\id LUK - Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 \ide UTF-8 \h LUKA \toc1 Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Luka \toc2 Luka \toc3 Lk \mt2 UTHENGA WABWINO WA YESU KHRISTU WOLEMBEDWA NDI \mt1 LUKA \c 1 \s1 Mawu Oyamba \p \v 1 Ambiri anayesa kufotokoza nkhani ya zimene zinakwaniritsidwa pakati pathu, \v 2 monga mmene zinaperekedwera kwa ife ndi iwo amene anaona poyambirira ndi atumiki a mawu. \v 3 Popeza inenso ndafufuza mosamalitsa chilichonse kuyambira pachiyambi, zandikomera kukulemberani mwatsatanetsatane inu wolemekezeka Tiofilo, \v 4 kuti mudziwe bwinobwino zoona za zinthu zimene mwaphunzitsidwa. \s1 Aneneratu za Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi \p \v 5 Mʼmasiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali wansembe dzina lake Zakariya wa gulu la ansembe la Abiya; mkazi wake Elizabeti analinso wa fuko la Aaroni. \v 6 Onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo amasunga malamulo ndi malangizo onse a Ambuye osalakwa konse. \v 7 Koma analibe ana chifukwa Elizabeti anali wosabereka; ndipo onse anali okalamba. \p \v 8 Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu, \v 9 Zakariyayo anasankhidwa mwa maere, monga mwa mwambo wa unsembe, kupita mʼNyumba ya Ambuye kukafukiza lubani. \v 10 Ndipo nthawi yofukiza lubani itafika, gulu lonse lopembedza linkapemphera kunja. \p \v 11 Kenaka mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye, atayimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizira. \v 12 Zakariya ataona mngeloyo, anadzidzimuka ndipo anagwidwa ndi mantha. \v 13 Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane. \v 14 Ndipo adzakhala chimwemwe ndi chisangalalo kwa iwe, ndipo ambiri adzasangalala chifukwa cha kubadwa kwake, \v 15 chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa. \v 16 Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo. \v 17 Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.” \p \v 18 Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.” \p \v 19 Mngeloyo anayankha kuti, “Ine ndine Gabrieli. Ndimayima pamaso pa Mulungu, ndipo ndatumidwa kwa iwe kudzakuwuza uthenga wabwinowu. \v 20 Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.” \p \v 21 Pa nthawiyi, anthu ankadikira Zakariya ndipo anadabwa chifukwa anatenga nthawi yayitali ali mʼNyumba ya Mulungu. \v 22 Atatuluka sanathe kuyankhulana nawo. Anazindikira kuti anaona masomphenya mʼNyumbamo, chifukwa ankasonyeza zizindikiro kwa iwo koma sankatha kuyankhula. \p \v 23 Nthawi yake yotumikira itatha, anabwerera kwawo. \v 24 Zitatha izi, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pakati ndipo anadzibisa kwa miyezi isanu. \v 25 Iye anati, “Ambuye wandichitira izi, kuti mʼmasiku ano wandionetsera kukoma mtima kwake ndi kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.” \s1 Aneneratu za Kubadwa kwa Yesu \p \v 26 Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya, \v 27 kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya. \v 28 Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.” \p \v 29 Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere. \v 30 Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. \v 31 Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. \v 32 Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, \v 33 ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.” \p \v 34 Mariya anafunsa mngeloyo kuti, “Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?” \p \v 35 Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. \v 36 Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. \v 37 Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.” \p \v 38 Mariya anayankha kuti, “Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera.” \s1 Mariya Acheza kwa Elizabeti \p \v 39 Nthawi imeneyo anakonzeka ndipo anapita mofulumira ku mudzi wa ku mapiri a dziko la Yudeya, \v 40 kumene anakalowa mʼnyumba ya Zakariya nalonjera Elizabeti. \v 41 Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. \v 42 Anafuwula ndi mawu akulu kuti, “Ndiwe wodala pakati pa akazi, ndipo ndi wodala mwana amene udzabereke! \v 43 Koma nʼchifukwa chiyani andikomera mtima kuti amayi a Ambuye anga abwere kwa ine? \v 44 Nthawi yomwe ndinamva mawu akulonjera kwanu, mwana anatakataka mʼmimba mwanga chifukwa cha chimwemwe. \v 45 Wodala iye amene wakhulupirira kuti chimene Ambuye wanena kwa iye chidzakwaniritsidwa!” \s1 Nyimbo ya Mariya \p \v 46 Ndipo Mariya anati: \q1 “Moyo wanga ulemekeza Ambuye. \q2 \v 47 Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga, \q1 \v 48 pakuti wakumbukira \q2 kudzichepetsa kwa mtumiki wake. \q1 Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala, \q2 \v 49 pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu, \q2 dzina lake ndi loyera. \q1 \v 50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye \q2 kufikira mibadomibado. \q1 \v 51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake; \q2 Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo. \q1 \v 52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu, \q2 koma wakweza odzichepetsa. \q1 \v 53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino \q2 koma anachotsa olemera wopanda kanthu. \q1 \v 54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli, \q2 pokumbukira chifundo chake. \q1 \v 55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse \q2 monga ananena kwa makolo athu.” \p \v 56 Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu ndipo kenaka anabwerera kwawo. \s1 Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi \p \v 57 Itakwana nthawi yoti Elizabeti abereke, anabereka mwana wamwamuna. \v 58 Anansi ndi abale ake anamva kuti Ambuye anamuchitira chifundo chachikulu ndipo anakondwera naye pamodzi. \p \v 59 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu anabwera ndi mwana kuti adzachitidwe mdulidwe, ndipo anafuna kumupatsa dzina la abambo ake Zakariya, \v 60 koma amayi ake anayankhula nati, “Ayi, atchulidwe kuti Yohane.” \p \v 61 Iwo anati kwa iye, “Palibe mmodzi mwa abale ake amene ali ndi dzina limeneli.” \p \v 62 Pamenepo anapanga zizindikiro kwa abambo ake kuti adziwe dzina limene akanakonda kumutcha mwanayo. \v 63 Iye anapempha poti alembepo, ndipo chodabwitsa kwa aliyense analemba kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” \v 64 Nthawi yomweyo pakamwa pake panatsekuka ndi lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula, nayamika Mulungu. \v 65 Anansi onse anachita mantha kwambiri, ndipo ku madera onse a kumapiri a Yudeya, anthu anayankhula zinthu zonsezi. \v 66 Aliyense amene anamva izi anadabwa nazo nafunsa kuti, “Kodi mwana uyu adzakhala wotani?” Pakuti dzanja la Ambuye lili pa iye. \s1 Nyimbo ya Zakariya \p \v 67 Abambo ake, Zakariya, anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenera kuti, \q1 \v 68 “Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli \q2 chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake. \q1 \v 69 Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife \q2 mu nyumba ya mtumiki wake Davide. \q1 \v 70 (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera), \q1 \v 71 chipulumutso kuchoka kwa adani athu \q2 ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida, \q1 \v 72 kuonetsa chifundo kwa makolo athu \q2 ndi kukumbukira pangano lake loyera, \q2 \v 73 lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu: \q1 \v 74 kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu, \q2 ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha, \q2 \v 75 mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse. \b \q1 \v 76 “Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba; \q2 pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake, \q1 \v 77 kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso \q2 kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo, \q1 \v 78 chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu, \q2 ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba, \q1 \v 79 kuwalira iwo okhala mu mdima \q2 ndi mu mthunzi wa imfa, \q1 kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere.” \p \v 80 Ndipo mwanayo anakula nakhala wamphamvu mu mzimu; ndipo anakhala ku chipululu mpaka pamene anaonekera poyera mu Israeli. \c 2 \s1 Kubadwa kwa Yesu \p \v 1 Mʼmasiku amenewo Kaisara Augusto anapereka lamulo kuti kalembera achitike mʼdziko lonse la Aroma. \v 2 (Uyu ndi kalembera woyamba amene anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya). \v 3 Ndipo aliyense anapita ku mzinda wa kwawo kukalembetsa. \p \v 4 Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide. \v 5 Iye anapita kumeneko kukalembetsa pamodzi ndi Mariya, amene anapalana naye ubwenzi kuti akwatirane ndipo anali woyembekezera. \v 6 Ali kumeneko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe, \v 7 ndipo anabereka mwana wake woyamba, wamwamuna. Iye anamukulunga mʼnsalu ndi kumuyika modyera ngʼombe, chifukwa kunalibe malo mʼnyumba ya alendo. \s1 Abusa ndi Angelo \p \v 8 Ndipo kunali abusa amene amakhala ku dera lomwelo, kuyangʼanira ziweto zawo usiku. \v 9 Mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iwo ndipo ulemerero wa Ambuye unawala mowazungulira. Iwo anachita mantha. \v 10 Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse. \v 11 Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye. \v 12 Ichi chidzakhala chizindikiro kwa inu: mukapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera ngʼombe.” \p \v 13 Mwadzidzidzi gulu lalikulu la angelo linaonekera pamodzi ndi mngeloyo, kuyamika Mulungu ndi kumati, \q1 \v 14 “Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba, \q2 ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo.” \p \v 15 Angelowo atabwerera kumwamba, abusawo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni ku Betelehemu tikaone zinthu zomwe zachitika, zimene Ambuye atiwuza ife.” \p \v 16 Ndipo iwo anafulumira nyamuka nakapeza Mariya ndi Yosefe ndi mwana wakhanda, amene anagona modyera ngʼombe. \v 17 Pamene anamuona Iye, iwo anafotokoza zomwe anawuzidwa za mwanayo, \v 18 ndipo onse amene anamva zimene abusawa ananena anadabwa. \v 19 Koma Mariya anasunga zonsezi mu mtima mwake ndi kumazilingalira. \v 20 Abusa anabwerera, akulemekeza ndi kuyamika Mulungu chifukwa cha zonse anazimva ndi kuziona, zomwe zinali monga anawuzidwira ndi angelo aja. \s1 Yesu Aperekedwa mʼNyumba ya Mulungu \p \v 21 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, tsiku loti amuchite mdulidwe anamutcha Yesu, dzina limene mngelo anamupatsa asanabadwe. \p \v 22 Nthawi yoyeretsedwa kwawo itatha, monga mwa lamulo la Mose, Yosefe ndi Mariya anapita naye ku Yerusalemu kukamupereka kwa Ambuye. \v 23 (Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”), \v 24 ndi kupereka nsembe posunga zimene zinanenedwa mulamulo la Ambuye: “Njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri.” \p \v 25 Ndipo taonani, mu Yerusalemu munali munthu wotchedwa Simeoni, amene anali wolungama ndi wodzipereka. Iye ankadikira chitonthozo cha Israeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. \v 26 Mzimu Woyera anamuwululira kuti sadzafa asanaone Khristu wa Ambuye. \v 27 Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo, \v 28 Simeoni anamunyamula mʼmanja mwake nayamika Mulungu, nati: \q1 \v 29 “Ambuye waulamuliro, monga munalonjeza, \q2 tsopano lolani kuti mtumiki wanu apite mu mtendere. \q1 \v 30 Pakuti maso anga aona chipulumutso chanu, \q2 \v 31 chimene Inu munakonza pamaso pa anthu onse, \q1 \v 32 kuwala kowunikira anthu a mitundu ina \q2 ndi kwa ulemerero kwa anthu anu Aisraeli.” \p \v 33 Abambo ndi amayi a Mwanayo anadabwa chifukwa cha zimene zinanenedwa za Iye. \v 34 Kenaka Simeoni anawadalitsa ndipo anati kwa Mariya amayi ake: “Mwana uyu wakonzedwa kukhala kugwa ndi kudzuka kwa ambiri mu Israeli, ndi kukhala chizindikiro chimene adzayankhula motsutsana nacho, \v 35 kotero kuti malingaliro a mitima ya ambiri adzawululidwa. Ndipo lupanga lidzabaya moyo wakonso.” \p \v 36 Panalinso mneneri wamkazi, dzina lake Ana, mwana wa Fanuelo, wa fuko la Aseri. Anali wokalamba kwambiri; anakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri atakwatiwa, \v 37 ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera. \v 38 Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu. \p \v 39 Yosefe ndi Mariya atachita zonse zimene zinkafunikira ndi lamulo la Ambuye, anabwerera ku Galileya ku mudzi wa Nazareti. \v 40 Ndipo Mwanayo anakula nakhala wamphamvu; Iye anadzazidwa ndi nzeru, ndipo chisomo cha Mulungu chinali pa Iye. \s1 Yesu mʼNyumba ya Mulungu \p \v 41 Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska. \v 42 Iye ali ndi zaka khumi ndi ziwiri, anapita ku phwando, monga mwa mwambo. \v 43 Phwando litatha, pamene makolo ake ankabwerera kwawo, mnyamata Yesu anatsalira ku Yerusalemu, koma iwo sanadziwe zimenezi. \v 44 Poganiza kuti anali nawo mʼgulu lawo, anayenda tsiku limodzi. Kenaka anayamba kumufunafuna pakati pa abale awo ndi anzawo. \v 45 Atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu kukamufuna. \v 46 Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso. \v 47 Aliyense amene anamumva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake. \v 48 Makolo ake atamuona, anadabwa. Amayi ake anati kwa Iye, “Mwanawe, watichitira zimenezi chifukwa chiyani? Abambo ako ndi ine takhala tili ndi nkhawa kukufunafuna Iwe.” \p \v 49 Iye anawafunsa kuti, \wj “Nʼchifukwa chiyani mumandifunafuna? Kodi simukudziwa kuti ndikuyenera kukhala mʼnyumba ya Atate anga?”\wj* \v 50 Koma iwo sanazindikire chomwe Iye amatanthauza. \p \v 51 Kenaka anapita nawo ku Nazareti ndipo anawamvera iwo. Koma amayi ake anasunga zinthu zonsezi mu mtima mwawo. \p \v 52 Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu. \c 3 \s1 Yohane Mʼbatizi Akonza Njira \p \v 1 Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene. \v 2 Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu. \v 3 Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo. \v 4 Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti: \q1 “Mawu a wofuwula mʼchipululu, \q1 konzani njira ya Ambuye, \q2 wongolani njira zake. \q1 \v 5 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa \q2 ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa, \q1 misewu yokhotakhota idzawongoledwa, \q2 ndi njira zosasalala zidzasalazidwa. \q1 \v 6 Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.” \p \v 7 Yohane anati kwa magulu a anthu amene amabwera kudzabatizidwa ndi iye, “Ana anjoka inu! Anakuchenjezani ndani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwera? \v 8 Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana. \v 9 Nkhwangwa ili kale pa muzu wamitengo, ndipo mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.” \p \v 10 Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?” \p \v 11 Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.” \p \v 12 Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?” \p \v 13 Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.” \v 14 Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” \p Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.” \p \v 15 Anthu ankadikira ndi chiyembekezo ndipo ankasinkhasinkha mʼmitima mwawo kuti mwina Yohane nʼkukhala Khristu. \v 16 Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto. \v 17 Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.” \v 18 Ndipo ndi mawu ena ambiri, Yohane anawachenjeza anthu ndi kuwalalikira Uthenga Wabwino. \p \v 19 Koma pamene Yohane anadzudzula Herode wolamulirayo chifukwa chokwatira Herodia, mkazi wa mʼbale wake, ndi zoyipa zina zonse anazichita, \v 20 Herode anawonjezanso choyipa ichi pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende. \s1 Ubatizo wa Yesu \p \v 21 Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka. \v 22 Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.” \s1 Makolo a Yesu \p \v 23 Ndipo Yesu anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ntchito yake. Monga mmene anthu ankaganizira, Iyeyo anali mwana wa Yosefe, \b \li1 mwana wa Heli, \v 24 mwana wa Matate, \li1 mwana wa Levi, mwana wa Meliki, \li1 mwana wa Yaneyi, mwana wa Yosefe \li1 \v 25 mwana wa Matati, mwana wa Amosi, \li1 mwana wa Naomi, mwana wa Esli, \li1 mwana wa Nagai, \v 26 mwana wa Maati, \li1 mwana wa Matatiyo, mwana wa Simeoni, \li1 mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda \li1 \v 27 mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, \li1 mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli, \li1 mwana wa Neri, \v 28 mwana wa Meliki, \li1 mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, \li1 mwana wa Elmadama, mwana wa Ere, \li1 \v 29 mwana wa Jose, mwana wa Eliezara, \li1 mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, \li1 mwana wa Levi, \v 30 mwana wa Simeoni, \li1 mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe, \li1 mwana wa Yonamu, mwana wa Eliakimu, \li1 \v 31 mwana wa Meleya, mwana wa Mena, \li1 mwana wa Matata, mwana wa Natani, \li1 mwana wa Davide, \v 32 mwana wa Yese, \li1 mwana wa Obedi, mwana wa Bowazi, \li1 mwana wa Salimoni, mwana wa Naasoni, \li1 \v 33 mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni, \li1 mwana wa Hezronu, mwana wa Perezi, \li1 mwana wa Yuda, \v 34 mwana wa Yakobo, \li1 mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu, \li1 mwana wa Tera, mwana wa Nakoro, \li1 \v 35 mwana wa Serugi, mwana wa Reu, \li1 mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi, \li1 mwana wa Sela, \v 36 mwana wa Kainane, \li1 mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu, \li1 mwana wa Nowa, mwana wa Lameki, \li1 \v 37 mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, \li1 mwana wa Yaredi mwana wa Malaleeli, \li1 mwana wa Kainane, \v 38 mwana wa Enosi, \li1 mwana wa Seti, \li1 mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu. \c 4 \s1 Kuyesedwa kwa Yesu \p \v 1 Yesu, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anachoka ku mtsinje wa Yorodani ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu Woyerayo kupita ku chipululu, \v 2 kumene anayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anayi. Sanadye kena kalikonse pa masiku amenewo, ndipo pa mapeto pake anamva njala. \p \v 3 Mdierekezi anati kwa Iye, “Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, uza mwala uwu kuti usanduke buledi.” \p \v 4 Yesu anayankha kuti, \wj “Zalembedwa: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.’ ”\wj* \p \v 5 Mdierekezi anamutengera Iye pamalo aatali ndipo mʼkamphindi namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi. \v 6 Ndipo anati kwa Iye, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wawo; pakuti anandipatsa ine, ndipo ndingathe kupereka kwa aliyense amene ndikufuna. \v 7 Ngati mutandilambira, zonsezi zidzakhala zanu.” \p \v 8 Yesu anayankha kuti, \wj “Zalembedwa: ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”\wj* \p \v 9 Mdierekezi anapita naye ku Yerusalemu namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu dziponyeni nokha pansi kuchokera pano. \v 10 Pakuti kwalembedwa, \q1 “Adzalamulira angelo ake za iwe \q2 kuti akutchinjirize mosamala; \q1 \v 11 ndipo adzakunyamula ndi manja awo, \q2 kuti phazi lako lisagunde pa mwala.” \p \v 12 Yesu anayankha kuti, \wj “Mawu akuti, ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”\wj* \p \v 13 Mdierekezi atamaliza mayesero awa onse, anamusiya Iye kufikira atapeza mpata wina. \s1 Yesu Akanidwa ku Nazareti \p \v 14 Yesu anabwerera ku Galileya mu mphamvu ya Mzimu Woyera, ndipo mbiri yake inafalikira ku madera onse a ku midzi. \v 15 Iye ankaphunzitsa mʼmasunagoge awo, ndipo aliyense ankamulemekeza. \p \v 16 Iye anapita ku Nazareti, kumene anakulira, ndipo pa tsiku la Sabata anakalowa mʼsunagoge, monga mwa chikhalidwe chake. Ndipo anayimirira kuti awerenge malemba. \v 17 Anamupatsa buku la mneneri Yesaya. Atalitsekula, anapeza pamalo pamene panalembedwa kuti, \q1 \v 18 \wj “Mzimu wa Ambuye ali pa Ine;\wj* \q2 \wj chifukwa wandidzoza\wj* \q2 \wj kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka.\wj* \q1 \wj Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe\wj* \q2 \wj ndi kwa osaona kuti apenyenso,\wj* \q1 \wj kumasulidwa kwa osautsidwa,\wj* \q2 \v 19 \wj ndi kulalikira za nthawi imene Ambuye adzakomere mtima anthu awo.”\wj* \p \v 20 Kenaka Iye anatseka bukulo, nalibwezera kwa wotumikira ndipo anakakhala pansi. Maso a aliyense mʼsunagogemo anali pa Iye, \v 21 ndipo anawawuza kuti, \wj “Lero malemba awa akwaniritsidwa mmene mwamveramu.”\wj* \p \v 22 Onse anayankhula zabwino za Iye ndipo anadabwa ndi mawu ogwira moyo amene anatuluka mʼkamwa mwake. Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu si mwana wa Yosefe?” \p \v 23 Yesu anawawuza kuti, \wj “Zoonadi, mudzandiwuza mwambi uwu: Singʼanga, dzichiritse wekha! Chitanso mʼmudzi wa kwanu kuno zimene ife tamva kuti Iwe unazichita ku Kaperenawo.”\wj* \p \v 24 Iye anapitiriza kuti, \wj “Zoonadi, ndikukuwuzani kuti palibe mneneri amene amavomerezedwa ku mudzi kwawo.\wj* \v 25 \wj Ine ndikukutsimikizirani kunali amayi ambiri amasiye mu Israeli mʼnthawi ya Eliya, kumwamba kutatsekedwa kwa zaka zitatu ndi theka ndipo kunali njala yayikulu mʼdziko lonselo.\wj* \v 26 \wj Komabe Eliya sanatumidwe kwa mmodzi mwa iwo, koma kwa mkazi wamasiye wa ku Zerefati ku chigawo cha Sidoni.\wj* \v 27 \wj Ndipo kunali akhate ambiri ku Israeli mʼnthawi ya mneneri Elisa, koma panalibe mmodzi mwa iwo anachiritsidwa kupatula Naamani wa ku Siriya.”\wj* \p \v 28 Anthu onse mʼsunagogemo anapsa mtima atamva izi. \v 29 Anayimirira namutulutsira kunja kwa mzindawo, ndipo anamutengera pamwamba pa phiri pamene mzindawo unamangidwapo, ndi cholinga chakuti amuponyere ku phompho. \v 30 Koma Iye anangoyenda pakati pa gulu la anthulo nachokapo. \s1 Yesu Atulutsa Mzimu Woyipa \p \v 31 Kenaka Iye anapita ku Kaperenawo, mudzi wa ku Galileya, ndipo pa Sabata anayamba kuphunzitsa anthu. \v 32 Iwo anadabwa ndi chiphunzitso chake chifukwa uthenga wake unali ndi ulamuliro. \p \v 33 Mʼsunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu woyipa. Iye analira ndi mawu akulu, akuti \v 34 “Aa! Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!” \p \v 35 Yesu anachidzudzula kwambiri nati, \wj “Khala chete! Tuluka mwa iye.”\wj* Chiwandacho chinamugwetsa munthuyo pansi pamaso pa onse ndipo chinatuluka wosamupweteka. \p \v 36 Anthu onse anadabwa ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi chiphunzitso ichi ndi chotani? Ndi ulamuliro ndi mphamvu Iye akulamulira mizimu yoyipa ndipo ikutuluka!” \v 37 Ndipo mbiri yake inafalikira madera onse ozungulira. \s1 Yesu Achiritsa Anthu Ambiri \p \v 38 Yesu anatuluka mʼsunagoge ndipo anapita kwa Simoni. Tsopano mpongozi wake wa Simoni amadwala malungo akulu, ndipo anamupempha Yesu kuti amuthandize. \v 39 Ndipo anawerama nadzudzula malungowo ndipo anamusiya. Anadzuka nthawi yomweyo nayamba kuwatumikira. \p \v 40 Pamene dzuwa linkalowa, anthu anabweretsa kwa Yesu onse amene anali ndi matenda osiyanasiyana, ndipo atasanjika manja ake pa aliyense, anachiritsidwa. \v 41 Komanso ziwanda zinkatuluka mwa anthu ambiri, zikufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” Koma Iye anazidzudzula ndipo sanazilole kuyankhula chifukwa zimadziwa kuti Iye ndi Khristu. \p \v 42 Kutacha, Yesu anapita ku malo a yekha. Anthu ankamufunafuna Iye ndipo pamene anafika kumene anali, anthuwo anayesetsa kumuletsa kuti asawachokere. \v 43 Koma Iye anati, \wj “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.”\wj* \v 44 Ndipo Iye anapitirirabe kulalikira mʼmasunagoge a ku Yudeya. \c 5 \s1 Yesu Ayitana Ophunzira Oyamba \p \v 1 Tsiku lina Yesu anayima mʼmbali mwa nyanja ya Genesareti, gulu la anthu litamuzungulira likumvetsera mawu a Mulungu. \v 2 Iye anaona mabwato awiri ali mʼmphepete mwa nyanja, asodzi amene ankachapa makhoka awo atawasiya pamenepo. \v 3 Iye analowa mʼbwato limodzi limene linali la Simoni, ndi kumupempha kuti alikankhire mʼkati mwa nyanja pangʼono. Kenaka Iye anakhala pansi nayamba kuphunzitsa anthu ali mʼbwatomo. \p \v 4 Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, \wj “Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba.”\wj* \p \v 5 Simoni anayankha kuti, “Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka.” \p \v 6 Atachita izi, anagwira nsomba zambiri kotero kuti makhoka awo anayamba kungʼambika. \v 7 Choncho anakodola anzawo a bwato linalo kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo anabwera nadzaza mabwato onse awiri mpaka kuyamba kumira. \p \v 8 Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, “Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!” \v 9 Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira, \v 10 chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anzake a Simoniyo. \p Kenaka Yesu anati kwa Simoni, \wj “Musachite mantha; kuyambira tsopano ndidzakusandutsani asodzi a anthu.”\wj* \v 11 Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye. \s1 Yesu Achiritsa Munthu Wakhate \p \v 12 Yesu ali ku mudzi wina, munthu amene anali ndi khate thupi lonse anabwera kwa Iye. Munthuyo ataona Yesu, anagwa chafufumimba ndipo anamupempha Iye kuti, “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” \p \v 13 Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo. Iye anati, \wj “Ine ndikufuna, yeretsedwa!”\wj* Ndipo nthawi yomweyo khate lake linachoka. \p \v 14 Kenaka Yesu anamulamula kuti, \wj “Usawuze wina aliyense, koma pita, kadzionetse kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose anakulamulirani za kuyeretsedwa kwanu monga umboni kwa iwo.”\wj* \p \v 15 Koma mbiri yake inafalikirabe kwambiri kotero kuti magulu a anthu anabwera kudzamvetsera ndi kuti achiritsidwe ku matenda awo. \v 16 Koma Yesu nthawi zambiri ankachoka kupita ku malo a yekha kukapemphera. \s1 Yesu Achiritsa Wofa Ziwalo \p \v 17 Tsiku lina pamene ankaphunzitsa, Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, amene anachokera ku midzi yonse ya Galileya ndi ku Yudeya ndi Yerusalemu, anakhala pansi pomwepo. Ndipo mphamvu ya Ambuye inalipo yakuti Iye achiritse odwala. \v 18 Amuna ena anabwera atanyamula munthu wofa ziwalo pa mphasa ndipo anayesa kumulowetsa mʼnyumba kuti amugoneke pamaso pa Yesu. \v 19 Atalephera kupeza njira yochitira zimenezi chifukwa cha gulu la anthu, anakwera naye pa denga ali pa mphasa pomwepo ndi kumutsitsira mʼkati pakati pa gulu la anthu, patsogolo penipeni pa Yesu. \p \v 20 Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati, \wj “Mnzanga, machimo ako akhululukidwa.”\wj* \p \v 21 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anayamba kuganiza mwa iwo okha kuti, “Kodi munthu uyu ndi ndani amene ayankhula zamwano? Kodi ndani amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu?” \p \v 22 Yesu anadziwa zomwe iwo amaganiza ndipo anafunsa kuti, \wj “Kodi ndi chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi mʼmitima mwanu?\wj* \v 23 \wj Kodi chapafupi ndi chiti: kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo yenda?’\wj* ” \v 24 \wj Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo,\wj* Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, \wj “Ine ndikuwuza iwe kuti, ‘Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’ ”\wj* \v 25 Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu. \v 26 Aliyense anadabwa ndi kuchita mantha ndipo anayamika Mulungu. Iwo anadabwa kwambiri ndipo anati, “Lero taona zinthu zosayiwalika.” \s1 Kuyitanidwa kwa Levi \p \v 27 Zitatha izi, Yesu anachoka ndipo anaona wolandira msonkho dzina lake Levi atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anati kwa iye, \wj “Nditsate Ine.”\wj* \v 28 Ndipo Levi anayimirira, nasiya zonse ndi kumutsata Iye. \p \v 29 Kenaka Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu ku nyumba yake ndipo gulu lalikulu la amisonkho ndi ena ankadya naye pamodzi. \v 30 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amene anali a gulu lawo anadandaula kwa ophunzira ake, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukudya ndi kumwa pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?” \p \v 31 Yesu anawayankha kuti, \wj “Amene sakudwala safuna singʼanga, koma odwala.\wj* \v 32 \wj Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.”\wj* \s1 Yesu Afunsidwa za Kusala Kudya \p \v 33 Iwo anati kwa Iye, “Ophunzira a Yohane amasala kudya ndi kupemphera kawirikawiri, monganso ophunzira a Afarisi, koma anu amangodya ndi kumwa.” \p \v 34 Yesu anawayankha kuti, \wj “Kodi alendo a mkwati angasale kudya pamene mkwati ali pakati pawo?\wj* \v 35 \wj Koma nthawi ikubwera pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo. Masiku amenewo adzasala kudya.”\wj* \p \v 36 Iye anawawuza fanizo ili: \wj “Palibe amene amangʼamba chigamba kuchokera pa chovala chatsopano ndi kuchisokerera pa chakale. Ngati atatero, ndiye kuti adzangʼamba chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chochokera pa chovala chatsopano chija sichidzagwirizana ndi chakale.\wj* \v 37 \wj Ndipo palibe amene amakhuthulira vinyo watsopano mʼmatumba a vinyo akale. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa zikopazo, vinyo adzatayika ndipo zikopa za vinyozo zidzawonongeka.\wj* \v 38 \wj Ayi, vinyo watsopano ayenera kuthiridwa mʼmatumba a vinyo azikopa zatsopano.\wj* \v 39 \wj Ndipo palibe amene atamwa vinyo wakale amafuna watsopano, pakuti amati, ‘Wakale ndi okoma.’ ”\wj* \c 6 \s1 Yesu Mbuye wa Sabata \p \v 1 Tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa mʼminda yatirigu, ndipo ophunzira ake anayamba kubudula ngala zatirigu, namazifikisa mʼmanja mwawo ndi kumadya. \v 2 Ena mwa Afarisi anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mukuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata?” \p \v 3 Yesu anawayankha iwo kuti, \wj “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali ndi njala?\wj* \v 4 \wj Iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo atatenga buledi wopatulika anadya amene ndi ololedwa kudya ansembe okha. Ndipo anaperekanso wina kwa anzake.”\wj* \v 5 Kenaka Yesu anawawuza kuti, \wj “Mwana wa Munthu ndi Ambuye wa Sabata.”\wj* \p \v 6 La Sabata lina Iye analowa mʼsunagoge kukaphunzitsa ndipo mʼmenemo anapeza munthu wadzanja lolumala. \v 7 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo ankamuyangʼana kuti apeze chifukwa Yesu, choncho anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati Iye akanamuchiritsa pa Sabata. \v 8 Koma Yesu anadziwa zimene ankaganiza ndipo anati kwa munthu wadzanja lolumalayo, “Tanyamuka ndipo uyime patsogolo pa onsewa.” Choncho iye ananyamuka nayima pamenepo. \p \v 9 Kenaka Yesu anawawuza kuti, \wj “Ndikufunseni, kodi chololedwa pa Sabata ndi chiti: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kuwononga?”\wj* \p \v 10 Iye atawayangʼana onsewo, anati kwa munthuyo, \wj “Wongola dzanja lako.”\wj* Iye anaterodi, ndipo dzanja lake linachiritsidwa. \v 11 Koma iwo anapsa mtima nayamba kukambirana wina ndi mnzake chomwe akanamuchitira Yesu. \s1 Atumwi Khumi ndi Awiri \p \v 12 Tsiku lina, masiku amenewo, Yesu anapita ku phiri kukapemphera ndipo anakhala usiku wonse akupemphera kwa Mulungu. \v 13 Kutacha, anayitana ophunzira ake ndipo anasankha khumi ndi awiri a iwo amene anawayika kukhala atumwi: \v 14 Simoni (amene anamutcha Petro), mʼbale wake wa Andreya, Yakobo, Yohane, Filipo, Bartumeyu, \v 15 Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Simoni amene amatchedwa Zaleti, \v 16 Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikarioti amene anamupereka. \s1 Madalitso ndi Tsoka \p \v 17 Iye anatsika pamodzi ndi atumwiwo ndipo anayima pamalo athyathyathya. Gulu lalikulu la ophunzira ake, gulu lalikulu la anthu ochokera ku Yudeya konse, ku Yerusalemu ndi ochokera mʼmphepete mwa nyanja ya Turo ndi Sidoni anali pomwepo. \v 18 Iwo anabwera kudzamvetsera ndi kuchiritsidwa ku matenda awo. Osautsidwa ndi mizimu yoyipa anachiritsidwa, \v 19 ndipo anthu ankayesetsa kuti amukhudze chifukwa mphamvu imatuluka mwa Iye ndi kuchiritsa onse. \p \v 20 Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati, \q1 \wj “Odala ndinu amene ndi osauka,\wj* \q2 \wj chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.\wj* \q1 \v 21 \wj Inu amene mukumva njala tsopano, ndinu odala\wj* \q2 \wj chifukwa mudzakhutitsidwa.\wj* \q1 \wj Inu amene mukulira tsopano, ndinu odala\wj* \q2 \wj chifukwa mudzasekerera.\wj* \q1 \v 22 \wj Ndinu odala, anthu akamakudani,\wj* \q2 \wj kukusalani ndi kukunyozani\wj* \q2 \wj ndi kumayipitsa dzina lanu chifukwa cha Mwana wa Munthu.\wj* \p \v 23 \wj “Nthawi imeneyo sangalalani ndipo lumphani ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba. Pakuti ndi zomwezonso zimene makolo awo anachitira aneneri.\wj* \q1 \v 24 \wj “Ndinu atsoka, anthu olemera,\wj* \q2 \wj popeza mwalandiriratu zokusangalatsani.\wj* \q1 \v 25 \wj Tsoka inu amene mukudya bwino tsopano,\wj* \q2 \wj chifukwa mudzakhala ndi njala.\wj* \q1 \wj Ndinu atsoka, amene mukusekerera tsopano,\wj* \q2 \wj chifukwa mudzabuma ndi kulira.\wj* \q1 \v 26 \wj Ndinu atsoka, anthu akamakuyamikirani,\wj* \q2 \wj popeza makolo anu anawachitira aneneri onama zomwezi.”\wj* \s1 Kukonda Adani \p \v 27 \wj “Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani.\wj* \v 28 \wj Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani.\wj* \v 29 \wj Ngati wina akumenyani patsaya limodzi mupatseninso tsaya linalo. Ngati wina akulanda mwinjiro wako, umulole atenge ndi mkanjo omwe.\wj* \v 30 \wj Mupatseni aliyense amene akupemphani kanthu ndipo ngati wina atenga chinthu chanu, musamulamule kuti akubwezereni.\wj* \v 31 \wj Inu muwachitire anthu ena, zomwe mukanafuna kuti iwo akuchitireni.\wj* \p \v 32 \wj “Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amakonda amene amawakondanso.\wj* \v 33 \wj Ndipo ngati muchita zabwino kwa amene ndi abwino kwa inu, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amachita izi.\wj* \v 34 \wj Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse.\wj* \v 35 \wj Koma kondani adani anu, achitireni zabwino, akongozeni koma osayembekezera kulandira kanthu. Pamenepo mphotho yanu idzakhala yayikulu ndipo inu mudzakhala ana a Wammwambamwamba, chifukwa ndi wokoma mtima kwa anthu osayamika ndi oyipa.\wj* \v 36 \wj Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo.”\wj* \s1 Za Kuweruza Ena \p \v 37 \wj “Musaweruze, ndipo inu simudzaweruzidwa. Musatsutse ndipo inu simudzatsutsidwa. Khululukirani ena ndipo mudzakhululukidwa.\wj* \v 38 \wj Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.”\wj* \p \v 39 Iye anawawuzanso fanizo ili, \wj “Kodi munthu wakhungu angatsogolere munthu wakhungu mnzake? Kodi onse sadzagwera mʼdzenje?\wj* \v 40 \wj Wophunzira sangapose mphunzitsi wake, koma yense amene waphunzitsidwa bwinobwino adzakhala ngati mphunzitsi wake.\wj* \p \v 41 \wj “Kodi ndi chifukwa chiyani mumaona kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu ndi kusasamala mtengo uli mʼdiso mwanu?\wj* \v 42 \wj Kodi munganene bwanji kwa mʼbale wanu kuti, ‘Mʼbale nʼtakuchotsa kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene inu eni ake mukulephera kuona mtengo uli mʼdiso mwanu? Inu achiphamaso, yambani mwachotsa mtengo uli mʼdiso mwanu, ndipo kenaka mudzaona bwinobwino ndi kuchotsa kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu.”\wj* \s1 Mtengo ndi Zipatso Zake \p \v 43 \wj Palibe mtengo wabwino umene umabala chipatso choyipa, kapena mtengo oyipa umene umabala chipatso chabwino.\wj* \v 44 \wj Mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake. Anthu sathyola nkhuyu pa mtengo waminga, kapena mphesa pa nthungwi.\wj* \v 45 \wj Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zosungidwa mu mtima mwake, koma munthu oyipa amatulutsa zinthu zoyipa zosungidwa mu mtima mwake. Pakamwa pake pamayankhula zimene zadzaza mu mtima mwake.\wj* \s1 Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa \p \v 46 \wj “Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena?\wj* \v 47 \wj Ine ndidzakuonetsani mmene alili munthu amene amabwera kwa Ine ndi kumva mawu anga ndi kuwachita.\wj* \v 48 \wj Iye ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama nayika maziko ake pa mwala. Madzi osefukira atabwera ndi mphamvu, nawomba nyumbayo koma sinagwedezeka, chifukwa anayimanga bwino.\wj* \v 49 \wj Koma amene amamva mawu anga koma osawachita, akufanana ndi munthu amene anamanga nyumba yake koma yopanda maziko. Nthawi yomwe madziwo anawomba nyumbayo, inagwa ndipo inawonongekeratu.”\wj* \c 7 \s1 Chikhulupiriro cha Kenturiyo \p \v 1 Yesu atamaliza kunena zonsezi pamaso pa anthu amene ankamvetsera, analowa mu Kaperenawo. \v 2 Kumeneko wantchito wa Kenturiyo, amene amamukhulupirira kwambiri, anadwala ndipo anali pafupi kufa. \v 3 Kenturiyo anamva za Yesu ndipo anatumiza ena a akulu Ayuda kwa Iye kuti abwere adzachiritse wantchito wakeyo. \v 4 Iwo atafika kwa Yesu, anamudandaulira kwambiri, nati, “Munthuyu ayenera kuthandizidwa \v 5 chifukwa amakonda mtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge wathu.” \v 6 Pamenepo Yesu anapita nawo. \p Iye sanali patali ndi nyumba pamene Kenturiyo anatumiza anzake kuti akamuwuze kuti, “Ambuye, musadzivutitse, pakuti ndine wosayenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga. \v 7 Nʼchifukwa chake sindinadziyenereze ndi pangʼono pomwe kuti ndibwere kwa inu. Koma nenani mawu, ndipo wantchito wanga adzachira. \v 8 Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita.” \p \v 9 Yesu atamva izi, anadabwa naye, ndipo anatembenukira gulu la anthu limene limamutsatira nati, \wj “Ndikukuwuzani kuti, sindinapeze chikhulupiriro chachikulu ngati ichi mu Israeli.”\wj* \v 10 Kenaka anthu amene anatumidwawo anabwerera ku nyumba ndipo anakamupeza wantchitoyo atachira. \s1 Yesu Aukitsa Mwana wa Mayi Wamasiye \p \v 11 Zitangotha izi, Yesu anapita ku mudzi wa Naini ndipo ophunzira ake ndi gulu lalikulu la anthu linapita naye pamodzi. \v 12 Akufika pa chipata cha mudziwo, anakumana ndi anthu amene ankatuluka ndi munthu wakufa amene anali mwana yekhayo wa mkazi wamasiye. Gulu lalikulu la anthu a mʼmudziwo linali naye. \v 13 Ambuye atamuona mayiyo, mtima wawo unagwidwa naye chifundo ndipo anati, \wj “Usalire.”\wj* \p \v 14 Kenaka anapita nakakhudza chithatha cha maliro ndipo amene anachinyamulawo anayima. Iye anati, \wj “Mnyamata, ndikukuwuza kuti, dzuka!”\wj* \v 15 Wakufayo anakhala tsonga ndi kuyamba kuyankhula, ndipo Yesu anamupereka mnyamatayo kwa amayi ake. \p \v 16 Onse anachita mantha kwambiri nalemekeza Mulungu. Iwo anati, “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu. Mulungu wabwera kudzathandiza anthu ake.” \v 17 Mbiriyi inafalikira ku Yudeya konse ndi ku madera ozungulira. \s1 Yesu ndi Yohane Mʼbatizi \p \v 18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuwuza Yohaneyo zinthu zonsezi. Atayitana awiri a ophunzirawo, \v 19 anawatumiza kwa Ambuye kukafunsa kuti, “Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?” \p \v 20 Anthuwo atafika kwa Yesu anati, “Yohane Mʼbatizi watituma kwa Inu kuti tidzafunse kuti, ‘Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?’ ” \p \v 21 Pa nthawi yomweyo, Yesu anachiritsa ambiri amene ankavutika, odwala ndi amene anali mizimu yoyipa, ndiponso anapenyetsa anthu osaona. \v 22 Ndipo Iye anawayankha otumidwawo kuti, \wj “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwaona ndi kumva: Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka.\wj* \v 23 \wj Odala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”\wj* \p \v 24 Anthu otumidwa ndi Yohane aja atachoka, Yesu anayamba kuyankhula ndi gulu la anthu za Yohaneyo kuti, \wj “Kodi munkapita ku chipululu kukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo?\wj* \v 25 \wj Ngati si choncho, munkapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zabwino? Ayi, ovala zovala zodula ndi okhala moyo wapamwamba ali mʼnyumba zaufumu.\wj* \v 26 \wj Koma inu munkapita kukaona chiyani? Mneneri? Inde, Ine ndikukuwuzani, woposa mneneri.\wj* \v 27 \wj Uyu ndi amene malemba akunena za Iye kuti,\wj* \q1 \wj “ ‘Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,\wj* \q2 \wj amene adzakonza njira yanu.’\wj* \m \v 28 \wj Ine ndikukuwuzani kuti pakati pa obadwa kuchokera mwa mkazi palibe wina wamkulu kuposa Yohane; komabe amene ali wamngʼono mu ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.”\wj* \p \v 29 Anthu onse, ngakhale amisonkho, atamva mawu a Yesu, anavomereza kuti njira ya Mulungu ndi yolondola, chifukwa anabatizidwa ndi Yohane. \v 30 Koma Afarisi ndi akatswiri amalamulo anakana cholinga cha Mulungu kwa iwo okha, chifukwa sanabatizidwe ndi Yohane. \p \v 31 \wj “Kodi ndingawafanizire chiyani anthu a mʼbado uno? Ali ngati chiyani?\wj* \v 32 \wj Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti,\wj* \q1 \wj “ ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro,\wj* \q2 \wj koma inu simunavine.\wj* \q1 \wj Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro,\wj* \q2 \wj koma inu simunalire.’\wj* \m \v 33 \wj Pakuti Yohane Mʼbatizi sanabwere kudzadya buledi kapena kumwa vinyo, koma inu mumati, ‘Ali ndi chiwanda.’\wj* \v 34 \wj Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’\wj* \v 35 \wj Ndipo nzeru zimaoneka zolondola mwa ana ake onse.”\wj* \s1 Yesu Adzozedwa ndi Mayi Wochimwa \p \v 36 Tsopano mmodzi mwa Afarisi anayitana Yesu kuti akadye naye ku nyumba kwake ndipo anapita nakakhala pa tebulo. \v 37 Mayi amene amakhala moyo wauchimo mu mzindawo atadziwa kuti Yesu akudya ku nyumba ya Mfarisiyo, anabweretsa botolo la mafuta onunkhira a alabasta. \v 38 Iye anayimirira kumbuyo kwa Yesu pa mapazi ake akulira, nayamba kumadontheza misozi pa mapazi ake. Ndipo iye anapukuta mapaziwo ndi tsitsi lake, nawapsompsona ndi kuwathira mafuta onunkhirawo. \p \v 39 Mfarisiyo anamuyitanayo ataona izi, anati mu mtima mwake, “Ngati munthuyu akanakhala mneneri, akanadziwa kuti akumukhudzayo ndi mayi otani, kuti ndi wochimwa.” \p \v 40 Yesu anamuyankha iye kuti, \wj “Simoni, ndili ndi kanthu koti ndikuwuze.”\wj* \p Iye anati, “Ndiwuzeni Aphunzitsi.” \p \v 41 \wj “Anthu awiri anakongola ndalama kwa munthu wina wokongoletsa ndalama: mmodzi ndalama zokwana 500 ndi winayo ndalama makumi asanu.\wj* \v 42 \wj Panalibe mmodzi mwa iwo anali ndi ndalama zobwezera, ndipo iye anawakhululukira ngongole zawo. Tsopano ndi ndani mwa awiriwa adzamukonde koposa?”\wj* \p \v 43 Simoni anayankha kuti, “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira ngongole yayikulu.” \p Yesu anati, \wj “Wayankha molondola.”\wj* \p \v 44 Kenaka anatembenukira kwa mayiyo nati kwa Simoni, \wj “Ukumuona mayiyu? Ine ndabwera mʼnyumba yako. Iwe sunandipatse madzi otsukira mapazi anga, koma iyeyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake.\wj* \v 45 \wj Iwe sunandipsompsone, koma mayiyu, kuyambira pamene Ine ndalowa, sanaleke kupsompsona mapazi anga.\wj* \v 46 \wj Iwe sunadzoze mutu wanga mafuta, koma iye wadzoza mapazi anga mafuta onunkhira.\wj* \v 47 \wj Tsono, ndikukuwuza iwe, machimo ake amene ndi ambiri akhululukidwa, monga chaonetsera chikondi chake chachikulu. Koma iye amene wakhululukidwa zochepa amakonda pangʼono.”\wj* \p \v 48 Kenaka anati kwa mayiyo, \wj “Machimo ako akhululukidwa.”\wj* \p \v 49 Alendo enawo anayamba kumanena mʼmitima mwawo kuti, “Uyu ndi ndani amene akhululukiranso machimo?” \p \v 50 Yesu anati kwa mayiyo, \wj “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa. Pita mu mtendere.”\wj* \c 8 \s1 Fanizo la Wofesa \p \v 1 Zitatha izi, Yesu anayendayenda kuchoka mzinda wina kupita wina ndiponso mudzi wina kupita wina, akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi awiri aja anali naye, \v 2 komanso akazi ena amene anachiritsidwa ku mizimu yoyipa ndi matenda: Mariya, wotchedwa Magadalena, amene mwa iye munatuluka ziwanda zisanu ndi ziwiri; \v 3 Yohana mkazi wa Kuza, woyangʼanira mʼnyumba ya Herode; Suzana; ndi ena ambiri analinso. Akazi awa ankawathandiza ndi chuma chawo. \p \v 4 Anthu ambiri ankasonkhana, ndipo pamene anthu ankabwera kwa Yesu kuchokera ku midzi, Iye anawawuza fanizo ili, \v 5 \wj “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya.\wj* \v 6 \wj Zina zinagwa pa thanthwe, ndipo pamene zinamera, zinafota chifukwa panalibe chinyezi.\wj* \v 7 \wj Mbewu zina zinagwera pakati pa minga, zinakulira pamodzi ndi mingazo ndipo zinalepheretsa mmerawo kukula.\wj* \v 8 \wj Mbewu zina zinagwera pa nthaka yabwino. Zinamera ndipo zinabala mowirikiza 100 kuposa zimene zinafesedwa zija.”\wj* \p Atanena izi, anafuwula kuti, \wj “Amene ali ndi makutu, amve.”\wj* \p \v 9 Ophunzira ake anamufunsa tanthauzo lake la fanizolo. \v 10 Iye anati, \wj “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti,\wj* \q1 \wj “ngakhale akuona, asapenye;\wj* \q2 \wj ngakhale akumva, asazindikire.”\wj* \p \v 11 \wj “Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu.\wj* \v 12 \wj Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa.\wj* \v 13 \wj Mbewu za pa thanthwe ndi anthu amene amalandira mawu mwachimwemwe pamene akumva, koma mawuwo sazika mizu. Iwo amakhulupirira kwa kanthawi, koma pa nthawi ya mayesero, amagwa.\wj* \v 14 \wj Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima.\wj* \v 15 \wj Koma mbewu za pa nthaka yabwino zikuyimira anthu amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, amene amamva mawu nawasunga, ndipo amalimbikira mpaka amabala zipatso.\wj* \s1 Nyale ndi Choyikapo Chake \p \v 16 \wj “Palibe amayatsa nyale ndi kuyibisa mu mtsuko kapena kuyika pansi pa bedi. Koma mʼmalo mwake, amayika pa choyikapo chake, kuti anthu olowamo aone kuwala.\wj* \v 17 \wj Pakuti palibe kanthu kobisika kamene sikadzawululika, ndipo palibe kanthu kophimbika kamene sikadzadziwika kapena kuonetsedwa poyera.\wj* \v 18 \wj Choncho ganizirani mozama. Iye amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, iye amene alibe, ngakhale chimene akuganiza kuti ali nacho adzalandidwa.”\wj* \s1 Amayi ndi Abale a Yesu \p \v 19 Tsopano amayi ndi abale a Yesu anabwera kudzamuona Iye, koma analephera kuti afike pafupi ndi Iye chifukwa cha gulu la anthu. \v 20 Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunja, akufuna kukuonani.” \p \v 21 Yesu anayankha kuti, \wj “Amayi ndi abale anga ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kumachita zimene mawuwo akunena.”\wj* \s1 Yesu Aletsa Namondwe \p \v 22 Tsiku lina Yesu anati kwa ophunzira ake, \wj “Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja.”\wj* Ndipo analowa mʼbwato nanyamuka. \v 23 Akuwoloka, Iye anagona tulo. Namondwe wamkulu anayamba pa nyanja, ndipo bwatolo linayamba kudzaza ndi madzi ndipo anali pa chiopsezo chachikulu. \p \v 24 Ophunzira anapita ndi kukamudzutsa Iye, nati, “Ambuye, Ambuye, ife tikumira!” \p Anadzuka ndipo anadzudzula mphepo ndi madzi owindukawo. Namondwe anasiya, ndipo panali bata. \v 25 Iye anafunsa ophunzira ake kuti, \wj “Chikhulupiriro chanu chili kuti?”\wj* \p Koma pogwidwa ndi mantha ndi kudabwa anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndi ndani? Iye alamulira ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera Iye.” \s1 Achiritsidwa Munthu Wogwidwa ndi Ziwanda \p \v 26 Iwo anawolokera ku chigawo cha Gerasa chimene chili tsidya lina la nyanja kuchokera ku Galileya. \v 27 Yesu ataponda pa mtunda, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi ziwanda wochokera mu mzindawo. Kwa nthawi yayitali munthuyu sanavale zovala kapena kukhala mʼnyumba, koma amakhala ku manda. \v 28 Iye ataona Yesu, anakuwa nagwa pa mapazi ake akufuwula kwambiri kuti, “Mukufuna chiyani ndi ine, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikupemphani Inu, musandizunze ine!” \v 29 Pakuti Yesu analamula mzimu woyipawo kuti utuluke mwa munthuyo. Kawirikawiri umamugwira iye, ndipo ngakhale anali womangidwa ndi unyolo dzanja ndi mwendo ndi kuti ankamuyangʼanira, koma amadula maunyolo akewo ndipo ziwanda zimamutengera kumalo a yekha. \p \v 30 Yesu anamufunsa kuti, \wj “Dzina lako ndani?”\wj* \p Iye anayankha kuti, “Legiyo,” chifukwa ziwanda zambiri zinalowa mwa iye. \v 31 Ndipo ziwandazo zimamupempha mobwerezabwereza kuti asazitumize ku dzenje la mdima. \p \v 32 Gulu lalikulu la nkhumba limadya pamenepo mʼmbali mwa phiri. Ziwandazo zinamupempha Yesu kuti azilole kuti zikalowe mu nkhumbazo ndipo Iye anazilola. \v 33 Ziwanda zija zitatuluka mwa munthuyo, zinakalowa mwa nkhumbazo, ndipo gulu lonselo linathamangira ku mtsetse ndi kukalowa mʼnyanja ndi kumira. \p \v 34 Oweta nkhumbazo ataona zimene zinachitikazo, anathamanga ndi kukanena izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi. \v 35 Ndipo anthu anapita kukaona zimene zinachitika. Atafika kwa Yesu, anapeza munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja atakhala pa mapazi a Yesu, atavala ndipo ali ndi nzeru zake; ndipo iwo anachita mantha. \v 36 Amene anaona izi anawuza anthu mmene munthu wogwidwa ndi ziwandayo anachiritsidwira. \v 37 Kenaka anthu onse a ku chigawo cha Gerasa anamupempha Yesu kuti achoke kwa iwo, chifukwa anadzazidwa ndi mantha. Choncho Iye analowa mʼbwato nachoka. \p \v 38 Munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja, anapempha Yesu kuti apite nawo, koma Yesu anamubweza nati, \v 39 \wj “Bwerera kwanu kafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.”\wj* Ndipo munthuyo anachoka ndi kukanena ku mzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira iye. \s1 Mwana Wamkazi wa Yairo ndi Mayi Wokhudza Chovala cha Yesu \p \v 40 Yesu atabwerera, gulu lalikulu la anthu linamulandira, chifukwa onse ankamuyembekezera. \v 41 Nthawi yomweyo munthu wotchedwa Yairo, woweruza wa mu sunagoge, anabwera ndi kugwa pa mapazi a Yesu, namupempha Iye kuti apite ku nyumba kwake, \v 42 chifukwa mwana wake yekhayo wamkazi, kamtsikana ka zaka khumi ndi ziwiri, kanali pafupi kufa. \p Pamene Yesu ankapita gulu la anthu linkamupanikiza. \v 43 Ndipo pomwepo panali mayi wina amene ankataya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, koma panalibe wina akanamuchiritsa. \v 44 Iye anafika kumbuyo kwake ndi kukhudza mothera mwa chovala chake, ndipo nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka. \p \v 45 Yesu anafunsa kuti, \wj “Wandikhudza ndani?”\wj* \p Onse atakana, Petro anati, “Anthu akukupanikizani ndi kukukankhani.” \p \v 46 Koma Yesu anati, \wj “Wina wandikhudza; ndikudziwa chifukwa mphamvu yachoka mwa Ine.”\wj* \p \v 47 Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo. \v 48 Kenaka anati kwa iye, \wj “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere.”\wj* \p \v 49 Pamene Yesu ankayankhulabe, munthu wina anabwera kuchokera ku nyumba ya Yairo, woweruza wa ku sunagoge uja. Iye anati, “Mwana wanu wa mkazi wamwalira, musawavutitsenso Aphunzitsiwa.” \p \v 50 Atamva zimenezi, Yesu anati kwa Yairo, \wj “Usachite mantha, ingokhulupirira basi ndipo adzachiritsidwa.”\wj* \p \v 51 Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo. \v 52 Pa nthawiyi nʼkuti anthu onse akubuma ndi kumulirira iye. Yesu anati, \wj “Lekani kulira, sanafe koma wagona tulo.”\wj* \p \v 53 Iwo anamuseka podziwa kuti anali atamwalira. \v 54 Koma Iye anamugwira dzanja lake ndipo anati, \wj “Mwana wanga, dzuka!”\wj* \v 55 Mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anayimirira. Kenaka Yesu anawawuza kuti amupatse chakudya. \v 56 Makolo ake anadabwa, koma Iye anawalamulira kuti asawuze wina aliyense zimene zinachitikazo. \c 9 \s1 Yesu Atuma Ophunzira ake Khumi ndi Awiri \p \v 1 Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda. \v 2 Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala. \v 3 Iye anawawuza kuti, \wj “Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera.\wj* \v 4 \wj Nyumba iliyonse imene mulowa, mukhale momwemo kufikira mutachoka mu mzindawo.\wj* \v 5 \wj Ngati anthu sakulandirani, sasani fumbi la kumapazi anu pomwe mukuchoka mu mzinda wawo ngati umboni owatsutsa.”\wj* \v 6 Ndipo iwo ananyamuka napita, mudzi ndi mudzi, kulalikira Uthenga Wabwino ndi kuchiritsa anthu paliponse. \p \v 7 Tsopano Herode olamulirayo anamva zonse zimachitikazi. Ndipo iye anavutika kwambiri chifukwa ena amati Yohane waukitsidwa kwa akufa, \v 8 ena amati Eliya waonekera, ndipo ena anatinso mmodzi wa aneneri akalekale waukanso. \v 9 Koma Herode anati, “Ine ndinamudula mutu Yohane. Nanga uyu ndani amene ndikumva zinthu zotere za Iye?” Ndipo iye anayesetsa kuti amuone Iye. \s1 Yesu Adyetsa Anthu 5,000 \p \v 10 Atumwi atabwerera, anamuwuza Yesu zimene anachita. Kenaka Iye anawatenga napita kwa okha ku mudzi wa Betisaida. \v 11 Koma gulu la anthu linadziwa ndipo anamutsatira. Iye anawalandira ndi kuyankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa amene amafuna machiritso. \p \v 12 Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, “Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo.” \p \v 13 Iye anayankha kuti, \wj “Apatseni chakudya kuti adye.”\wj* \p Iwo anayankha kuti, “Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa.” \v 14 (Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000). \p Koma Iye anati kwa ophunzira ake, \wj “Akhazikeni pansi mʼmagulu a anthu pafupifupi makumi asanu.”\wj* \v 15 Ophunzira ake anachita zomwezo ndipo aliyense anakhala pansi. \v 16 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri zija anayangʼana kumwamba, nayamika ndipo anazigawa. Kenaka anazipereka kwa ophunzira ake kuti azipereke kwa anthu. \v 17 Onse anadya nakhuta, ndipo ophunzira ake anatolera madengu khumi ndi awiri odzaza ndi nyenyeswa zomwe zinatsala. \s1 Petro Avomereza Khristu \p \v 18 Nthawi ina pamene Yesu amapemphera malo a yekha ali ndi ophunzira ake, Iye anawafunsa kuti, \wj “Kodi anthu amati Ine ndine yani?”\wj* \p \v 19 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati mmodzi wa aneneri akalekale waukanso.” \p \v 20 Iye anafunsa kuti, \wj “Koma nanga inu mumati Ine ndine yani?”\wj* \p Petro anayankha kuti, “Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.” \s1 Yesu Aneneratu za Imfa yake \p \v 21 Yesu anawachenjeza kwambiri kuti asawuze wina aliyense za izi. \v 22 Ndipo Iye anati, \wj “Mwana wa Munthu ayenera kuzunzika kwambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, Iye ayenera kuphedwa ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa.”\wj* \p \v 23 Ndipo Iye anawuza onse kuti, \wj “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine.\wj* \v 24 \wj Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa.\wj* \v 25 \wj Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini?\wj* \v 26 \wj Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera.\wj* \v 27 \wj Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu.”\wj* \s1 Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri \p \v 28 Patatha pafupifupi masiku asanu ndi atatu Yesu atanena izi, Iye anatenga Petro, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera ku phiri kukapemphera. \v 29 Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri. \v 30 Anthu awiri, Mose ndi Eliya, \v 31 anaonekera mu ulemerero opambana akuyankhulana ndi Yesu. Iwo amayankhulana za kuchoka kwake, kumene Iye anali pafupi kukakwaniritsa ku Yerusalemu. \v 32 Petro ndi anzake anali ndi tulo tambiri, koma atadzuka, iwo anaona ulemerero wake ndi anthu awiri atayima pamodzi ndi Iye. \v 33 Pamene anthuwo ankamusiya Yesu, Petro anati kwa Iye, “Ambuye, ndi chabwino kwa ife kuti tikhale pano. Tiloleni kuti timange misasa itatu, umodzi wanu, umodzi wa Mose ndi umodzi wa Eliya.” (Iye sanadziwe chimene amayankhula). \p \v 34 Pamene Iye ankayankhula, mtambo unaonekera ndi kuwaphimba iwo, ndipo anachita mantha pamene mtambowo unawakuta. \v 35 Mawu anachokera mu mtambomo nati, “Uyu ndi Mwana wanga amene ndamusankha; mumvereni Iye.” \v 36 Atamveka mawuwa, anaona kuti Yesu anali yekha. Ophunzirawo anazisunga izi mwa iwo okha ndipo sanawuze wina aliyense pa nthawiyi za zomwe iwo anaziona. \s1 Kuchiritsidwa kwa Mwana Wogwidwa ndi Chiwanda \p \v 37 Mmawa mwake, akutsika ku phiri, anthu ambiri anakumana naye. \v 38 Munthu wina mʼgulu la anthulo anayitana kuti, “Aphunzitsi, ndikupemphani kuti muone mwana wangayu, pakuti ndi mmodzi yekhayu. \v 39 Chiwanda chikamugwira amafuwula mwadzidzidzi; chimamugwedeza kolimba mpaka kutuluka thovu kukamwa. Sichimusiya ndipo chikumuwononga. \v 40 Ine ndinapempha ophunzira anu kuti achitulutse, koma alephera.” \p \v 41 Yesu anayankha kuti, \wj “Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno.”\wj* \p \v 42 Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake. \v 43 Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu. \s1 Yesu Abwereza Kunena za Imfa yake \p Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake, \v 44 \wj “Tamvetsetsani zimene ndikufuna kukuwuzani: Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.”\wj* \v 45 Koma iwo sanazindikire zimene amatanthauza. Izi zinawadabwitsa kotero sanathe kuzimvetsa ndipo anaopa kumufunsa. \s1 Wamkulu Ndani? \p \v 46 Mkangano unayambika pakati pa ophunzira wa kuti wamkulu koposa akanakhala ndani mwa iwo. \v 47 Yesu podziwa maganizo awo, anatenga kamwana nakayimika pambali pake. \v 48 Ndipo Iye anawawuza kuti, \wj “Aliyense wolandira bwino kamwana aka mʼdzina langa, ndiye kuti akulandiranso bwino Ine; ndipo aliyense wolandira bwino Ine, ndiye kuti akulandiranso bwino amene anandituma Ine. Pakuti amene ndi wamngʼono pakati panu, ndiye amene ali wamkulu koposa.”\wj* \p \v 49 Yohane anati, “Ambuye, ife tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo tinayesa kumuletsa, chifukwa iyeyo si mmodzi wa ife.” \p \v 50 Yesu anati, \wj “Wosamuletsa, pakuti amene satsutsana nanu ali mbali yanu.”\wj* \s1 A Samariya Akana Yesu \p \v 51 Nthawi itayandikira yoti Iye atengedwe kupita kumwamba, Yesu anatsimikiza zopita ku Yerusalemu, \v 52 ndipo anatuma nthumwi kuti zitsogole. Iwo anapita mʼmudzi wa Asamariya kuti akonzekere kumulandira, \v 53 koma anthu kumeneko sanamulandire chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu. \v 54 Ophunzira awa, Yohane ndi Yakobo ataona zimenezi, anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukufuna ife tiyitane moto kuchokera kumwamba kuti uwawononge?” \v 55 Koma Yesu anatembenuka ndi kuwadzudzula, \v 56 ndipo iwo anapita ku mudzi wina. \s1 Kutsatira Yesu \p \v 57 Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, “Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita.” \p \v 58 Yesu anayankha kuti, \wj “Nkhandwe zili ndi mapanga ake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe malo wogonekapo mutu wake.”\wj* \p \v 59 Iye anati kwa wina, \wj “Nditsate Ine.”\wj* \p Koma munthuyo anayankha kuti, “Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga.” \p \v 60 Yesu anati kwa iye, \wj “Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu.”\wj* \p \v 61 Koma winanso anati, “Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa.” \p \v 62 Yesu anayankha kuti, \wj “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”\wj* \c 10 \s1 Yesu Atuma Ophunzira 72 \p \v 1 Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako. \v 2 Iye anawawuza kuti, \wj “Zokolola ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa. Pemphani Ambuye wa zokolola, kuti atumize antchito ku munda wake wa zokolola.\wj* \v 3 \wj Pitani! Ine ndikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu.\wj* \v 4 \wj Musatenge chikwama kapena thumba kapena nsapato; ndipo musalonjere wina aliyense pa njira.\wj* \p \v 5 \wj “Mukamalowa mʼnyumba, poyamba nenani kuti, ‘Mtendere pa nyumba ino.’\wj* \v 6 \wj Ngati mʼnyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere wanuwo udzakhala pa iyeyo; ngati mulibemo, mtendere wanuwo udzabwerera kwa inu.\wj* \v 7 \wj Khalani mʼnyumba yomweyo, idyani ndi kumwa chilichonse chimene akupatsani, pakuti wantchito ayenera kulandira malipiro ake. Musachoke kumene mwafikirako ndi kupita ku nyumba zina.\wj* \p \v 8 \wj “Mukamalowa mʼmudzi, ndi kulandiridwa, idyani chilichonse akukonzerani.\wj* \v 9 \wj Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’\wj* \v 10 \wj Koma mukalowa mʼmudzi ndipo osalandiridwa bwino, kapiteni ku misewu mʼmudzimo nʼkukanena kuti,\wj* \v 11 \wj ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la mʼmudzi wanuwu limene lamamatira ku mapazi athuwa. Komabe dziwani izi: Ufumu wa Mulungu wayandikira.’\wj* \v 12 \wj Ine ndikuwuzani kuti adzachita chifundo polanga Sodomu pa tsikulo kusiyana ndi mudziwo.\wj* \p \v 13 \wj “Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa.\wj* \v 14 \wj Koma adzachita chifundo polanga Turo ndi Sidoni kusiyana ndi inu.\wj* \v 15 \wj Kodi iwe Kaperenawo, adzakukweza mpaka kumwamba? Ayi, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.\wj* \p \v 16 \wj “Womvera inu, akumvera Ine; wokana inu, akukana Ine. Ndipo wokana Ine; akukana Iye amene anandituma Ine.”\wj* \p \v 17 Anthu 72 aja anabwerera ndi chimwemwe ndipo anati, “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera ife mʼdzina lanu.” \p \v 18 Iye anayankha kuti, \wj “Ndinaona Satana akugwa kuchokera kumwamba ngati mphenzi.\wj* \v 19 \wj Ine ndakupatsani ulamuliro woponda njoka ndi zinkhanira, ndi kugonjetsa mphamvu zonse za mdani; palibe chimene chidzakupwetekani.\wj* \v 20 \wj Komabe musakondwere chifukwa mizimu yoyipa inakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu analembedwa kumwamba.”\wj* \p \v 21 Nthawi imeneyo Mzimu Woyera anadzaza Yesu ndi chimwemwe ndipo anati, \wj “Ine ndikulemekeza Inu, Atate Ambuye a kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwawabisira anthu anzeru ndi ophunzira zinthu izi ndipo mwaziwulula kwa ana aangʼono. Inde, Atate, pakuti munachita zimenezi mwachifuniro chanu.\wj* \p \v 22 \wj “Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.”\wj* \p \v 23 Kenaka anatembenukira kwa ophunzira ake nawawuza iwo okha kuti, \wj “Ndi odala maso amene akuona zimene mukuonazi.\wj* \v 24 \wj Pakuti kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu anafunitsitsa kuona zimene mukuonazi koma sanazione, ndi kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.”\wj* \s1 Fanizo la Msamariya Wachifundo \p \v 25 Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” \p \v 26 Yesu anayankha kuti, \wj “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?”\wj* \p \v 27 Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.” \p \v 28 Yesu anayankha kuti, \wj “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”\wj* \p \v 29 Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, “Kodi mnansi wanga ndani?” \p \v 30 Yesu pomuyankha anati, \wj “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa.\wj* \v 31 \wj Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala.\wj* \v 32 \wj Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso.\wj* \v 33 \wj Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni.\wj* \v 34 \wj Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira.\wj* \v 35 \wj Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’\wj* \p \v 36 \wj “Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?”\wj* \p \v 37 Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.” \p Yesu anamuwuza kuti, \wj “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”\wj* \s1 Marita ndi Mariya \p \v 38 Yesu ndi ophunzira ake akuyenda, anafika pa mudzi kumene mayi wotchedwa Marita anamulandira Iye mʼnyumba mwake. \v 39 Mayiyu anali ndi mchemwali wake wotchedwa Mariya, amene anakhala pa mapazi a Yesu kumverera zimene Iye ankanena. \v 40 Koma Marita anatanganidwa ndi zokonzekera zonse zimene zimayenera kuchitika. Iye anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Ambuye, kodi simusamala kuti mchemwali wanga wandisiya kuti ndichite ntchito yonse ndekha? Muwuzeni andithandize!” \p \v 41 Ambuye anati, \wj “Marita, Marita, ukudandaula ndi kuvutika ndi zinthu zambiri,\wj* \v 42 \wj koma chofunika nʼchimodzi chokha. Mariya wasankha chinthu chabwino, ndipo palibe angamulande chimenechi.”\wj* \c 11 \s1 Yesu Aphunzitsa za ku Pemphera \p \v 1 Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.” \p \v 2 Yesu anawawuza kuti, \wj “Pamene mukupemphera muzinena kuti:\wj* \q1 \wj “ ‘Atate,\wj* \q1 \wj dzina lanu lilemekezedwe,\wj* \q1 \wj ufumu wanu ubwere.\wj* \q1 \v 3 \wj Mutipatse chakudya chathu chalero,\wj* \q1 \v 4 \wj mutikhululukire machimo athu,\wj* \q2 \wj monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira.\wj* \q1 \wj Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ ”\wj* \p \v 5 Kenaka anawawuza kuti, \wj “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi,\wj* \v 6 \wj chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’\wj* \p \v 7 \wj “Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’\wj* \v 8 \wj Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.\wj* \p \v 9 \wj “Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani.\wj* \v 10 \wj Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.\wj* \p \v 11 \wj “Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka?\wj* \v 12 \wj Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira?\wj* \v 13 \wj Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”\wj* \s1 Yesu ndi Belezebabu \p \v 14 Yesu amatulutsa chiwanda chimene chinali chosayankhula. Chiwandacho chitatuluka, munthu wosayankhulayo anayankhula, ndipo gulu la anthu linadabwa. \v 15 Koma ena mwa iwo anati, “Iye akutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mfumu ya ziwanda.” \v 16 Ena anamuyesa pomufunsa chizindikiro chochokera kumwamba. \p \v 17 Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, \wj “Ufumu uliwonse wogawikana udzawonongeka, ndipo nyumba yogawikana idzapasuka.\wj* \v 18 \wj Ngati Satana adziwukira yekha, ufumu wake ungalimbe bwanji? Ine ndikunena izi chifukwa inu mukuti Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu.\wj* \v 19 \wj Tsopano ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu, nanga ophunzira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Choncho, iwowo ndiye adzakhala oweruza anu.\wj* \v 20 \wj Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika pakati panu.\wj* \p \v 21 \wj “Munthu wamphamvu, amene ali ndi zida, akamalondera nyumba yake, katundu wake amatetezedwa.\wj* \v 22 \wj Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa namugonjetsa, amalanda zida zimene munthuyo amazidalirazo ndi kugawa katundu wake.\wj* \p \v 23 \wj “Munthu amene sali mbali yanga ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ameneyo ndi womwaza.\wj* \s1 Za Mzimu Woyipa \p \v 24 \wj “Mzimu woyipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo owuma, kufunafuna malo opumulirako ndipo suwapeza. Kenaka umati, ‘Ndibwerera ku nyumba kwanga kumene ndachokera.’\wj* \v 25 \wj Ukafika umapeza mʼnyumba mosesedwa bwino ndi mokonza.\wj* \v 26 \wj Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa iwowo ndipo imakalowa ndi kukhala mʼmenemo. Ndipo makhalidwe otsiriza a munthuyo amakhala oyipa kuposa oyamba aja.”\wj* \s1 Munthu Wodala \p \v 27 Pamene Yesu ankanena zonsezi, mayi wina mʼgulu la anthuwo anafuwula nati, “Ndi wodala amayi amene anakubalani ndi kukulerani!” \p \v 28 Koma Yesu anayankha kuti, “\wj Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”\wj* \s1 Chizindikiro cha Yona \p \v 29 Pamene gulu la anthu limachuluka, Yesu anati, \wj “Uno ndi mʼbado oyipa. Umafuna kuona chizindikiro chodabwitsa. Koma sadzachiona kupatula chizindikiro chija cha Yona.\wj* \v 30 \wj Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu ku Ninive, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mʼbado uno.\wj* \v 31 \wj Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi anthu a mʼbado uno ndipo idzawatsutsa, chifukwa iyo inachokera kumapeto a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Solomoni.\wj* \v 32 \wj Anthu a ku Ninive adzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi mʼbado uno ndipo adzawutsutsa, pakuti anatembenuka mtima ndi ulaliki wa Yona. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Yona.\wj* \s1 Nyale ndi Thupi \p \v 33 \wj “Palibe amene amayatsa nyale ndi kuyiika pa malo poti sionekera, kapena pansi pa mtsuko. Mʼmalo mwake amayika pa choyikapo chake, kuti iwo amene akulowamo aone kuwunika.\wj* \v 34 \wj Diso lanu ndi nyale ya thupi lanu. Pamene maso anu ali bwino, thupi lanu lonse limadzaza ndi kuwunika. Koma ngati ali oyipa, thupi lanunso ndi lodzaza ndi mdima.\wj* \v 35 \wj Onetsetsani tsono, kuti kuwunika kuli mwa inu si mdima.\wj* \v 36 \wj Choncho, ngati thupi lanu lonse ndi lodzaza ndi kuwunika, ndiye kuti palibe dera lina lili mdima, lonselo lidzakhala kuwunika, monga momwe kuwunika kwa nyale kumakuwalirani.”\wj* \s1 Tsoka la Afarisi ndi Alembi Amalamulo \p \v 37 Yesu atamaliza kuyankhula, Mfarisi wina anamuyitana kuti akadye naye. Tsono Yesu analowa mʼnyumba ndi kukhala podyera. \v 38 Mfarisiyo anadabwa atazindikira kuti Yesu anayamba kudya wosatsata mwambo wawo wakasambidwe ka mʼmanja. \p \v 39 Kenaka Ambuye anamuwuza kuti, \wj “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkati mwanu ndi modzaza ndi kudzikonda ndi zoyipa.\wj* \v 40 \wj Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga zamʼkati sanapangenso zakunja?\wj* \v 41 \wj Koma popereka kwa osauka, perekani chimene chili mʼkati ndipo chilichonse chidzakhala choyera.\wj* \p \v 42 \wj “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi.\wj* \p \v 43 \wj “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malonje mʼmalo a pa msika.\wj* \p \v 44 \wj “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa muli ngati manda osawaka, amene anthu amangoyendapo, osawadziwa.”\wj* \p \v 45 Mmodzi mwa akatswiri a Malamulo anamuyankha Iye nati, “Aphunzitsi, pamene mukunena zinthu izi, mukutinyoza ifenso?” \p \v 46 Yesu anayankha kuti, \wj “Tsoka kwa inunso akatswiri a Malamulo chifukwa mumawalemetsa anthu ndi mtolo umene iwo sangathe kunyamula, ndipo inu eni ake simutenga chala chanu kuti muwathandize.\wj* \p \v 47 \wj “Tsoka kwa inu, chifukwa mumawaka manda a aneneri, komatu ndi makolo anu amene anawapha.\wj* \v 48 \wj Tsono potero mumachitira umboni za zimene makolo anu anachita. Anapha aneneri, ndipo inu mumawaka manda awo.\wj* \v 49 \wj Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’\wj* \v 50 \wj Choncho mʼbado uwu udzasenza magazi a aneneri onse amene anakhetsedwa kuyambira pachiyambi cha dziko,\wj* \v 51 \wj kuyambira magazi a Abele kufikira magazi a Zakariya amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi malo opatulika. Inde, Ine ndikuwuzani inu, mʼbado uno udzasenza zonsezi.\wj* \p \v 52 \wj “Tsoka kwa inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mwachotsa kiyi wachidziwitso inu eni akenu musanalowemo, ndipo mwatsekerezanso iwo amene amalowa.”\wj* \p \v 53 Pamene Yesu anachokamo, Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo anayamba kumamutsutsa koopsa ndi kumupanikiza ndi mafunso, \v 54 pofuna kumukola muchina chilichonse chimene Iye angayankhule. \c 12 \s1 Chenjezo ndi Chilimbikitso \p \v 1 Nthawi yomweyo, anthu miyandamiyanda atasonkhana, ndi kumapondanapondana, Yesu anayamba kuyankhula poyamba kwa ophunzira ake, nati, \wj “Chenjereni ndi yisiti wa Afarisi, amene ndi chinyengo.\wj* \v 2 \wj Palibe chinthu chophimbika chimene sichidzawululika, kapena chobisika chimene sichidzadziwika.\wj* \v 3 \wj Chimene mwanena mu mdima chidzamveka dzuwa likuwala, ndipo zimene mwanongʼona mʼkhutu mʼchipinda chamʼkati, zidzayankhulidwa pa denga la nyumba.\wj* \p \v 4 \wj “Ine ndikuwuzani, abwenzi anga, musachite mantha ndi amene amapha thupi chifukwa akatero sangachitenso kanthu.\wj* \v 5 \wj Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye.\wj* \v 6 \wj Kodi atimba asanu samagulidwa ndi ndalama ziwiri? Ngakhale zili chomwecho palibe imodzi ya izo imene imayiwalika ndi Mulungu.\wj* \v 7 \wj Ndithudi, tsitsi lonse la mʼmutu mwanu ndi lowerengedwa. Musachite mantha; inu ndi oposa kwambiri mpheta zambiri.\wj* \p \v 8 \wj “Ine ndikukuwuza kuti, aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa Munthu adzamuvomerezanso pamaso pa angelo a Mulungu.\wj* \v 9 \wj Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu adzakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu.\wj* \v 10 \wj Ndipo aliyense amene ayankhulira Mwana wa Munthu mawu oyipa adzakhululukidwa, koma iye wochitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa.\wj* \p \v 11 \wj “Akadzakutengerani ku masunagoge pamaso pa oweruza ndi a maulamuliro, musadere nkhawa mmene mudzadzitchinjirizire nokha kapena chimene mudzayankhule,\wj* \v 12 \wj pakuti Mzimu Woyera nthawi imeneyo adzakuphunzitsani zoyenera kunena.”\wj* \s1 Fanizo la Munthu Wachuma Wopusa \p \v 13 Munthu wina mʼgulu la anthu anati kwa Iye, “Aphunzitsi, muwuzeni mʼbale wanga andigawireko chuma chamasiye.” \p \v 14 Yesu anayankha kuti, \wj “Munthu iwe, ndani anandiyika Ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma pakati panu?”\wj* \v 15 Kenaka Iye anawawuza kuti, \wj “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”\wj* \p \v 16 Ndipo Iye anawawuza fanizo ili, \wj “Munda wa munthu wina wachuma unabereka kwambiri.\wj* \v 17 \wj Iye anaganiza kuti, ‘Ndichite chiyani? Ndilibe malo osungiramo mbewu zanga.’\wj* \p \v 18 \wj “Ndipo Iye anati, ichi ndi chimene ndidzachite: Ndidzaphwasula nkhokwe zanga zonse ndi kumanga zokulirapo, ndipo ndidzasungira mʼmenemo mbewu ndi katundu.\wj* \v 19 \wj Ndipo ndidzawuza moyo wanga kuti, ‘Uli nazo zinthu zabwino zambiri zimene zikhalepo zaka zambiri, usapupulume; idya, imwa ndi kukondwera.’ ”\wj* \p \v 20 \wj “Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Iwe wopusa! Usiku womwe uno moyo wako udzachotsedwa kwa iwe, ndipo ndi ndani amene adzatenge zimene iwe wadzikonzera?’\wj* \p \v 21 \wj “Umu ndi mmene zidzakhalire ndi aliyense amene amadziwunjikira chuma, koma si wachuma pamaso pa Mulungu.”\wj* \s1 Musadere Nkhawa \p \v 22 Kenaka Yesu anati kwa ophunzira ake, \wj “Choncho Ine ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu, zimene mudzadya; kapena za thupi lanu, zimene mudzavala.\wj* \v 23 \wj Moyo uposa chakudya, ndi thupi liposa chovala.\wj* \v 24 \wj Taonani makwangwala: iwo safesa kapena kukolola, alibe nyumba zosungamo zinthu kapena nkhokwe; komabe, Mulungu amawadyetsa. Koposa kotani inu amene ndi ofunikira kuposa mbalame.\wj* \v 25 \wj Ndi ndani wa inu akhoza kuwonjeza ora pa moyo wake chifukwa cha kudandaula?\wj* \v 26 \wj Popeza simungathe kuchita kanthu kakangʼono aka, nʼchifukwa chiyani mumadandaula ndi zinazi?\wj* \p \v 27 \wj “Taonani mmene maluwa amakulira. Iwo sagwira ntchito kapena kusoka zovala. Koma Ine ndikuwuzani kuti, ngakhale Solomoni muulemelero wake wonse sanavalepo ngati limodzi la awa.\wj* \v 28 \wj Ngati umu ndi mmene Mulungu amavekera udzu wakuthengo, umene lero ulipo ndipo mawa uponyedwa pa moto, nanga Iye adzakuvekani inu motani. Haa! Inu achikhulupiriro chochepa!\wj* \v 29 \wj Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa.\wj* \v 30 \wj Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi.\wj* \v 31 \wj Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi.\wj* \s1 Chuma cha Kumwamba \p \v 32 \wj “Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu.\wj* \v 33 \wj Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge.\wj* \v 34 \wj Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”\wj* \s1 Kukhala a Atcheru \p \v 35 \wj “Khalani okonzekeratu ndipo nyale zanu ziziyaka,\wj* \v 36 \wj ngati anthu oyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera kuphwando la ukwati, kuti pamene afika ndi kugogoda akhoza nthawi yomweyo kumutsekulira chitseko.\wj* \v 37 \wj Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo pobwera adzawapeze akudikira. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti adzakonzekera kuwatumikira, adzakhala nawo pa tebulo ndipo adzabwera ndi kuwatumikira.\wj* \v 38 \wj Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo adzawapeze ali okonzeka, ngakhale iye atabwera pa ora lachiwiri kapena lachitatu usiku.\wj* \v 39 \wj Koma zindikirani izi: Ngati mwini nyumba akanadziwa ora limene mbala ibwera, sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe.\wj* \v 40 \wj Inunso muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa ora limene simukumuyembekezera Iye.”\wj* \s1 Wantchito Wokhulupirika ndi Wosakhulupirika \p \v 41 Petro anafunsa kuti, “Kodi mukunena fanizoli kwa ife, kapena kwa aliyense?” \p \v 42 Ambuye anayankha kuti, \wj “Kodi tsono woyangʼanira wokhulupirika ndi wanzeru ndani? Kodi ndi amene mbuye wake wamuyika kukhala oyangʼanira antchito ake kuti aziwapatsa ndalama yachakudya pa nthawi yake yoyenera?\wj* \v 43 \wj Zidzamukhalira bwino wantchito amene mbuye wake adzamupeza akuchita zimene pamene iye abwera.\wj* \v 44 \wj Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense.\wj* \v 45 \wj Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo aziganiza mu mtima mwake kuti, ‘Bwana wanga akuchedwa kwambiri kubwera,’ ndipo kenaka ndi kuyamba kumenya antchito aamuna ndi aakazi ndi kudya, kumwa ndi kuledzera.\wj* \v 46 \wj Mbuye wake adzabwera tsiku limene iye sakumuyembekezera ndi ora limene iye sakudziwa. Iye adzamulanga ndi kumusiya kumalo kumene kuli osakhulupirira.\wj* \p \v 47 \wj “Wantchito amene amadziwa chifuniro cha mbuye wake koma wosakonzeka kapena wosachita chimene mbuye wake akufuna adzakwapulidwa zikwapu zambiri.\wj* \v 48 \wj Koma wantchito amene sadziwa koma nʼkuchita zinthu zoyenera chilango, adzakwapulidwa zikwapu zochepa. Aliyense amene anapatsidwa zambiri, adzayenera kubwezanso zambiri; ndipo amene anamusungitsa zambiri, adzamulamula kuti abweze zambirinso.”\wj* \s1 Za Kugawikana \p \v 49 \wj “Ine ndabwera kudzayatsa moto pa dziko lapansi, ndipo ndikanakonda ukanayaka kale.\wj* \v 50 \wj Koma Ine ndiyenera kubatizidwa, ndipo ndikusautsika mu mtima mpaka utachitika!\wj* \v 51 \wj Kodi mukuganiza kuti Ine ndinabwera kudzabweretsa mtendere pa dziko lapansi? Ayi, Ine ndikukuwuzani kuti, ndinabweretsa kugawikana.\wj* \v 52 \wj Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo mʼbanja limodzi mudzakhala anthu asanu ndipo adzawukirana wina ndi mnzake, atatu kuwukira awiri, ndipo awiri kuwukira atatu.\wj* \v 53 \wj Anthu adzawukirana. Abambo kudzawukira mwana wawo wamwamuna, mwana wawoyo adzawukira abambo ake. Amayi adzawukira mwana wawo wamkazi, mwana wawoyo adzawukira amayi ake. Amayi adzawukira mpongozi wawo wamkazi, mpongoziyo adzawukira amayiwo.”\wj* \s1 Kumasulira Nthawi \p \v 54 Iye anati kwa gulu la anthu, \wj “Pamene mukuona mtambo ukukwera kummawa, nthawi yomweyo inu mumati, ‘kugwa mvula,’ ndipo imagwadi.\wj* \v 55 \wj Ndipo pamene mphepo yakummwera ikuwomba, inu mumati ‘kutentha’ ndipo kumaterodi.\wj* \v 56 \wj Achiphamaso inu! Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a dziko lapansi ndi thambo. Zikutheka bwanji kuti simukudziwa kumasulira kwa nthawi ino?\wj* \p \v 57 \wj “Bwanji simukuzindikira nokha zoyenera kuchita?\wj* \v 58 \wj Pamene mukupita kwa woweruza ndi amene munalakwirana naye, yesetsani kwambiri kuti muyanjane naye mʼnjiramo, chifukwa mukapanda kutero akhoza kukutengerani ku bwalo la milandu ndipo woweruzayo adzakuperekani kwa woyangʼanira ndende, ndipo woyangʼanira ndendeyo adzakuponyani mʼndende.\wj* \v 59 \wj Ine ndikuwuzani kuti, simudzatulukamo mpaka mutalipira ndalama zonse.”\wj* \c 13 \s1 Za Kutembenuka Mtima \p \v 1 Nthawi yomweyo panali ena amene analipo omwe amamuwuza Yesu za Agalileya amene magazi awo Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo. \v 2 Yesu anayankha kuti, \wj “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewa anali ochimwa kwambiri kuposa Agalileya ena onse chifukwa anavutika mʼnjira iyi?\wj* \v 3 \wj Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.\wj* \v 4 \wj Kapena anthu 18 aja amene anafa nsanja ya Siloamu itawagwera, kodi mukuganiza kuti iwo aja anali ochimwa kwambiri kuposa onse amene amakhala mu Yerusalemu?\wj* \v 5 \wj Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.”\wj* \p \v 6 Kenaka Iye anawawuza fanizo kuti, \wj “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu, umene anadzala mʼmunda wamphesa, ndipo Iye anapita kukayangʼana zipatso, koma sanazipeze.\wj* \v 7 \wj Tsono kwa munthu amene amasamalira munda wamphesawo anati, ‘Kwa zaka zitatu tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna chipatso pa mtengo uwu ndipo sindinachipeze. Udule! Nʼchifukwa chiyani ukuwononga nthaka?’\wj* \p \v 8 \wj “Munthuyo anayankha kuti, ‘Bwana, tawusiyani kwa chaka chimodzi chokha ndipo ine ndikumba ngalande mozungulira ndi kuthira manyowa.\wj* \v 9 \wj Ngati udzabale zipatso chaka chamawa, zili bwino! Koma ngati sudzabala, pamenepo mudzawudule.’ ”\wj* \s1 Mayi Wokhota Msana Achiritsidwa pa Sabata \p \v 10 Pa Sabata Yesu ankaphunzitsa mʼsunagoge ina, \v 11 ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe. \v 12 Yesu atamuona anamuyitana kutsogolo ndipo anati kwa iye, \wj “Amayi, mwamasulidwa ku mavuto.”\wj* \v 13 Kenaka anasanjika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo anawongoka nayamika Mulungu. \p \v 14 Chifukwa cha kuyipidwa kuti Yesu anachiritsa pa Sabata, wolamulira sunagoge anati kwa anthu, “Pali masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Choncho bwerani kuti mudzachiritsidwe masiku amenewo osati pa Sabata.” \p \v 15 Ambuye anamuyankha kuti, \wj “Iwe wachiphamaso! Kodi nonsenu simumasula pa Sabata ngʼombe zanu kapena bulu kumuchotsa mʼkhola ndi kupita naye kukamupatsa madzi?\wj* \v 16 \wj Nanga mayiyu, amene ndi mwana wa Abrahamu, ndipo anamangidwa ndi Satana zaka 18, kodi siwoyenera kuti amasulidwe msinga imeneyi pa tsiku la Sabata?”\wj* \p \v 17 Atanena izi, onse omutsutsa anachititsidwa manyazi, koma anthu anakondwera ndi zodabwitsa zonse zimene Iye anazichita. \s1 Fanizo la Mbewu ya Mpiru ndi la Yisiti \p \v 18 Kenaka Yesu anafunsa kuti, \wj “Kodi ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani? Kodi Ine ndingawufanizire ndi chiyani?\wj* \v 19 \wj Uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Inakula, nʼkukhala mtengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinakhala mʼnthambi zake.”\wj* \p \v 20 Iye anafunsanso kuti, \wj “Kodi ufumu wa Mulungu ndingawufanizire ndi chiyani?\wj* \v 21 \wj Uli ngati yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza ndi ufa wambiri mpaka anafufumitsa ufawo.”\wj* \s1 Khomo Lopapatiza \p \v 22 Ndipo Yesu anayendayenda mʼmizinda ndi mʼmidzi, kumaphunzitsa pamene Iye ankapita ku Yerusalemu. \v 23 Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?” \p Iye anawawuza kuti, \v 24 \wj “Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero.\wj* \v 25 \wj Nthawi yomwe mwini nyumba adzayimirira ndi kutseka chitseko, inu mudzayima kunja kugogoda ndi kudandaula kuti, ‘Bwana, tatitsekulirani khomo.’\wj* \p \wj “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera.’\wj* \p \v 26 \wj “Ndipo inu mudzati, tinkadya ndi kumwa ndi inu ndipo munkaphunzitsa mʼmisewu yathu.\wj* \p \v 27 \wj “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera. Chokereni inu nonse ochita zoyipa!’\wj* \p \v 28 \wj “Mudzalira ndi kukuta mano mukadzaona Abrahamu, Isake ndi Yakobo ndi aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu koma inuyo mutaponyedwa kunja.\wj* \v 29 \wj Anthu adzachokera kummawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kummwera, kudzakhala pa phwando mu ufumu wa Mulungu.\wj* \v 30 \wj Ndithudi otsirizira ndiye adzakhale oyambirira, ndipo oyambirira ndiye adzakhale otsirizira.”\wj* \s1 Yesu Amvera Chisoni Yerusalemu \p \v 31 Pa nthawi imeneyo Afarisi anabwera kwa Yesu ndipo anati kwa Iye, “Chokani malo ano ndipo pitani kumalo ena aliwonse. Herode akufuna kukuphani.” \p \v 32 Iye anayankha kuti, \wj “Pitani kawuzeni nkhandweyo, Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa ndipo tsiku lachitatu ndidzakwaniritsa cholinga changa.”\wj* \v 33 \wj Mʼnjira ina iliyonse, Ine ndiyenera kupitirira ulendo wanga lero, mawa ndi mkuja. Zoona nʼzakuti mneneri sangafere kunja kwa Yerusalemu.\wj* \p \v 34 \wj Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri ndi kuwagenda miyala anthu amene atumizidwa kwa iwe. Nthawi zambiri ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune!\wj* \v 35 \wj Taona, nyumba yako yasanduka bwinja. Ine ndikukuwuza kuti, sudzandionanso mpaka pamene udzati, “Wodala amene akubwera mʼdzina la Ambuye!”\wj* \c 14 \s1 Yesu Mʼnyumba ya Mfarisi \p \v 1 Pa tsiku lina la Sabata, Yesu atapita kukadya ku nyumba ya Mfarisi wodziwika, Afarisi anamulonda mosamalitsa. \v 2 Poteropo, patsogolo pake panali munthu amene anadwala matenda otupa mimba ndi miyendo. \v 3 Yesu anafunsa Afarisi ndi akatswiri amalamulo kuti, \wj “Kodi ndi zololedwa kuchiritsa pa tsiku la Sabata kapena ayi?”\wj* \v 4 Koma iwo sanayankhe. Tsono atamutenga munthuyo, Iye anamuchiritsa ndipo anamuwuza kuti azipita. \p \v 5 Kenaka Iye anawafunsa kuti, \wj “Kodi ngati mmodzi mwa inu ali ndi mwana wamwamuna kapena ngʼombe imene yagwera mʼchitsime tsiku la Sabata, kodi simungamuvuwulemo tsiku lomwelo?”\wj* \v 6 Ndipo iwo analibe choyankha. \s1 Kudzichepetsa ndi Kulandira Ulemu \p \v 7 Iye ataona momwe alendo amasankhira malo aulemu pa tebulo, Iye anawawuza fanizo ili: \v 8 \wj “Pamene wina wakuyitanani ku phwando la ukwati, musakhale pa malo aulemu ayi, chifukwa mwina anayitananso munthu wina wolemekezeka kuposa inu.\wj* \v 9 \wj Ngati zitatero, ndiye kuti munthu uja amene anakuyitani inu nonse awiri adzakuwuzani kuti, ‘Mupatseni munthu uyu malo anu.’ Pamenepo inu mudzachita manyazi, pokakhala malo wotsika.\wj* \v 10 \wj Koma akakuyitanani, khalani pa malo otsika, kuti amene anakuyitanani uja adzakuwuzeni kuti, ‘Bwenzi, bwera udzakhale pa malo aulemu pano.’ Pamenepo inu mudzalandira ulemu pamaso pa alendo anzanu onse.\wj* \v 11 \wj Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.”\wj* \p \v 12 Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, \wj “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako.\wj* \v 13 \wj Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona.\wj* \v 14 \wj Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.”\wj* \s1 Fanizo la Phwando Lalikulu \p \v 15 Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, \wj “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.”\wj* \p \v 16 Yesu anayankha kuti, \wj “Munthu wina ankakonza phwando lalikulu ndipo anayitana alendo ambiri.\wj* \v 17 \wj Nthawi yaphwando itakwana anatuma wantchito wake kuti akawuze onse amene anayitanidwa kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’\wj* \p \v 18 \wj “Koma onse anayamba kupereka zifukwa mofanana. Woyamba anati, ‘Ine ndangogula kumene munda, ndipo ndikuyenera kupita kuti ndikawuone. Pepani mundikhululukire.’\wj* \p \v 19 \wj “Wina anati, ‘Ndangogula kumene ngʼombe khumi zokoka ngolo ndipo kupita kukaziyesa. Pepani mundikhululukire.’\wj* \p \v 20 \wj “Wina anatinso, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sinditha kubwera.’\wj* \p \v 21 \wj “Wantchitoyo anabwera ndikudzamuwuza bwana wakeyo zimenezi. Pamenepo mphwandoyo anapsa mtima ndipo analamula wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msangamsanga kunja mʼmisewu ndi mʼmakwalala a mu mzinda ndipo ukabweretse osauka, ofa ziwalo, osaona ndi olumala.’\wj* \p \v 22 \wj “Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’\wj* \p \v 23 \wj “Ndipo mbuye uja anawuza wantchito wake kuti, ‘Pita kunja ku misewu ikuluikulu ndi kunja kwa mpanda ndipo ukawawuze kuti alowe, kuti nyumba yanga idzaze.\wj* \v 24 \wj Ine ndikukuwuzani inu kuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anayitanidwa adzalawa phwandolo.’ ”\wj* \s1 Dipo la Kutsatira Yesu \p \v 25 Gulu lalikulu la anthu linkayenda naye Yesu ndipo atatembenukira kwa iwo anati, \v 26 \wj “Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga.\wj* \v 27 \wj Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.\wj* \p \v 28 \wj “Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire?\wj* \v 29 \wj Pakuti ngati ayika maziko ndi kulephera kutsiriza, aliyense amene adzayiona adzamuseka,\wj* \v 30 \wj nanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba kumanga koma sanathe kutsiriza.’\wj* \p \v 31 \wj “Kapena mfumu imene ikupita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, kodi siyamba yakhala pansi ndi kulingalira ngati ingathe ndi anthu 10,000 kulimbana ndi amene akubwera ndi 20,000?\wj* \v 32 \wj Ngati singathe, idzatuma nthumwi pomwe winayo ali kutali ndi kukapempha mgwirizano wamtendere.\wj* \v 33 \wj Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga.\wj* \p \v 34 \wj “Mchere ndi wabwino, koma ngati usukuluka adzawukoleretsanso ndi chiyani?\wj* \v 35 \wj Suyeneranso ngakhale mʼnthaka kapena kudzala la manyowa; umatayidwa kunja.\wj* \p \wj “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”\wj* \c 15 \s1 Fanizo la Nkhosa Yotayika \p \v 1 Tsopano amisonkho ndi “ochimwa” ankasonkhana kudzamvera mawu ake. \v 2 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amangʼungʼudza nati, “Munthu uyu amalandira ochimwa ndi kudya nawo.” \p \v 3 Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili: \v 4 \wj “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza?\wj* \v 5 \wj Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe\wj* \v 6 \wj ndi kupita kwawo. Kenaka amayitana anzake ndi anansi pamodzi, ndi kuti, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza nkhosa yanga yotayika ija.’\wj* \v 7 \wj Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”\wj* \s1 Fanizo la Ndalama Yotayika \p \v 8 \wj “Kapena tiyeni tifanizire mayi amene anali ndi ndalama zasiliva khumi ndipo imodzi nʼkutayika, kodi sayatsa nyale ndi kusesa mʼnyumba ndi kufuna mosamalitsa mpaka atayipeza?\wj* \v 9 \wj Ndipo pamene wayipeza, amayitana anzake, ndi anansi pamodzi nati, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza ndalama yanga yotayika ija.’\wj* \v 10 \wj Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.”\wj* \s1 Fanizo la Mwana Wolowerera \p \v 11 Yesu anapitiriza kunena kuti, \wj “Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri.\wj* \v 12 \wj Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo.\wj* \p \v 13 \wj “Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko.\wj* \v 14 \wj Iye atawononga zonse, kunagwa njala yoopsa mʼdziko lonselo ndipo anayamba kusauka.\wj* \v 15 \wj Iye anapita kwa nzika ina ya dzikolo nakakhala naye ndi kumagwira ntchito, amene anamutumiza ku munda kukadyetsa nkhumba.\wj* \v 16 \wj Iye analakalaka atakhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumbazo zinkadya, koma panalibe wina amene anamupatsa kanthu.\wj* \p \v 17 \wj “Maganizo ake atabweramo, iye anati, ‘Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala!\wj* \v 18 \wj Ine ndinyamuka ndi kubwerera kwa abambo anga ndipo ndikati kwa iwo: abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi kwa inu.\wj* \v 19 \wj Ndine wosayeneranso kutchedwa mwana wanu; munditenge ngati mmodzi wa antchito anu.’\wj* \v 20 \wj Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake.\wj* \p \wj “Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.\wj* \p \v 21 \wj “Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’\wj* \p \v 22 \wj “Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato.\wj* \v 23 \wj Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera.\wj* \v 24 \wj Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera.\wj* \p \v 25 \wj “Nthawi imeneyi, mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Iye atafika pafupi ndi nyumba, anamva anthu akuyimba ndi kuvina.\wj* \v 26 \wj Ndipo iye anayitana mmodzi wa antchito, namufunsa chimene chimachitika.\wj* \v 27 \wj Iye anayankha kuti, ‘Mʼbale wako wabwera ndipo abambo ako apha mwana wangʼombe wonenepa chifukwa wabwera wamoyo ndipo ali bwino.’\wj* \p \v 28 \wj “Mwana wamkulu anakwiya ndipo anakana kulowa. Chomwecho abambo ake anatuluka ndi kumudandaulira.\wj* \v 29 \wj Koma iye anayankha abambo ake kuti, ‘Taonani! Zaka zonsezi ndakhala ndikukutumikirani kugwira ntchito yowawa ndipo palibe pamene sindinamvere malamulo anu. Koma inu simunandipatse ngakhale mwana wambuzi kuti ine ndichite phwando ndi anzanga.\wj* \v 30 \wj Koma pamene mwana wanu uyu amene wawononga chuma chanu ndi achiwerewere wabwera ku nyumba, inu mwamuphera mwana wangʼombe wonenepa.’ ”\wj* \p \v 31 \wj Abambowo anati, “Mwana wanga, iwe umakhala ndi ine nthawi zonse ndipo zonse ndili nazo ndi zako.\wj* \v 32 \wj Koma tinayenera kukondwera ndi kusangalala, chifukwa mʼbale wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyonso; iye anali wotayika ndipo wapezeka.”\wj* \c 16 \s1 Fanizo la Kapitawo Wosakhulupirika \p \v 1 Yesu anawuza ophunzira ake kuti, \wj “Panali munthu wina wachuma amene kapitawo wake anzake anamuneneza kuti amawononga chuma chakecho.\wj* \v 2 \wj Choncho anamuyitana ndi kumufunsa kuti, ‘Kodi nʼchiyani chimene ndikumva za iwe? Pereka tsatanetsatane wa ntchito yako, pakuti supitirizanso kukhala kapitawo wanga.’\wj* \p \v 3 \wj “Kapitawoyo analingalira kuti, ‘Kodi tsopano ndidzachita chiyani? Bwana wanga andichotsa ntchito. Ine ndilibe mphamvu zokwanira zolimira, komanso ine ndimachita manyazi kupempha.\wj* \v 4 \wj Ine ndikudziwa chimene ndidzachita kotero kuti, pamene ntchito yanga yatha pano, anthu adzandilandire mʼnyumba zawo.’\wj* \p \v 5 \wj “Choncho iye anayitana aliyense amene anali ndi ngongole kwa bwana wake. Iye anafunsa woyamba, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa bwana wanga?’\wj* \p \v 6 \wj “Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’\wj* \p \wj “Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’\wj* \p \v 7 \wj “Kenaka iye anafunsa wachiwiri kuti, ‘Nanga iwe uli ndi ngongole yotani?’\wj* \p \wj “Iye ayankha kuti madengu a tirigu 1,000.\wj* \p \wj “Iye anati, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo ndipo ulembepo 800.’\wj* \p \v 8 \wj “Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika.\wj* \v 9 \wj Ine ndikukuwuzani inu, gwiritsani ntchito chuma cha dziko lapansi kuti mudzipezere nokha abwenzi, kuti pamene chatha mudzalandiridwe mʼmalo okhala amuyaya.\wj* \p \v 10 \wj “Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri.\wj* \v 11 \wj Ndipo ngati simunakhale okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma cha dziko lapansi, ndani amene adzakusungitsani chuma chenicheni?\wj* \v 12 \wj Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi chuma cha mwini wake, ndani amene adzakupatsani katundu wanuwanu?\wj* \p \v 13 \wj “Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.”\wj* \p \v 14 Afarisi amene ankakonda ndalama atamva zimenezi anamuseka Yesu. \v 15 Yesu anawawuza kuti, \wj “Inu ndi amene mumadzilungamitsa nokha pamaso pa anthu, koma Mulungu amadziwa mitima yanu. Zinthu zimene anthu amaziyesa zopambana, ndi zonyansa pamaso pa Mulungu.\wj* \s1 Ziphunzitso Zina \p \v 16 \wj “Malamulo ndi Aneneri zinagwira ntchito mpaka nthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ukulalikidwa, ndipo aliyense akuyesetsa mwamphamvu kuti alowemo.\wj* \v 17 \wj Nʼkwapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kulekana ndi kuti kalemba kakangʼono kachoke mʼMalamulo.\wj* \p \v 18 \wj “Aliyense amene asiya mkazi wake ndi kukakwatira mkazi wina akuchita chigololo, ndipo mwamuna amene akwatira mkazi wosiyidwayo akuchitanso chigololo.”\wj* \s1 Za Munthu Wachuma ndi Lazaro \p \v 19 \wj “Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse.\wj* \v 20 \wj Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse\wj* \v 21 \wj ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake.\wj* \p \v 22 \wj “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda.\wj* \v 23 \wj Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake.\wj* \v 24 \wj Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’\wj* \p \v 25 \wj “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo.\wj* \v 26 \wj Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’\wj* \p \v 27 \wj “Iye anayankha kuti, ‘Ndipo ndikupemphani inu, abambo, mutumeni Lazaro ku nyumba ya abambo anga,\wj* \v 28 \wj pakuti ine ndili ndi abale asanu. Lolani iye akawachenjeze kotero kuti asadzabwere kumalo ano amazunzo.’\wj* \p \v 29 \wj “Abrahamu anayankha kuti, ‘Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.’\wj* \p \v 30 \wj “Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’\wj* \p \v 31 \wj “Anati kwa iye, ‘Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’ ”\wj* \c 17 \s1 Za Uchimo, Chikhulupiriro ndi Ntchito \p \v 1 Yesu anati kwa ophunzira ake, \wj “Zinthu zimene zimachimwitsa sizingalephere kubwera, koma tsoka kwa munthu wozibweretsayo.\wj* \v 2 \wj Kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala wamphero mʼkhosi mwake kusiyana kuti achimwitse mmodzi mwa ana aangʼonowa.\wj* \v 3 \wj Nʼchifukwa chake dziyangʼanireni nokha.\wj* \p \wj “Ngati mʼbale wanu achimwa, mudzudzuleni, ndipo ngati alapa, mukhululukireni.\wj* \v 4 \wj Ngati iye akulakwira kasanu ndi kawiri pa tsiku, ndipo ngati nʼkubweranso kwa iwe kasanu ndi kawiri nati, ‘Ndalapa,’ umukhululukire.”\wj* \p \v 5 Atumwiwo anati kwa Ambuye, “Kulitsani chikhulupiriro chathu!” \p \v 6 Yesu anayankha kuti, \wj “Ngati muli ndi chikhulupiriro chachingʼono ngati kambewu kampiru, mukhoza kulamula mtengo wamkuyu uwu kuti, ‘Zulidwa ndi kukadzalidwa mʼnyanja,’ ndipo udzakumverani.\wj* \p \v 7 \wj “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu anali ndi wantchito wolima kapena woweta nkhosa, kodi angawuze wantchitoyo atabwera ku munda kuti, ‘Tsopano bwera kuno khala pansi kuti udye?’\wj* \v 8 \wj Kodi sangamuwuze kuti, ‘Konzere chakudya cha madzulo, iweyo ukonzeke ndipo undidikirire pamene ndikudya ndi kumwa; kenaka ukhoza kudya ndi kumwa?’\wj* \v 9 \wj Kodi iye angathokoze wantchitoyo chifukwa chochita chimene anawuzidwa kuchita?\wj* \v 10 \wj Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munawuzidwa, muzinena kuti, ‘Ndife antchito osayenera; tangogwira ntchito yathu basi.’ ”\wj* \s1 Yesu Achiritsa Akhate Khumi \p \v 11 Tsopano Yesu anayenda mʼmalire a pakati pa Samariya ndi Galileya pa ulendo wake wa ku Yerusalemu. \v 12 Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali \v 13 ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!” \p \v 14 Iye atawaona, anati, \wj “Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe.”\wj* Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa. \p \v 15 Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza. \v 16 Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya. \p \v 17 Yesu anafunsa kuti, \wj “Kodi amene anachiritsidwa sanalipo khumi? Nanga asanu ndi anayi ena ali kuti?\wj* \v 18 \wj Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?”\wj* \v 19 Pamenepo anati kwa iye, \wj “Imirira ndipo pita; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe.”\wj* \s1 Za Ufumu wa Mulungu \p \v 20 Ndipo Afarisi atamufunsa Iye kuti, ufumu wa Mulungu udzabwera liti, Yesu anayankha kuti, \wj “Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso,\wj* \v 21 \wj kapenanso kuti anthu adzati, ‘Uwu uli apa,’ kapena ‘Uwo uli apo,’ Pakuti taonani ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”\wj* \p \v 22 Kenaka Iye anati kwa ophunzira ake, \wj “Masiku akubwera pamene inu mudzalakalaka mutaona tsiku limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona.\wj* \v 23 \wj Anthu adzakuwuzani kuti, ‘Uyo ali apoyo!’ kapena ‘Uyu ali apa!’ Musawathamangire iwo.\wj* \v 24 \wj Pakuti monga mphenzi ingʼanima ndi kuwala kuchokera mbali ina ya thambo kufikira inzake, koteronso adzakhala ali Mwana wa Munthu pa tsiku lake.\wj* \v 25 \wj Koma poyamba ayenera kuzunzika mu zambiri ndi kukanidwa ndi mʼbado uno.\wj* \p \v 26 \wj “Monga mmene zinkachitikira nthawi ya Nowa, momwemonso zidzachitikanso nthawi ya Mwana wa Munthu.\wj* \v 27 \wj Anthu ankadya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo. Pomwepo chigumula chinafika ndi kuwawononga onsewo.\wj* \p \v 28 \wj “Zinalinso chimodzimodzi nthawi ya Loti. Anthu ankadya ndi kumwa, kugula ndi kugulitsa, kudzala ndi kumanga.\wj* \v 29 \wj Koma tsiku limene Loti anachoka ku Sodomu, moto ndi sulufule zinavumbwa kuchokera kumwamba ndi kuwawononga onsewo.\wj* \p \v 30 \wj “Zidzakhalanso choncho Mwana wa Munthu akadzaonekera.\wj* \v 31 \wj Tsiku limenelo munthu amene ali pa denga la nyumba yake, ndi katundu wake ali mʼnyumbamo, asadzatsike kukatenga. Chimodzimodzinso, munthu amene adzakhale ali ku munda asadzabwerere kukatenga chilichonse.\wj* \v 32 \wj Kumbukirani mkazi wa Loti!\wj* \v 33 \wj Aliyense amene ayesetsa kusunga moyo wake adzawutaya, ndipo aliyense amene ataya moyo wake adzawusunga.\wj* \v 34 \wj Ine ndikukuwuzani inu, usiku umenewo anthu awiri adzagona pa mphasa imodzi; wina adzatengedwa ndipo wina adzasiyidwa.\wj* \v 35 \wj Amayi awiri adzakhala pamodzi akusinja; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa.\wj* \v 36 \wj Amuna awiri adzakhala akulima mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa.”\wj* \p \v 37 Iwo anafunsa kuti, “Ambuye, kodi zimenezi zidzachitikira kuti?” \p Iye anayankha kuti, \wj “Kumene kuli mtembo, nʼkumene makwangwala amasonkhanako.”\wj* \c 18 \s1 Fanizo la Mayi Wakhama pa Kupempha \p \v 1 Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke. \v 2 Iye anati, \wj “Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu.\wj* \v 3 \wj Ndipo panali mkazi wamasiye mʼmudzimo amene ankabwerabwera kwa iye ndi dandawulo lake kuti, ‘Mundiweruze mlandu mwachilungamo pakati pa ine ndi otsutsana nane.’\wj* \p \v 4 \wj “Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu,\wj* \v 5 \wj koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’ ”\wj* \p \v 6 Ndipo Ambuye anati, \wj “Tamvani zimene woweruza wopanda chilungamoyu wanena.\wj* \v 7 \wj Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira?\wj* \v 8 \wj Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?”\wj* \s1 Fanizo la Mfarisi ndi Wolandira Msonkho \p \v 9 Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse. \v 10 \wj “Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho.\wj* \v 11 \wj Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu.\wj* \v 12 \wj Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’\wj* \p \v 13 \wj “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’\wj* \p \v 14 \wj “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”\wj* \s1 Yesu Adalitsa Ana Aangʼono \p \v 15 Anthu amabweretsanso ana aangʼono kwa Yesu kuti awadalitse. Ophunzira ataona izi, anawadzudzula. \v 16 Koma Yesu anayitana anawo kuti abwere kwa Iye nati, \wj “Lolani ana abwere kwa Ine ndipo musawatsekereze, pakuti ufumu wa Mulungu uli wa anthu otere.\wj* \v 17 \wj Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene salandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono, sadzalowamo.”\wj* \s1 Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu \p \v 18 Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?” \p \v 19 Yesu anamuyankha kuti, \wj “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha.\wj* \v 20 \wj Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”\wj* \p \v 21 Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.” \p \v 22 Yesu atamva izi, anati kwa iye, \wj “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.”\wj* \p \v 23 Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri. \v 24 Yesu anamuyangʼana nati, \wj “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!\wj* \v 25 \wj Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”\wj* \p \v 26 Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?” \p \v 27 Yesu anayankha kuti, \wj “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”\wj* \p \v 28 Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!” \p \v 29 Yesu anawawuza kuti, \wj “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu\wj* \v 30 \wj adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”\wj* \s1 Yesu Aneneratu za Imfa Yake Kachitatu \p \v 31 Yesu anatengera khumi ndi awiriwo pambali ndi kuwawuza kuti, \wj “Taonani ife tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zalembedwa ndi Aneneri za Mwana wa Munthu zidzakwaniritsidwa.\wj* \v 32 \wj Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira,\wj* \v 33 \wj adzamukwapula ndi kumupha. Tsiku lachitatu Iye adzaukanso.”\wj* \p \v 34 Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula. \s1 Yesu Achiritsa Wosaona \p \v 35 Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha, \v 36 anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika. \v 37 Iwo anamuwuza kuti “Yesu wa ku Nazareti akudutsa.” \p \v 38 Iye anayitana mofuwula, “Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!” \p \v 39 Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!” \p \v 40 Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti, \v 41 \wj “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”\wj* \p Iye anayankha kuti, “Ambuye, ine ndifuna ndionenso.” \p \v 42 Yesu anati kwa iye, \wj “Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.”\wj* \v 43 Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu. \c 19 \s1 Zakeyu Apulumutsidwa \p \v 1 Yesu analowa mu Yeriko napitirira. \v 2 Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera. \v 3 Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu. \v 4 Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo. \p \v 5 Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, \wj “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.”\wj* \v 6 Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala. \p \v 7 Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, “Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa.” \p \v 8 Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.” \p \v 9 Yesu anati kwa iye, \wj “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu.\wj* \v 10 \wj Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”\wj* \s1 Antchito Opindula Mosiyana \p \v 11 Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo. \v 12 Iye anati, \wj “Munthu wa banja laufumu anapita ku dziko lakutali kukadzozedwa ufumu ndipo kenaka abwerenso kwawo.\wj* \v 13 \wj Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’\wj* \p \v 14 \wj “Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’\wj* \p \v 15 \wj “Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo.\wj* \p \v 16 \wj “Woyamba anabwera ndipo anati, ‘Bwana ndalama zanu zapindula khumi zina.’\wj* \p \v 17 \wj “Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’\wj* \p \v 18 \wj “Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’\wj* \p \v 19 \wj “Bwana anayankha kuti, ‘Iwe lamulira mizinda isanu.’\wj* \p \v 20 \wj “Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu.\wj* \v 21 \wj Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’\wj* \p \v 22 \wj “Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale?\wj* \v 23 \wj Nanga nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga, kuti ine pobwera, ndidzayitenge ndi chiwongoladzanja?’\wj* \p \v 24 \wj “Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ”\wj* \p \v 25 \wj Iwo anati, “Bwana iyeyu ali nazo kale khumi!”\wj* \p \v 26 \wj Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho.\wj* \v 27 \wj Tsono adani anga aja amene sankafuna kuti ndikhale mfumu yawo, abweretseni pano ndi kuwapha ine ndikuona.”\wj* \s1 Yesu Alowa mu Yerusalemu Mwaulemerero \p \v 28 Yesu atatha kunena izi, anayendabe kupita ku Yerusalemu. \v 29 Iye atayandikira ku Betifage ndi Betaniya pa phiri lotchedwa Olivi, Iye anatuma awiri a ophunzira nati kwa iwo, \v 30 \wj “Pitani mʼmudzi uli patsogolo panu, mukakalowa mʼmudzimo, mukapeza mwana wabulu womangiriridwa amene wina aliyense sanakwerepo. Mukamumasule ndi kubwera naye kuno.\wj* \v 31 \wj Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumumasula mwana buluyo?’ Mukamuwuze kuti, ‘Ambuye akumufuna.’ ”\wj* \p \v 32 Otumidwawo anapita nakamupeza mwana wabulu monga momwe Yesu anawawuzira. \v 33 Pamene ankamasula mwana wabuluyo, eni ake anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukumasula mwana wabuluyo?” \p \v 34 Iwo anayankha kuti, “Ambuye akumufuna.” \p \v 35 Iwo anabweretsa buluyo kwa Yesu, naponya zovala zawo pa bulupo ndi kumukwezapo Yesu. \v 36 Pamene ankapita, anthu anayala zovala zawo mu msewu. \p \v 37 Iye atafika pafupi ndi pamene msewu umatsikira ku phiri la Olivi, gulu lonse la ophunzira linayamba kuyamika Mulungu mwachimwemwe ndi mawu ofuwula chifukwa cha zodabwitsa zonse anaziona. \q1 \v 38 “Yodala mfumu imene ikubwera mʼdzina la Ambuye!” \b \q1 “Mtendere kumwamba ndi ulemerero mmwambamwamba!” \p \v 39 Ena mwa Afarisi mʼgulumo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anu!” \p \v 40 Iye anayankha kuti, \wj “Ine ndikukuwuzani kuti, ngati atakhala chete, miyala idzafuwula.”\wj* \p \v 41 Iye atayandikira ku Yerusalemu ndi kuona mzindawo, anawulirira \v 42 nati, \wj “Iwe ukanadziwa lero lino zinthu zokubweretsera mtendere, koma tsopano zabisikira maso ako.\wj* \v 43 \wj Pakuti masiku adzabwera pamene adani ako adzamanga mitumbira yankhondo nakuzungulira, nadzakutsekereza mbali zonse.\wj* \v 44 \wj Iwo adzakugwetsera pansi, iwe, ana ako onse a mʼkati mwako. Iwo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa unzake, chifukwa sunazindikire nthawi ya kubwera kwa Mulungu.”\wj* \s1 Yesu mʼNyumba ya Mulungu \p \v 45 Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda. \v 46 Iye anawawuza kuti, \wj “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.”\wj* \p \v 47 Tsiku lililonse amaphunzitsa mʼNyumba ya Mulungu. Koma akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi atsogoleri pakati pa anthu amayesetsa kuti amuphe. \v 48 Komabe iwo sanathe kupeza njira ina iliyonse kuti achite izi, chifukwa anthu onse anakhulupirira mawu ake. \c 20 \s1 Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake \p \v 1 Tsiku lina pamene Iye ankaphunzitsa anthu mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu ndi kuphunzitsa Uthenga Wabwino, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, pamodzi ndi akuluakulu anabwera kwa Iye. \v 2 Iwo anati, “Mutiwuze mukuchita izi ndi ulamuliro wayani? Ndani anakupatsani ulamuliro uwu?” \p \v 3 Iye anayankha kuti, \wj “Inenso ndikufunsani, mundiyankhe,\wj* \v 4 \wj ‘Kodi ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena wochokera kwa anthu?’ ”\wj* \p \v 5 Iwo anakambirana pakati pawo ndikuti, “Ngati ife tinena kuti, ‘Kuchokera kumwamba’ Iye akatifunsa kuti, ‘chifukwa chiyani simunamukhulupirire iye?’ \v 6 Koma ngati ife tinena kuti, ‘kuchokera kwa anthu,’ anthu onse atigenda miyala, chifukwa amatsimikiza kuti Yohane anali mneneri.” \p \v 7 Pamenepo iwo anayankha kuti, “Ife sitidziwa kumene unachokera.” \p \v 8 Yesu anati, \wj “Ngakhale Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira zimenezi.”\wj* \s1 Fanizo la Olima Mʼmunda Wamphesa \p \v 9 Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: \wj “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali.\wj* \v 10 \wj Pa nthawi yokolola, iye anatumiza wantchito wake kwa alimi aja kuti amupatseko zina mwa zipatso za munda wamphesawo. Koma alimi aja anamumenya namubweza wopanda kanthu.\wj* \v 11 \wj Iye anatumiza wantchito wina, koma uyunso anamumenya namuchita zachipongwe ndi kumubweza wopanda kanthu.\wj* \v 12 \wj Iye anatumizanso wina wachitatu ndipo iwo anamuvulaza namuponya kunja.\wj* \p \v 13 \wj “Kenaka mwini mundawo anati, ‘Kodi ndichite chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wamwamuna, amene ndimukonda; mwina iwo adzamuchitira ulemu.’\wj* \p \v 14 \wj “Koma alimiwo ataona mwanayo, anakambirananso. Iwo anati, ‘Uyu ndiye wodzamusiyira chumachi. Tiyeni timuphe ndipo chumachi chikhala chathu.’\wj* \v 15 \wj Ndipo anamuponya kunja kwa mundawo ndi kumupha.\wj* \p \wj “Nanga tsono mwini munda wamphesayo adzawatani anthuwa?\wj* \v 16 \wj Iye adzabwera ndi kupha alimi aja ndi kupereka mundawo kwa ena.”\wj* \p Pamene anthu anamva izi, anati, “Musatero ayi.” \p \v 17 Yesu anawayangʼanitsitsa ndipo anafunsa kuti, \wj “Kodi tanthauzo lake ndi chiyani la zimene zinalembedwa kuti,\wj* \q1 \wj “ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana\wj* \q2 \wj wasanduka mwala wa pa ngodya.\wj* \m \v 18 \wj Aliyense amene agwa pa mwalawu adzapweteka, koma iye amene udzamugwera udzamuphwanya.’ ”\wj* \p \v 19 Aphunzitsi amalamulo ndi akulu a ansembe amafuna njira yoti amuphe nthawi yomweyo, chifukwa anadziwa kuti ananena fanizo ili powatsutsa iwo. Koma iwo anali ndi mantha chifukwa cha anthu. \s1 Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara \p \v 20 Pamene ankamulondalonda Iye, iwo anatumiza akazitape amene amaoneka ngati achilungamo. Iwo ankafuna kumutapa mʼkamwa Yesu mu china chilichonse chimene Iye ananena kuti amupereke Iye kwa amene anali ndi mphamvu ndi ulamuliro oweruza. \v 21 Potero akazitapewo anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi, tidziwa kuti mumayankhula ndi kuphunzitsa zimene zili zoonadi, ndi kuti simuonetsa tsankho koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mwachoonadi. \v 22 Kodi ndi bwino kwa ife kumapereka msonkho kwa Kaisara kapena kusapereka?” \p \v 23 Iye anaona chinyengo chawo ndipo anawawuza kuti, \v 24 \wj “Onetseni ndalama. Chithunzi ndi malembawa ndi zayani?”\wj* \p \v 25 Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.” \p Iye anawawuza kuti, \wj “Ndiye perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zimene ndi za Mulungu.”\wj* \p \v 26 Iwo analephera kumupeza cholakwa pa zimene ankayankhula pamaso pa anthu. Ndipo pothedwa nzeru ndi yankho lake, iwo anakhala chete. \s1 Za Kuuka kwa Akufa ndi Ukwati \p \v 27 Ena mwa Asaduki, amene ankanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Yesu ndi funso. \v 28 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. \v 29 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyambayo anakwatira mkazi ndipo anafa wopanda mwana. \v 30 Wachiwiri \v 31 ndipo kenaka wachitatuyo anamukwatira iye, ndipo chimodzimodzi asanu ndi awiri aja anafa osasiya ana. \v 32 Pa mapeto pake mkaziyo anafanso. \v 33 Tsopano, pa nthawi ya kuukanso, kodi mkaziyu adzakhala wayani popeza onse asanu ndi awiri anamukwatirapo?” \p \v 34 Yesu anayankha kuti, \wj “Anthu a mʼbado uno amakwatira ndi kukwatiwa.\wj* \v 35 \wj Koma mʼmoyo umene ukubwerawo, anthu amene adzaukitsidwe kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa.\wj* \v 36 \wj Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa.\wj* \v 37 \wj Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’\wj* \v 38 \wj Mulungu si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo, pakuti kwa Iye onse ali ndi moyo.”\wj* \p \v 39 Ena mwa aphunzitsi amalamulo anayankha kuti, “Mwanena bwino mphunzitsi!” \v 40 Ndipo panalibe wina amene akanalimba mtima kumufunsa Iye mafunso ena. \s1 Khristu ndi Mwana wa Ndani? \p \v 41 Kenaka Yesu anawawuza kuti, \wj “Zikutheka bwanji kuti aziti Khristu ndi mwana wa Davide?\wj* \v 42 \wj Davide mwini wake akunenetsa mʼbuku la Masalimo kuti,\wj* \q1 \wj “Ambuye anati kwa Ambuye anga:\wj* \q2 \wj ‘Khalani ku dzanja langa lamanja,\wj* \q1 \v 43 \wj mpaka Ine nditasandutsa adani anu\wj* \q2 \wj chopondapo mapazi anu?’\wj* \m \v 44 \wj Davide akumutcha Iye ‘Ambuye.’ Nanga zingatheke bwanji kuti Iye akhale mwana wake?”\wj* \s1 Achenjeza za Aphunzitsi Amalamulo \p \v 45 Pamene anthu onse ankamvetsera, Yesu anati kwa ophunzira ake, \v 46 \wj “Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando.\wj* \v 47 \wj Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”\wj* \c 21 \s1 Chopereka cha Mayi Wamasiye \p \v 1 Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu. \v 2 Iye anaonanso mkazi wamasiye wosauka akuyikamo timakopala tiwiri. \v 3 Iye anati, \wj “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa.\wj* \v 4 \wj Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.”\wj* \s1 Zizindikiro za Masiku Otsiriza \p \v 5 Ena mwa ophunzira ake ankachita ndemanga za mmene Nyumba ya Mulungu anayikongoletsera ndi miyala yokongola ndiponso zinthu zina zomwe anthu anapereka kwa Mulungu. Koma Yesu anati, \v 6 \wj “Koma zimene mukuziona panozi, nthawi idzafika pamene ngakhale mwala umodzi omwe sudzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”\wj* \p \v 7 Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi zonsezi zidzachitika liti? Ndipo tidzaonera chiyani kuti zili pafupi kuchitika?” \p \v 8 Iye anayankha kuti, \wj “Chenjerani kuti musanyengedwe. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati ‘Ine ndine Iye’ ndi kuti ‘Nthawi yayandikira.’ Musadzawatsate iwo.\wj* \v 9 \wj Mukadzamva zankhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha. Zinthu izi ziyenera kuchitika poyamba, koma chimaliziro sichidzafika nthawi yomweyo.”\wj* \p \v 10 Kenaka anawawuza kuti, \wj “Mtundu wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu kuwukira ufumu wina.\wj* \v 11 \wj Kudzakhala zivomerezi zazikulu, njala ndi miliri mʼmalo osiyanasiyana, ndi zinthu zoopsa ndi zizindikiro zamphamvu kuchokera kumwamba.\wj* \p \v 12 \wj “Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa.\wj* \v 13 \wj Umenewu udzakhala mwayi wanu ochitira umboni.\wj* \v 14 \wj Koma tsimikizani mtima kuti musadzade nkhawa za momwe mudzadzitchinjirizire.\wj* \v 15 \wj Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa.\wj* \v 16 \wj Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani.\wj* \v 17 \wj Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine.\wj* \v 18 \wj Koma palibe tsitsi limodzi la mʼmutu mwanu lidzawonongeke.\wj* \v 19 \wj Mukadzalimbikira ndiye mudzapeze moyo.\wj* \s1 Kuwonongedwa kwa Yerusalemu \p \v 20 \wj “Mukadzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, inu mudzadziwe kuti kuwonongeka kwake kuli pafupi.\wj* \v 21 \wj Pamenepo amene ali ku Yudeya adzathawire ku mapiri, amene ali mu mzinda adzatulukemo, ndi amene ali ku midzi asadzalowe mu mzinda.\wj* \v 22 \wj Pakuti iyi ndi nthawi yachilango pokwaniritsa zonse zimene zinalembedwa.\wj* \v 23 \wj Zidzakhala zoopsa nthawi imenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! Kudzakhala masautso aakulu mʼdziko ndipo anthu onse adzawakwiyira.\wj* \v 24 \wj Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndi kutengedwa ukapolo kupita ku mayiko wonse. Yerusalemu adzaponderezedwa ndi anthu a mitundu ina mpaka nthawi ya a mitundu ina itakwaniritsidwa.\wj* \p \v 25 \wj “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja.\wj* \v 26 \wj Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha, akadzamva za zimene zikubwera pa dziko lapansi, pakuti zinthu zamlengalenga zidzagwedezeka.\wj* \v 27 \wj Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.\wj* \v 28 \wj Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzayimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”\wj* \s1 Fanizo la Mtengo Wamkuyu \p \v 29 Iye anawawuza fanizo ili, \wj “Taonani mtengo wamkuyu ndi mitengo ina yonse.\wj* \v 30 \wj Ikamatulutsa masamba, mumakhoza kudzionera nokha ndi kudziwa kuti dzinja lili pafupi.\wj* \v 31 \wj Chimodzimodzinso, mukadzaona zinthu zonsezi, dziwani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.\wj* \p \v 32 \wj “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika.\wj* \v 33 \wj Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”\wj* \s1 Za Kukhala Tcheru \p \v 34 \wj “Samalani, kuti mitima yanu ingalemetsedwe ndi maphwando, kuledzera ndi kudera nkhawa za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingadzakupezeni modzidzimutsa ngati msampha.\wj* \v 35 \wj Pakuti lidzafika pa onse okhala pa dziko lonse lapansi.\wj* \v 36 \wj Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu.”\wj* \p \v 37 Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse. \v 38 Ndipo anthu onse amabwera mmamawa kudzamumva Iye ku Nyumba ya Mulungu. \c 22 \s1 Yudasi Avomera Kumupereka Yesu \p \v 1 Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira, \v 2 akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu. \v 3 Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo. \v 4 Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu. \v 5 Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama. \v 6 Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi. \s1 Paska Womaliza \p \v 7 Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe. \v 8 Yesu anatuma Petro ndi Yohane nati, \wj “Pitani kukatikonzera Paska kuti tikadye.”\wj* \p \v 9 Iwo anafunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonzere kuti?” \p \v 10 Iye anayankha kuti, \wj “Taonani, mukamalowa mu mzinda, mudzakumana ndi mwamuna atanyamula mtsuko wamadzi. Mulondoleni ku nyumba imene akalowe,\wj* \v 11 \wj ndipo mukamuwuze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi kufunsa kuti, chili kuti chipinda cha alendo, kumene Ine ndi ophunzira anga tikadyere Paska?’\wj* \v 12 \wj Iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala ndi zonse. Kachiteni zokonzekera mʼmenemo.”\wj* \p \v 13 Iwo anapita nakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Tsono anakonza Paska. \s1 Za Mgonero wa Ambuye \p \v 14 Ora litakwana, Yesu ndi ophunzira ake anakhala pa tebulo. \v 15 Ndipo Iye anawawuza kuti, \wj “Ine ndakhala ndikuyembekezera kudya Paska uyu ndi inu ndisanamve zowawa.\wj* \v 16 \wj Pakuti Ine ndikukuwuzani kuti sindidzadyanso Paska wina mpaka Paskayi itakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.”\wj* \p \v 17 Atanyamula chikho, Iye anayamika ndipo anati, \wj “Tengani ndipo patsiranani pakati panu.\wj* \v 18 \wj Pakuti ndikukuwuzani kuti, Ine sindidzamwanso zochokera ku chipatso cha mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utabwera.”\wj* \p \v 19 Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati, \wj “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”\wj* \p \v 20 \wj Chimodzimodzinso, utatha mgonero, anatenga chikho nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga, amene akhetsedwa chifukwa cha inu.\wj* \v 21 \wj Koma dzanja la amene akundipereka Ine lili pamodzi ndi langa pa chakudya pano.\wj* \v 22 \wj Mwana wa Munthu apita monga mmene zinalembedwera, koma tsoka kwa munthu amene amupereka Iye.”\wj* \v 23 Iwo anayamba kufunsana pakati pawo kuti ndi ndani wa iwo amene akanachita ichi. \s1 Mkangano Pakati pa Ophunzira \p \v 24 Komanso mkangano unabuka pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene amaganiziridwa kukhala wamkulu. \v 25 Yesu anawawuza kuti, \wj “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’\wj* \v 26 \wj Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira.\wj* \v 27 \wj Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani.\wj* \v 28 \wj Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero.\wj* \v 29 \wj Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine,\wj* \v 30 \wj kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.”\wj* \s1 Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana \p \v 31 \wj “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu.\wj* \v 32 \wj Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.”\wj* \p \v 33 Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.” \p \v 34 Yesu anayankha kuti, \wj “Ine ndikukuwuza Petro, tambala asanalire lero lino, udzandikana katatu kuti sukundidziwa Ine.”\wj* \p \v 35 Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, \wj “Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?”\wj* \p Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.” \p \v 36 Iye anawawuza kuti, \wj “Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula.\wj* \v 37 \wj Zalembedwa kuti, ‘Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi anthu ochimwa,’ ndipo Ine ndikuwuzani kuti izi ziyenera kukwaniritsidwa mwa Ine. Inde, zimene zinalembedwa za Ine, zikukwaniritsidwa.”\wj* \p \v 38 Ophunzira anati, “Taonani Ambuye, awa malupanga awiri.” \p Iye anayankha kuti, \wj “Amenewa akwanira.”\wj* \s1 Yesu Apemphera ku Phiri la Olivi \p \v 39 Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye. \v 40 Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti, \wj “Pempherani kuti musagwe mʼmayesero.”\wj* \v 41 Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti, \v 42 \wj “Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.”\wj* \v 43 Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa. \v 44 Ndipo mopsinjika mtima, anapemphera moona mtima, ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi akugwera pansi. \p \v 45 Iye atamaliza kupemphera, ndi kubwerera kwa ophunzira ake, anawapeza atagona atafowoka ndi chisoni. \v 46 Iye anafunsa kuti, \wj Nʼchifukwa chiyani mukugona? “Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero.”\wj* \s1 Amugwira Yesu \p \v 47 Pamene Iye ankayankhulabe, gulu la anthu linabwera, ndipo munthu wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo analitsogolera. Iye anamuyandikira Yesu kuti amupsompsone. \v 48 Koma Yesu anamufunsa kuti, \wj “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa Munthu ndi mpsopsono?”\wj* \p \v 49 Otsatira Yesu ataona zimene zimati zichitike, anati, “Ambuye, kodi timenyane ndi malupanga athu?” \v 50 Ndipo mmodzi wa iwo anatema wantchito wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake lamanja. \p \v 51 Koma Yesu anayankha kuti, \wj “Zisachitikenso zimenezi!”\wj* Ndipo Iye anakhudza khutu la munthuyo ndi kumuchiritsa. \p \v 52 Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti, \wj “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga?\wj* \v 53 \wj Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.”\wj* \s1 Petro Akana Yesu \p \v 54 Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali. \v 55 Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi. \v 56 Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.” \p \v 57 Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.” \p \v 58 Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, “Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo.” \p Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, ayi sindine.” \p \v 59 Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, “Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya.” \p \v 60 Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira. \v 61 Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, \wj “Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.”\wj* \v 62 Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri. \s1 Asilikali Amuchita Chipongwe Yesu \p \v 63 Anthu amene ankalonda Yesu anayamba kumuchita chipongwe ndi kumumenya. \v 64 Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?” \v 65 Ndipo iwo anamunena zachipongwe zambiri. \s1 Yesu Pamaso pa Pilato ndi Herode \p \v 66 Kutacha, bungwe la akuluakulu, pamodzi ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anakumana pamodzi, ndipo anamuyika Yesu patsogolo pawo. \v 67 Iwo anati, “Tiwuze, ngati ndiwe Khristu.” \p Yesu anayankha kuti, \wj “Ine nditakuwuzani simungandikhulupirire.\wj* \v 68 \wj Ine nditakufunsani inu, simungandiyankhe.\wj* \v 69 \wj Koma kuyambira tsopano, Mwana wa Munthu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvu.”\wj* \p \v 70 Onse anafunsa kuti, “Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” \p Iye anayankha kuti, \wj “Mwanena ndinu kuti Ndine.”\wj* \p \v 71 Pamenepo iwo anati, “Nanga tikufuniranjinso umboni wina? Ife tamva kuchokera pa milomo yake.” \c 23 \p \v 1 Kenaka gulu lonse la anthuwo linayimirira ndi kumutengera kwa Pilato. \v 2 Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.” \p \v 3 Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?” \p Yesu anayankha kuti, \wj “Mwatero ndinu.”\wj* \p \v 4 Kenaka Pilato anawawuza akulu a ansembe ndi gulu la anthu, “Ine sindikumupeza cholakwa munthuyu.” \p \v 5 Koma iwo analimbikirabe kuti, “Iyeyu amasokoneza anthu ku Yudeya konse ndi chiphunzitso chake, Iyeyu anayambira ku Galileya ndipo wayenda mtunda wonse mpaka kuno.” \p \v 6 Pakumva zimenezi, Pilato anafunsa ngati munthuyo ndi Mgalileya. \v 7 Iye atamva kuti Yesu anali pansi pa ulamuliro wa Herode, anamutumiza kwa Herodeyo, amene pa nthawi imeneyo analinso mu Yerusalemu. \p \v 8 Herode ataona Yesu, anakondwa kwambiri, chifukwa kwa nthawi yayitali, ankafunitsitsa atamuona. Kuchokera pa zimene anamva za Iye, anayembekezera kuti achita zodabwitsa. \v 9 Iye anamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sanayankhe. \v 10 Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anayimirira pamenepo ndi kumuneneza kwambiri. \v 11 Pamenepo Herode ndi asilikali ake anamuseka ndi kumunyoza Iye. Atamuveka mkanjo wonyezimira, anamutumizanso kwa Pilato. \v 12 Tsiku limenelo, Herode ndi Pilato anakhala abwenzi. Zisanachitike izi anali adani. \p \v 13 Pilato anasonkhanitsa akulu a ansembe, oweruza ndi anthu, \v 14 ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu. \v 15 Herodenso sanapeze chifukwa pakuti wamutumizanso kwa ife monga mmene mukuoneramu. Iyeyu sanachite chinthu chakuti aphedwe. \v 16 Nʼchifukwa chake, ine ndingomulanga, nʼkumumasula.” \v 17 (Pa nthawi yachikondwerero cha Paska iye ankayenera kumasula munthu mmodzi). \p \v 18 Onse pamodzi anafuwula kuti, “Muchotseni munthuyu! Timasulireni Baraba!” \v 19 (Baraba anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe mu mzinda ndi kupha). \p \v 20 Pofuna kumumasula Yesu, Pilato anawadandaulira iwo. \v 21 Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” \p \v 22 Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.” \p \v 23 Koma ndi mawu ofuwulitsa, analimbikirabe kuti Iye apachikidwe, ndipo kufuwulako kunapitirira. \v 24 Choncho Pilato anatsimikiza kuchita zofuna zawozo. \v 25 Iye anawamasulira munthu amene anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe ndi kupha, amene ankamufunayo, ndipo anawapatsa Yesu mwakufuna kwawo. \s1 Kupachikidwa kwa Yesu \p \v 26 Ndipo pamene ankapita naye, anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera ku munda, namusenzetsa mtanda namuyendetsa pambuyo pa Yesu. \v 27 Gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye, kuphatikiza amayi amene ankabuma ndi kumulirira. \v 28 Yesu anatembenuka nati kwa iwo, \wj “Ana aakazi a Yerusalemu, musandilirire Ine; dzililireni nokha ndi ana anu.\wj* \v 29 \wj Pakuti nthawi idzabwera imene inu mudzati, ‘Ndi odala amayi osabereka, mimba zimene sizinabereke ndi mawere amene sanayamwitse!’\wj* \v 30 \wj Kenaka,\wj* \q1 \wj “adzawuza mapiri kuti tigwereni ife;\wj* \q2 \wj zitunda kuti tiphimbeni ife.\wj* \m \v 31 \wj Chifukwa ngati anthu akuchita izi pa mtengo wauwisi, chidzachitike nʼchiyani ndi wowuma?”\wj* \p \v 32 Amuna ena awiri, onsewo achifwamba, anatengedwanso pamodzi ndi Yesu kukaphedwa. \v 33 Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere. \v 34 Yesu anati, \wj “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.”\wj* Ndipo anagawana malaya ake mochita maere. \p \v 35 Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.” \p \v 36 Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa, \v 37 ndipo anati, “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” \p \v 38 Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: \sc uyu ndi mfumu ya ayuda\sc*. \p \v 39 Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, “Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!” \p \v 40 Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi? \v 41 Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu.” \p \v 42 Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.” \p \v 43 Yesu anayankha kuti, \wj “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”\wj* \s1 Imfa ya Yesu \p \v 44 Linali tsopano pafupi ora lachisanu ndi chimodzi, ndipo mdima unagwa pa dziko lonse mpaka ora lachisanu ndi chinayi, \v 45 pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati. \v 46 Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, \wj “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.”\wj* Atanena zimenezi, anamwalira. \p \v 47 Kenturiyo, ataona zimene zinachitikazi, analemekeza Mulungu ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali munthu wolungama.” \v 48 Anthu onse amene anasonkhana kudzaonerera izi, ataona zinachitikazo, anadziguguda pachifuwa ndipo anachoka. \v 49 Koma onse amene anamudziwa Iye, kuphatikiza amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anayimirira akuona zinthu izi. \s1 Yesu Ayikidwa Mʼmanda \p \v 50 Ndipo taonani panali munthu wina wotchedwa Yosefe, mmodzi wa gulu loweruza, munthu wabwino ndi wolungama. \v 51 Iye sanavomereze zimene anzake abwalo anagwirizana ndi kuchita. Iye ankachokera ku mudzi wa Arimateyu wa ku Yudeya ndipo ankayembekezera ufumu wa Mulungu. \v 52 Atapita kwa Pilato, iye anakapempha mtembo wa Yesu. \v 53 Ndipo anawutsitsa, nawukulunga nsalu yabafuta nawuyika mʼmanda wosemedwa mʼmwala, amene panalibe wina amene anayikidwamo. \v 54 Linali tsiku lokonzekera ndipo Sabata linatsala pangʼono kuyamba. \p \v 55 Amayi amene anabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsata Yosefe ndipo anaona manda ndi momwe mtembo wake anawuyikira. \v 56 Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo. \c 24 \s1 Yesu Auka kwa Akufa \p \v 1 Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda. \v 2 Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika \v 3 ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. \v 4 Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo. \v 5 Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa? \v 6 Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya: \v 7 \wj ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ ”\wj* \v 8 Ndipo anakumbukira mawu ake. \p \v 9 Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse. \v 10 Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi. \v 11 Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru. \v 12 Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo. \s1 Zochitika pa Njira ya ku Emau \p \v 13 Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu. \v 14 Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo. \v 15 Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi; \v 16 koma iwo sanamuzindikire. \p \v 17 Iye anawafunsa kuti, \wj “Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?”\wj* \p Iwo anayima ndi nkhope zakugwa. \v 18 Mmodzi wa iwo wotchedwa Kaliyopa anamufunsa kuti, “Kodi ndiwe wekha wokhala mu Yerusalemu amene sukudziwa zinthu zimene zachitika mʼmasiku awa?” \p \v 19 Iye anafunsa kuti, \wj “Zinthu zotani?”\wj* \p Iwo anayankha nati, “Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse. \v 20 Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye; \v 21 koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi. \v 22 Kuwonjezanso apo, ena mwa amayi athu atidabwitsa ife. Iwo anapita ku manda mmamawa \v 23 koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo. \v 24 Kenaka ena mwa anzathu anapita ku manda ndipo anakapeza monga momwe amayiwo ananenera, koma Iye sanamuone.” \p \v 25 Iye anawawuza kuti, \wj “Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena!\wj* \v 26 \wj Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?”\wj* \v 27 Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini. \p \v 28 Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira. \v 29 Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, “Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa.” Ndipo Iye anapita kukakhala nawo. \p \v 30 Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira. \v 31 Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo. \v 32 Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?” \p \v 33 Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi \v 34 ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.” \v 35 Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi. \s1 Yesu Aonekera kwa Ophunzira \p \v 36 Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati, \wj “Mukhale ndi mtendere.”\wj* \p \v 37 Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa. \v 38 Iye anawafunsa kuti, \wj “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu?\wj* \v 39 \wj Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.”\wj* \p \v 40 Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake. \v 41 Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, \wj “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?”\wj* \v 42 Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika. \v 43 Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona. \p \v 44 Iye anawawuza kuti, \wj “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.”\wj* \p \v 45 Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba. \v 46 Iye anawawuza kuti, \wj “Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu.\wj* \v 47 \wj Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu.\wj* \v 48 \wj Inu ndinu mboni za zimenezi.\wj* \v 49 \wj Ine ndidzakutumizirani chimene Atate anga analonjeza. Koma khalani mu mzinda muno mpaka mutavekedwa mphamvu yochokera kumwamba.”\wj* \s1 Kupita Kumwamba \p \v 50 Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa. \v 51 Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba. \v 52 Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. \v 53 Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.