\id HAB - Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 \ide UTF-8 \h HABAKUKU \toc1 Habakuku \toc2 Habakuku \toc3 Hab \mt1 Habakuku \c 1 \p \v 1 Uthenga umene mneneri Habakuku analandira mʼmasomphenya. \s1 Dandawulo la Habakuku \q1 \v 2 Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani, \q2 koma wosayankha? \q1 Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!” \q2 koma wosatipulumutsa? \q1 \v 3 Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa? \q2 Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa? \q1 Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa; \q2 pali ndewu ndi kukangana kwambiri. \q1 \v 4 Kotero malamulo anu atha mphamvu, \q2 ndipo chilungamo sichikugwira ntchito. \q1 Anthu oyipa aposa olungama, \q2 kotero apotoza chilungamo. \s1 Yankho la Yehova \q1 \v 5 “Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu, ndipo penyetsetsani, \q2 ndipo muthedwe nazo nzeru. \q1 Pakuti ndidzachitadi zinthu pa nthawi yanu \q2 zimene inu simudzazikhulupirira, \q2 ngakhale wina atakufotokozerani. \q1 \v 6 Pakuti taonani, Ine ndikuwutsa Ababuloni, \q2 anthu ankhanza ndiponso amphamvu, \q1 amene amapita pa dziko lonse lapansi \q2 kukalanda malo amene si awo. \q1 \v 7 Iwowa ndi anthu ochititsa mantha, ndipo ndi owopsa; \q2 amadzipangira okha malamulo \q2 ndi kudzipezera okha ulemu. \q1 \v 8 Akavalo awo ndi aliwiro kwambiri kupambana akambuku \q2 ndi owopsa kupambana mimbulu yolusa nthawi ya madzulo. \q1 Okwerapo awo akuthamanga molunjika; \q2 a pa akavalo awo ndi ochokera kutali, \q1 akuwuluka ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama; \q2 \v 9 onse akubwera atakonzekera zachiwawa. \q1 Gulu la ankhondo likubwera ngati mphepo ya mʼchipululu \q2 ndi kugwira akapolo ochuluka ngati mchenga. \q1 \v 10 Akunyoza mafumu \q2 ndiponso kuchitira chipongwe olamulira. \q1 Akupeputsa mizinda yonse yotetezedwa; \q2 akumanga mitumbira ndi kulanda mizindayo. \q1 \v 11 Kenaka amasesa mofulumira ngati mphepo nʼkumangopitirirabe, \q2 anthu ochimwa, amene mphamvu zawo ndiye mulungu wawo.” \s1 Dandawulo Lachiwiri la Habakuku \q1 \v 12 Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire? \q2 Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa. \q1 Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo; \q2 Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange. \q1 \v 13 Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa; \q2 Inu simulekerera cholakwa. \q1 Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa? \q2 Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa \q2 akuwononga anthu olungama kupambana iwowo? \q1 \v 14 Mwasandutsa anthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja, \q2 ngati zolengedwa zamʼnyanja zimene zilibe wolamulira. \q1 \v 15 Mdani wawo woyipa amakoka anthu onse ndi mbedza, \q2 amawakola mu ukonde wake, \q1 amawasonkhanitsa mu khoka lake; \q2 kotero iyeyo amakondwa ndi kusangalala. \q1 \v 16 Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake \q2 ndiponso kufukizira lubani khoka lake, \q1 popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba \q2 ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri. \q1 \v 17 Kodi iye azipitirabe kugwiritsa ntchito makoka akewo, \q2 kuwononga mitundu ya anthu mopanda chifundo? \c 2 \q1 \v 1 Ndidzakhala pa malo anga aulonda, \q2 ndi kuyima pa mitumbira ya nkhondo; \q1 ndidzadikira kuti ndimve zimene Iye adzandiwuze, \q2 ndi yankho limene ndidzapatsidwe pa madandawulo anga. \s1 Yankho la Yehova \p \v 2 Tsono Yehova anandiyankha, nati: \q1 “Lemba masomphenyawa \q2 ndipo uwalembe mooneka bwino pa mapale \q2 kuti wowerenga awawerenge mosavuta. \q1 \v 3 Pakuti masomphenyawa akudikira nthawi yake; \q2 masomphenyawa akunena zamʼtsogolo \q2 ndipo sizidzalephera kuchitika. \q1 Ngakhale achedwe kukwaniritsidwa, uwayembekezere; \q2 zidzachitika ndithu ndipo sadzachedwa. \b \q1 \v 4 “Taona, mdani wadzitukumula; \q2 zokhumba zake sizowongoka, \q2 koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro. \q1 \v 5 Ndithu, wasokonezeka ndi vinyo; \q2 ndi wodzitama ndiponso wosakhazikika. \q1 Pakuti ngodzikonda ngati manda, \q2 ngosakhutitsidwa ngati imfa, \q1 wadzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu \q2 ndipo wagwira ukapolo anthu a mitundu yonse. \p \v 6 “Kodi onse ogwidwawo sadzamunyoza ndi kumunyogodola ponena kuti, \q1 “Tsoka kwa amene amadzikundikira katundu amene si wake \q2 ndipo amadzilemeretsa ndi chuma cholanda! \q2 Kodi izi zidzachitika mpaka liti? \q1 \v 7 Kodi angongole ako sadzakuwukira mwadzidzidzi? \q2 Kodi sadzadzuka ndi kukuchititsa mantha? \q2 Pamenepo iwe udzalandidwa kalikonse. \q1 \v 8 Pakuti unafunkha mitundu yambiri ya anthu, \q2 mitundu ina imene inatsala idzakufunkha iweyo. \q1 Pakuti wakhetsa magazi a anthu; \q2 wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo. \b \q1 \v 9 “Tsoka kwa amene amalemera ndi chuma chochipeza mwachinyengo, \q2 kukweza malo ake okhalapo, \q2 kuthawa mavuto! \q1 \v 10 Wakonzekera kuwononga mitundu yambiri ya anthu, \q2 kuchititsa manyazi nyumba yako yomwe ndi kuwononga moyo wako. \q1 \v 11 Mwala pa khoma udzafuwula, \q2 ndipo mitanda ya matabwa idzavomereza zimenezi. \b \q1 \v 12 “Tsoka kwa amene amanga mzinda pokhetsa magazi \q2 ndi kukhazikitsa mzinda pochita zoyipa! \q1 \v 13 Kodi Yehova Wamphamvuzonse sanatsimikize \q2 kuti ntchito za anthu zili ngati nkhuni pa moto, \q2 ndi kuti mitundu ya anthu imadzitopetsa popanda phindu? \q1 \v 14 Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, \q2 monga momwe madzi amadzazira nyanja. \b \q1 \v 15 “Tsoka kwa amene amamwetsa anzake zakumwa zoledzeretsa, \q2 kutsanula mʼbotolo mpaka ataledzera, \q2 kuti aone umaliseche wawo. \q1 \v 16 Udzachita manyazi mʼmalo mokhala ndi ulemerero. \q2 Tsopano ino ndi nthawi yako! Imwa mpaka umaliseche wako uwonekere! \q1 Chikho chochokera mʼdzanja lamanja la Yehova chikubwera kwa iwe, \q2 ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako. \q1 \v 17 Udzathedwa nzeru ndi chiwawa chimene unachita ku Lebanoni, \q2 ndiponso udzachita mantha ndi nyama zimene unaziwononga. \q1 Pakuti wakhetsa magazi a anthu; \q2 wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo. \b \q1 \v 18 “Kodi fano lili ndi phindu lanji, poti analisema ndi munthu, \q2 kapena chifanizo chimene chimaphunzitsa mabodza? \q1 Pakuti munthu amene walipanga amakhulupirira ntchito ya manja ake; \q2 amapanga mafano amene samatha kuyankhula. \q1 \v 19 Tsoka kwa amene amawuza mtengo kuti, ‘Khala wamoyo!’ \q2 Kapena mwala wopanda moyo kuti, ‘Dzuka!’ \q1 Kodi zimenezi zingathe kulangiza? \q2 Ndi zokutidwa ndi golide ndi siliva; \q2 mʼkati mwake mulibe mpweya. \q1 \v 20 Koma Yehova ali mʼNyumba yake yopatulika; \q2 dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.” \c 3 \s1 Pemphero la Habakuku \p \v 1 Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti. \q1 \v 2 Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu; \q2 Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa. \q1 Muzichitenso masiku athu ano, \q2 masiku athu ano zidziwike; \q2 mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo. \b \q1 \v 3 Mulungu anabwera kuchokera ku Temani, \q2 Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani. \q4 Sela \q1 Ulemerero wake unaphimba mlengalenga \q2 ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake. \q1 \v 4 Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa; \q2 kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake, \q2 mʼmene anabisamo mphamvu zake. \q1 \v 5 Patsogolo pake pankagwa mliri; \q2 nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake. \q1 \v 6 Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi; \q2 anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera. \q1 Mapiri okhazikika anagumuka \q2 ndipo zitunda zakalekale zinatitimira. \q2 Njira zake ndi zachikhalire. \q1 \v 7 Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto, \q2 mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu. \b \q1 \v 8 Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje? \q2 Kodi munakalipira timitsinje? \q1 Kodi munapsera mtima nyanja \q2 pamene munakwera pa akavalo anu \q2 ndiponso magaleta anu achipulumutso? \q1 \v 9 Munasolola uta wanu mʼchimake, \q2 munayitanitsa mivi yambiri. \q4 Sela \q1 Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje; \q2 \v 10 mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka. \q1 Madzi amphamvu anasefukira; \q2 nyanja yozama inakokoma \q2 ndipo mafunde ake anakwera kwambiri. \b \q1 \v 11 Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga, \q2 pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo, \q2 pa kunyezimira kwa mkondo wanu. \q1 \v 12 Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali, \q2 ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo. \q1 \v 13 Munapita kukalanditsa anthu anu, \q2 kukapulumutsa wodzozedwa wanu. \q1 Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa, \q2 munawononga anthu ake onse. \q4 Sela \q1 \v 14 Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wake \q2 pamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa, \q1 ankasangalala ngati kuti akudzawononga \q2 osauka amene akubisala. \q1 \v 15 Munapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu, \q2 kuvundula madzi amphamvu. \b \q1 \v 16 Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri, \q2 milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo; \q1 mafupa anga anaguluka, \q2 ndipo mawondo anga anawombana. \q1 Komabe ndikuyembekezera mofatsa, \q2 tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo. \q1 \v 17 Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa, \q2 ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa. \q1 Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso, \q2 ndipo mʼminda musatuluke kanthu. \q1 Ngakhale nkhosa \q2 ndi ngʼombe zithe mʼkhola, \q1 \v 18 komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova, \q2 ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga. \b \q1 \v 19 Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga; \q2 amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi, \q2 amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri. \b \q1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.