. \v 18 Sitidzabwerera ku midzi yathu mpaka Mwisraeli aliyense atalandira cholowa chake. \v 19 Sitidzalandira cholowa chilichonse pamodzi nawo ku tsidya lina la Yorodani, chifukwa cholowa chathu tachipezera ku tsidya lino la kummawa kwa Yorodani.” \p \v 20 Tsono Mose anati kwa anthuwo, “Ngati inu mudzachita zimenezi, kutenga zida zankhondo pamaso pa Yehova kuti muchite nkhondo, \v 21 ndipo ngati nonsenu mudzapita ndi zida kuwoloka Yorodani pamaso pa Yehova mpaka atachotsa adani ake pamaso pake, \v 22 dzikolo nʼkugonja pamaso pa Yehova, mudzabwera ndi kukhala mfulu pamaso pa Yehova ndi Aisraeli. Ndipo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Yehova. \p \v 23 “Koma mukalephera kuchita izi, mudzakhala mukuchimwira Yehova. Ndipo dziwani kuti tchimo lanu lidzakupezani. \v 24 Amangireni akazi ndi ana anu mizinda, mangani makola a ziweto zanu, koma chitani zomwe mwalonjeza.” \p \v 25 Agadi ndi Arubeni anati kwa Mose, “Ife antchito anu tidzachita monga mbuye wathu mwalamulira. \v 26 Ana ndi akazi athu, ziweto zathu zina ndi ngʼombe zidzatsala kuno ku mizinda ya Giliyadi, \v 27 koma antchito anufe, mwamuna aliyense amene ali ndi chida cha nkhondo, adzawoloka kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova monga mbuye wathu wanenera.” \p \v 28 Choncho Mose anapereka malamulo awa kwa wansembe Eliezara, kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa akulu a mafuko a Aisraeli. \v 29 Mose anawawuza kuti, ngati Agadi ndi Arubeni, mwamuna aliyense wokonzekera nkhondo, awoloka Yorodani pamodzi ndi inu pamaso pa Yehova, ndipo dzikolo nʼkugonjetsedwa pamaso panu, mudzawapatse dziko la Giliyadi kukhala lawo. \v 30 Koma ngati sawoloka pamodzi nanu ndi zida zankhondo, ayenera kulandira cholowa chawo pamodzi ndi inu ku Kanaani. \p \v 31 Agadi ndi Arubeni anayankha kuti, “Antchito anu adzachita zimene Yehova wanena. \v 32 Tidzawoloka pamaso pa Yehova ndipo tidzalowa mu Kanaani ndi zida zankhondo, koma cholowa chathu chidzakhala ku tsidya lino la Yorodani.” \p \v 33 Choncho Mose anapatsa Agadi, Arubeni ndi theka la fuko la Manase mwana wa Yosefe dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi, mfumu ya ku Basani, dziko lonse, mizinda yake ndi midzi yowazungulira. \p \v 34 Agadi anamanga Diboni, Ataroti, Aroeri, \v 35 Atiroti-Sofani, Yazeri, Yogibeha, \v 36 Beti-Nimira ndi Beti-Harani mizinda ya malinga. Anamanganso makola a ziweto zawo. \v 37 Ndipo Arubeni anamanga Hesiboni, Eleali, Kiriataimu, \v 38 Nebo ndi Baala-Meoni (mayina awa anasinthidwa) ndi Sibima. Anapereka mayina ku mizinda ina yomwe anamangayo. \p \v 39 Zidzukulu za Makiri mwana wa Manase zinapita ku Giliyadi kulanda mzindawo ndi kuthamangitsira kunja Aamori omwe anali kumeneko. \v 40 Tsono Mose anapereka Giliyadi kwa Amakiri, ana a Manase, ndipo anakhala kumeneko. \v 41 Yairi, mwana wa Manase analanda midzi yambiri ya Giliyadi ndi kuyitcha kuti Havoti-Yairi. \v 42 Ndipo Noba analanda Kenati ndi midzi yozungulira ndi kuyitcha Noba, kutengera dzina la iye mwini. \c 33 \s1 Malo omwe Aisraeli Anayima pa Ulendo Wawo \p \v 1 Malo otsatirawa ndi omwe Aisraeli anayima pa maulendo awo atatuluka mʼdziko la Igupto mʼmagulu awo motsogozedwa ndi Mose ndi Aaroni. \v 2 Mose analemba malo amene anayambira maulendo awo molamulidwa ndi Yehova. Maulendo awo ndi malo omwe anayambira ndi awa: \b \pi1 \v 3 Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona, \v 4 pamene ankayika maliro a ana awo oyamba kubadwa, omwe Yehova anawakantha pakati pawo chifukwa Yehova anaweruza milungu yawo. \pi1 \v 5 Aisraeli atachoka ku Ramesesi, anamanga misasa yawo ku Sukoti. \pi1 \v 6 Atachoka ku Sukoti anakamanga misasa yawo ku Etamu, mʼmbali mwa chipululu. \pi1 \v 7 Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli. \pi1 \v 8 Atachoka ku Pihahiroti anadutsa mʼkati mwa nyanja kupita ku chipululu ndipo atayenda masiku atatu mʼchipululu cha Etamu, anamanga misasa yawo ku Mara. \pi1 \v 9 Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko. \pi1 \v 10 Atachoka ku Elimu anakamanga misasa yawo mʼmbali mwa Nyanja Yofiira. \pi1 \v 11 Atachoka ku Nyanja Yofiira anakamanga misasa yawo mʼchipululu cha Sini. \pi1 \v 12 Atachoka ku chipululu cha Sini anakamanga ku Dofika. \pi1 \v 13 Atachoka ku Dofika anakamanga misasa yawo ku Alusi. \pi1 \v 14 Atachoka ku Alusi anakamanga misasa yawo ku Refidimu, kumene kunalibe madzi woti anthu ndi kumwa. \pi1 \v 15 Atachoka ku Refidimu anakamanga ku chipululu cha Sinai \pi1 \v 16 Atachoka ku chipululu cha Sinai anakamanga misasa yawo ku Kiburoti-Hataava. \pi1 \v 17 Atachoka ku Kiburoti-Hataava anakamanga misasa yawo ku Heziroti. \pi1 \v 18 Atachoka ku Heziroti anakamanga ku Ritima. \pi1 \v 19 Atachoka ku Ritima anakamanga ku Rimoni-Perezi. \pi1 \v 20 Atachoka ku Rimoni-Perezi anakamanga ku Libina. \pi1 \v 21 Atachoka ku Libina anakamanga ku Risa. \pi1 \v 22 Atachoka ku Risa anakamanga ku Kehelata. \pi1 \v 23 Atachoka ku Kehelata anakamanga ku phiri la Seferi. \pi1 \v 24 Atachoka ku phiri la Seferi anakamanga ku Harada. \pi1 \v 25 Atachoka ku Harada anakamanga ku Mekheloti. \pi1 \v 26 Atachoka ku Mekheloti anakamanga ku Tahati. \pi1 \v 27 Atachoka ku Tahati anakamanga ku Tera. \pi1 \v 28 Atachoka ku Tera anakamanga ku Mitika. \pi1 \v 29 Atachoka ku Mitika anakamanga ku Hasimona. \pi1 \v 30 Atachoka ku Hasimona anakamanga ku Moseroti. \pi1 \v 31 Atachoka ku Moseroti anakamanga ku Beni Yaakani. \pi1 \v 32 Atachoka ku Beni Yaakani anakamanga ku Hori-Hagidigadi. \pi1 \v 33 Atachoka ku Hori-Hagidigadi anakamanga ku Yotibata. \pi1 \v 34 Atachoka ku Yotibata anakamanga ku Abirona. \pi1 \v 35 Atachoka ku Abirona anakamanga ku Ezioni-Geberi. \pi1 \v 36 Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi. \pi1 \v 37 Anachoka ku Kadesi ndi kukamanga ku phiri la Hori, mʼmalire mwa dziko la Edomu. \v 38 Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto. \v 39 Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123. \pi1 \v 40 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi yomwe inkakhala ku Negevi kummwera kwa Kanaani, inamva kuti Aisraeli akubwera. \pi1 \v 41 Atachoka ku phiri la Hori anakamanga ku Zalimoni. \pi1 \v 42 Atachoka ku Zalimoni anakamanga ku Punoni. \pi1 \v 43 Atachoka ku Punoni anakamanga ku Oboti. \pi1 \v 44 Atachoka ku Oboti anakamanga ku Iye-Abarimu. \pi1 \v 45 Atachoka ku Iye-Abarimu anakamanga ku Diboni Gadi. \pi1 \v 46 Atachoka ku Diboni Gadi anakamanga ku Alimoni-Dibulataimu. \pi1 \v 47 Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo. \pi1 \v 48 Atachoka ku mapiri a Abarimu anakamanga ku zigwa za Mowabu mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko. \v 49 Ali ku zigwa za Mowabu anamanga mʼmbali mwa Yorodani kuchokera ku Beti-Yesimoti mpaka ku Abeli-Sitimu. \b \p \v 50 Pa zigwa za Mowabu, mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti, \v 51 “Nena kwa Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mʼdziko la Kanaani, \v 52 mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo. \v 53 Mukalande dzikolo ndi kukhalamo chifukwa ndakupatsani dziko limenelo kuti mukhalemo. \v 54 Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu. \p \v 55 “ ‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo. \v 56 Ndipo pamenepo ndidzachitira inu zomwe ndinaganiza kuwachitira iwowo.’ ” \c 34 \s1 Malire a Dziko la Kanaani \p \v 1 Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa: \b \p \v 3 “ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere. \v 4 Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni, \v 5 kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu. \p \v 6 “ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo. \p \v 7 “ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori \v 8 ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi, \v 9 ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto. \p \v 10 “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu. \v 11 Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti. \v 12 Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere. \p “ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ” \b \p \v 13 Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka, \v 14 chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo. \v 15 Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.” \p \v 16 Yehova anawuza Mose kuti, \v 17 “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni. \v 18 Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo. \v 19 Mayina awo ndi awa: \b \li1 Kalebe mwana wa Yefune, \li2 wochokera ku fuko la Yuda, \li1 \v 20 Semueli mwana wa Amihudi, \li2 wochokera ku fuko la Simeoni; \li1 \v 21 Elidadi mwana wa Kisiloni, \li2 wochokera ku fuko la Benjamini; \li1 \v 22 Buki mwana wa Yogili, \li2 mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani; \li1 \v 23 Hanieli mwana wa Efodi, \li2 mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe; \li1 \v 24 Kemueli mwana wa Sifitani, \li2 mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe. \li1 \v 25 Elizafani mwana wa Parinaki, \li2 mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni; \li1 \v 26 Palitieli mwana wa Azani, \li2 mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara, \li1 \v 27 Ahihudi mwana wa Selomi, \li2 mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri; \li1 \v 28 Pedaheli mwana wa Amihudi, \li2 mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.” \p \v 29 Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani. \c 35 \s1 Midzi ya Alevi \p \v 1 Ku zigwa za Mowabu pafupi ndi Yorodani ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti, \v 2 “Lamula Aisraeli kuti apereke kwa Alevi midzi yoti azikhalamo kuchokera pa cholowa chomwe adzalandira. Muwapatsenso malo oweteramo ziweto kuzungulira midziyo. \v 3 Midziyo idzakhala yawo ndipo azidzakhala mʼmenemo. Malo a msipu adzakhala a ngʼombe, nkhosa ndi zoweta zawo zina zonse. \p \v 4 “Malo a msipu a mudziwo amene mudzawapatse Aleviwo, adzayambire ku khoma la mudzi ndipo adzatuluke kunja mamita 450, kuzungulira mudziwo. \v 5 Kunja kwa mudzi yezani mamita 900 kummawa, mamita 900 kumpoto ndipo mudziwo ukhale pakati. Adzakhala ndi dera limeneli ngati malo a midziyo, owetera ziweto zawo. \s1 Mizinda Yopulumukirako \p \v 6 “Isanu ndi umodzi mwa midzi imene mudzapereke kwa Alevi idzakhala mizinda yopulumukirako, kumene munthu wopha mnzake adzathawireko. Ndipo mudzawapatsenso midzi ina 42. \v 7 Midzi yonse imene mudzapereke kwa Alevi idzakhale 48, pamodzi ndi malo oweterako ziweto. \v 8 Pamene mukupatula midzi imeneyi pa cholowa cha Aisraeli, muchotsepo midzi yambiri pa mafuko aakulu, ndipo midzi pangʼono pa mafuko aangʼono. Fuko lililonse lidzapereka kwa Alevi molingana ndi kukula kwa cholowa chimene lalandira.” \p \v 9 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, \v 10 “Yankhula ndi Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mu Kanaani, \v 11 sankhani midzi ina kuti ikhale mizinda yanu yopulumukirako, kumene munthu wopha munthu wina mwangozi angathawireko. \v 12 Adzakhala malo obisalako pothawa munthu wofuna kulipsira, kuti munthu wopha mnzake mwangozi asaphedwe mpaka akayime pamaso pa gulu la anthu kuti akaweruzidwe. \v 13 Midzi isanu ndi umodzi imene muyiperekeyi idzakhala mizinda yopulumukirako. \v 14 Mupereke itatu mbali ino ya Yorodani ndi itatu ina mu Kanaani kuti ikhale mizinda yopulumukirako. \v 15 Midzi isanu ndi umodzi idzakhala malo opulumukirako Aisraeli, alendo ndi anthu ena onse okhala pakati pawo kuti wina aliyense wopha mnzake mwangozi adzathawireko. \p \v 16 “ ‘Ngati munthu amenya mnzake ndi chitsulo, munthuyo nʼkufa, ndiye kuti iyeyo ndi wakupha ndipo wakuphayo aphedwe. \v 17 Kapenanso ngati wina wake ali ndi mwala mʼdzanja mwake womwe ungaphe munthu, ndipo agenda nawo wina, munthu winayo nʼkufa, ndiye kuti iyeyo ndi wakupha ndipo wakuphayo adzayenera kuphedwa. \v 18 Kapenanso ngati wina ali ndi chibonga mʼdzanja mwake choti nʼkupha nacho munthu, namenya nacho munthu, munthuyo nʼkufa, ndiye kuti iyeyo ndi wakupha, wakuphayo ayenera kuphedwa. \v 19 Wolipsira adzamuphanso wakuphayo. Pamene akumana naye adzayenera kumupha ndithu. \v 20 Ndipo ngati wina wake, chifukwa cha udani, aganiza zokankha munthu wina kapena kumuponyera chinthu china mwadala munthuyo nʼkufa, \v 21 kapena ngati, chifukwa cha udani, amenya mnzake ndi nkhonya, mnzakeyo ndi kufa, munthuyo ayenera kuphedwa. Iyeyo ndi wakupha. Wolipsira adzamuphe wakuphayo pamene akumana naye. \p \v 22 “ ‘Koma ngati popanda udani wina uliwonse, mwadzidzidzi akankha wina kapena kumuponyera chinthu osati mwadala, \v 23 kapena mosamuona nʼkumuponyera mwala womwe utha kumupha, munthuyo nʼkufa, tsono pakuti sanali mdani wake ndipo sanaganizire zomupweteka, \v 24 gulu liweruze pakati pa iye ndi wolipsira monga mwa malamulo ake. \v 25 Gulu lidzapulumutsa munthu wakuphayo mʼmanja mwa wolipsira uja ndi kumubwezera ku mzinda wopulumukirako kumene anathawira. Ayenera kukhala kumeneko kufikira imfa ya mkulu wa ansembe, amene anadzozedwa ndi mafuta oyera. \p \v 26 “ ‘Koma ngati wolakwayo atuluka kunja kwa malire a mzinda wopulumukirako kumene anathawira \v 27 ndipo wobwezera choyipa nʼkumupeza kunja kwa mzindawo, wolipsirayo atha kumupha wolakwayo popanda kugamula mlandu wakupha. \v 28 Wolakwayo ayenera kukhala mu mzinda wopulumukiramowo mpaka imfa ya mkulu wa ansembe ndipo pamenepo atha kubwerera kwawo. Pokhapokha atafa mkulu wa ansembe ndi pamene angathe kubwerera ku malo ake. \p \v 29 “ ‘Amenewa akhale malamulo ndi malangizo kwa inu nthawi zonse ndi ku mibado ya mʼtsogolo, kulikonse kumene mudzakhalako. \p \v 30 “ ‘Aliyense wopha munthu ayeneranso kuphedwa ngati pali umboni okwanira. Koma wina asaphedwe ngati pali mboni imodzi yokha. \p \v 31 “ ‘Osalola kulandira dipo lowombolera munthu wakupha yemwe ayenera kuphedwa. Wakupha ayenera kuphedwa. \p \v 32 “ ‘Simuyeneranso kulandira dipo kwa munthu amene wathawira ku mzinda wopulumikirako kuti wothawayo abwerere kwawo, pokhapokha ngati mkulu wa ansembe wamwalira. \p \v 33 “ ‘Musayipitse dziko limene mukukhalamolo. Magazi amayipitsa dziko ndipo nʼkosatheka kulipirira dziko chifukwa cha magazi amene akhetsedwa mʼmenemo, kupatula pokhetsa magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo. \v 34 Choncho musadetse dziko limene mukukhalamo, dziko limene Inenso ndimakhalamo, pakuti Ine Yehova, ndimakhala pakati pa Aisraeli.’ ” \c 36 \s1 Cholowa cha Ana Aakazi a Zelofehadi \p \v 1 Atsogoleri a mabanja a fuko la Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase omwe anali ochokera ku fuko la ana a Yosefe anabwera ndi kuyankhula ndi Mose, atsogoleri ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli. \v 2 Iwo anati, “Pamene Yehova analamula mbuye wanga kuti apereke dziko ngati cholowa kwa Aisraeli mwa maere, anakulamulani inu kupereka cholowa cha mʼbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi. \v 3 Tsopano ngati akwatiwa ndi aamuna ochokera ku mafuko ena a mitundu ya Aisraeli, cholowa chawo chidzatengedwa kuchoka pa cholowa cha makolo athu ndipo adzachiwonjezera ku fuko limene akwatiwakolo. Ndipo gawo lina la cholowacho, lopatsidwa kwa ife lidzatengedwa. \v 4 Pamene chaka cha chikondwerero cha zaka makumi asanu, cha Aisraeli chafika, cholowa chawo chidzawonjezeredwa ku fuko limene iwo akwatiwako. Ndipo katundu wawo adzachotsedwa pa cholowa cha fuko la makolo athu.” \p \v 5 Tsono mwa lamulo la Yehova, Mose anapereka lamulo ili kwa Aisraeli: “Zimene ana a Yosefe akunena ndi zoona. \v 6 Izi ndi zimene Yehova akulamula kwa ana aakazi a Zelofehadi: Atha kukwatiwa ndi aliyense amene angakondweretsedwe naye koma zingakhale bwino atakwatiwa mʼfuko la abambo awo \v 7 kuti cholowa cha Israeli chisapite ku fuko lina, pakuti Mwisraeli aliyense ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake. \v 8 Mwana wamkazi aliyense amene adzalandira cholowa cha dziko la fuko lililonse la Israeli ayenera kukwatiwa ndi munthu wa fuko la abambo ake. \v 9 Cholowa chilichonse mu Israeli sichiyenera kupita ku fuko lina, popeza fuko lililonse la Israeli liyenera kusunga cholowa chimene linalandira.” \p \v 10 Choncho ana aakazi a Zelofehadi anachita monga Yehova analamulira Mose. \v 11 Ana aakazi a Zelofehadi amene ndi Mahila, Tiriza, Hogila, Milika ndi Nowa, anakwatiwa ndi asuweni awo a ku mbali ya abambo awo. \v 12 Anakwatiwa mʼmafuko a zidzukulu za Manase mwana wa Yosefe, ndipo cholowa chawo chinakhalabe mʼfuko la abambo awo. \b \p \v 13 Awa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kupyolera mwa Mose ku chigwa cha Mowabu mʼmbali mwa Yorodani, ku Yeriko.